Zofunika Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso
Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lamlungu, pa April 8. Akulu asamalire zinthu izi:
◼ Poika nthaŵi ya msonkhano, onetsetsani kuti zizindikiro zisayendetsedwe dzuŵa lisanaloŵe.
◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthaŵi yeniyeni ndi kumene kudzachitikire mwambowu.
◼ Muyenera kupezeratu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.
◼ Mbale, makapu, tebulo labwino ndi nsalu za patebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthaŵi yabwino.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayenera kuyeretsedweratu bwinobwino.
◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi operekera zizindikiro ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu.
◼ Konzani kukapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense wodwala amene sangathe kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kotero kuti pasadzakhale kupanikizana kwa anthu pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto.