Zokumbutsa za Chikumbutso
Chikumbutso chidzakhalako Loŵeruka, pa April 11. Akulu asamalire zotsatirazi:
◼ Poika nthaŵi ya msonkhanowo, onani kuti zizindikiro zisadzayambe kuperekedwa mpaka dzuŵa litaloŵa.
◼ Aliyense, kuphatikizapo wokamba nkhani, ayenera kuuzidwa nthaŵi yeniyeni ndi malo ake.
◼ Mudzapezeretu mkate ndi vinyo woyenera nkukhala nazo chire.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985 (Chingelezi), tsamba 19.
◼ Mbale, magalasi, ndi thebulo yabwino ndi nsalu yapathebulo mudzabwere nazo ku holo nkuziyala pasadakhale.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena osonkhanira ayenera kudzayeretsedwa pasadakhale.
◼ Akalinde ndi otumikira ayenera kusankhidwa ndi kulangizidwa pasadakhale za mmene adzayendetsera zinthu ndi ntchito zawo.
◼ Mupange makonzedwe okaperekera zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense wofooka amene sangathe kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzimodziyo, mipingoyo idzagwirizane bwino za nthaŵi, kotero kuti pasadzakhale kupanikizana kwa anthu pakhonde, pakhomo, koimika magalimoto.