Zikumbutso za Chikumbutso
Zotsatirazi ndi mfundo zimene zifunikira chisamaliro Chikumbutso chisanachitike pa Lachiŵiri, April 2:
◼ Aliyense, kuphatikizapo mlankhuli, ayenera kudziŵitsidwa nthaŵi ndi malo enieni a chochitikacho.
◼ Muyenera kupeza ndi kusungiratu mtundu woyenera wa mkate ndi vinyo.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.
◼ Thebulo loyenera, nsalu ya pathebulo, mbale, ndi matambula ziyenera kukaikidwa m’holo pamalo pake pakali nthaŵi.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena a msonkhanowo ayenera kuyeretsedwa bwinobwino pakali nthaŵi.
◼ Akalinde ndi operekera zizindikiro ayenera kusankhidwa ndi kulangizidwa pasadakhale ponena za njira yoyenera ndi mathayo awo.
◼ Muyenera kupanga makonzedwe a kukaperekera zizindikiro kwa wodzozedwa aliyense amene ali wodwala ndi wosakhoza kupezekapo.
◼ Pamene chochitikacho chidzachitidwa nthaŵi zoposa imodzi m’Nyumba ya Ufumu imodzimodziyo, mipingo iyenera kugwirizana bwino kuti ipeŵe kuunjikana kwa anthu m’khonde, modzera, m’likole, ndi poimikira galimoto.
◼ Akalinde okhala ndi thayo la kuŵerenga anthu pamsonkhano umenewu ndi ina ayenera kusamala kuti asapereke chiŵerengero chopambanitsa. Anthu ochotsedwa amaloledwa kufika pa Chikumbutso ndipo amaŵerengedwa. Komabe, sitimaŵerenga wochotsedwa aliyense kapena aliyense amene ali wosabatizidwa kukhala wolandira zizindikiro ngati adya.