Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/96 tsamba 5
  • Kukonzekera—Mfungulo ya Chipambano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonzekera—Mfungulo ya Chipambano
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukonzekera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Kukonzekereratu Kumadzetsa Chimwemwe
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Khalani “Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Ngati Umagwira Mtima, Ugwiritsireni Ntchito!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 3/96 tsamba 5

Kukonzekera—Mfungulo ya Chipambano

1 Kukonzekera utumiki pasadakhale kudzathandiza munthu kulaka kukayikira kulikonse kumene angakhale nako ponena za kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Pamene mufika pamakomo, mudzadziŵa zimene mukufuna kunena kwa eni nyumba. Simudzachita mantha ndi zovuta zimene mungakumane nazo. Mutabwerera kwanu kuchokera ku utumiki, mudzakhala wolimbikitsidwa, mukumadziŵa kuti mwayesayesa bwino mu utumiki wakumunda. Inde, kukonzekera kosamalitsa ndiko mfungulo yonolera maluso athu akulalikira ndi kuphunzitsa.

2 Paulo anagogomezera kukonzekera mwa kutilimbikitsa ‘kudziveka mapazi ndi makonzedwe a uthenga wabwino wa mtendere.’ (Aef. 6:15) Zimenezi zimaphatikizapo kukonzekeretsa maganizo ndi mtima wathu ndipo kupeza chidaliro ndi mzimu wa kufunitsitsa. Pamene tikonzekera kuuza ena choonadi, ntchito yathu idzafupidwa ndi zipatso za Ufumu, zikumatisangalatsa.—Mac. 20:35.

3 Mmene Tingakonzekerere Ntchito Yolalikira: Tiyenera kusankha ulaliki umene tilingalira kuti ngwosavuta kwa ife, mwinamwake pakati pa aja osonyezedwa m’buku la Kukambitsirana kapena aja opezeka patsamba lomalizira la Utumiki Wathu Waufumu. Sinkhasinkhani mosamala pa lemba limene mukufuna kukagwiritsira ntchito, mukumasankha mawu kapena chiganizo chimene mudzagogomezera kuti musonyeze mfundo yanu. Palibe chifukwa choloŵezera ulaliki pamtima; m’malo mwake, ndi bwino koposa kusunga lingaliro lake, kulinena m’mawu anuanu, ndi kulifotokoza m’njira imene mulingalira kuti idzakopa womvetsera wanu.

4 Pendani chofalitsidwa chimene mwalinganiza kukagaŵira, ndipo sankhani mfundo zina zokondweretsa zokambitsirana. Sankhani kanthu kena kamene mukuganiza kuti kadzakhala kokondweretsa anthu a m’gawo lanu. Sinkhasinkhani za mmene mungasinthire ulaliki wanu kwa eni nyumba osiyanasiyana—kwa mwamuna, mkazi, nkhalamba, kapena wachichepere.

5 Kodi mwayesapo kukhala ndi nthaŵi zakuyeseza? Sonkhanani ndi banja lanu kapena ofalitsa ena kuti mukambitsirane za maulaliki amene angakhale ogwira mtima, ndiyeno kuwayeseza momveketsa mawu kotero kuti aloŵe bwino m’maganizo mwa onse. Yesani kuyerekezera mikhalidwe yeniyeni ndi zitsutso zimene mungapeze m’gawolo. Kuyeseza kotero kudzawongolera kulankhula kwanu mwamyaa, kudzawonjezera kugwira mtima kwanu polalikira, ndi kukulitsa chidaliro chanu.

6 Ndiponso kuwonjezera pa kukonzekera ndi kuyeseza kwanu ulaliki, muyeneranso kudzifunsa kuti, ‘Kodi zovala zimene ndikufuna kuvala nzoyenerera utumiki? Kodi ndili ndi zimene ndifunikira m’chikwama changa, kuphatikizapo mabuku amene ndikufuna kukagwiritsira ntchito? Kodi nzabwino? Kodi ndili ndi buku langa la Kukambitsirana, matrakiti, cholembapo cha kunyumba ndi nyumba, ndi pensulo?’ Kulinganiza kwanzeru kwapasadakhale kudzakuthandizani kukhala ndi tsiku lopindulitsa mu utumiki.

7 Titachita zonse zimene tingathe kudzikonzekeretsa, tiyenera kupempherera mzimu wa Yehova kuti utithandize kukhala achipambano. (1 Yoh. 5:14, 15) Kuika mtima pa kukonzekera kuzadzetsa chimwemwe chachikulu pantchito yathu, pamene ‘tikwaniritsa utumiki wathu.’—2 Tim. 4:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena