Zokumbutsa za Chikumbutso
Chikumbutso chaka chino chidzachitika Lachinayi, pa April 1. Akulu ayenera kusamalira zinthu izi:
◼ Poika nthaŵi ya msonkhano, onetsetsani kuti zizindikiro zisayendetsedwe dzuŵa lisanaloŵe.
◼ Aliyense, kuphatikizapo wokamba nkhani, ayenera kudziŵitsidwa nthaŵi yeniyeni ndi malo a chochitikachi.
◼ Muyenera kupezeratu mkate ndi vinyo woyenera komanso zikhale zokonzeka.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.
◼ Mbale, matambula, tebulo yabwino ndi nsalu zabwino zoyala patebulo ziyenera kubweretsedwa msanga ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse osonkhanapo ayenera kuyeretsedwa bwino pasadakhale.
◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi otumikira ndipo alangizirenitu mmene adzayendetsera zinthu ndi ntchito yawo.
◼ Mupange makonzedwe okaperekera zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense wathanzi lofooka amene sangathe kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kotero kuti pasadzakhale kupanikizana kwa anthu pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto.