Zikumbutso za pa Chikumbutso
Phwando la Chikumbutso lidzakhalako pa Sande, March 23. Akulu ayenera kusamalira zinthu zotsatirapozi:
◼ Poika nthaŵi ya msonkhanowu, tsimikizani kuti zizindikiro sizidzaperekedwa mpaka dzuŵa litaloŵa.
◼ Aliyense, kuphatikizapo wokamba nkhani, ayenera kuuzidwa za nthaŵi yeniyeni ndi malo enieni a phwandolo.
◼ Mtundu woyenera wa mkate ndi vinyo ziyenera kukhalapo zili zokonzeka.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.
◼ Mbale, matambula, ndi thebulo labwino ndi nsalu ya pathebulo muyenera kuzibweretsa ku holo ndi kuziikiratu pamalo ake pasadakhale.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena osonkhaniramo ayenera kuyeretsedwa mosamalitsa pasadakhale.
◼ Akalinde ndi operekera zizindikiro ayenera kusankhidwa ndi kupatsidwa malangizo pasadakhale ponena za kachitidwe koyenera ndi mathayo awo.
◼ Muyenera kupanga makonzedwe a kupereka zizindikiro kwa odzozedwa alionse a thanzi lofooka ndipo osakhoza kupezekapo.
◼ Pamene mipingo yambiri idzagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzimodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino kuti apeŵe kupanikizana kosayenera m’njira yapakati, pakhomo, tinjira ta onse, ndi poimika magalimoto.