Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/02 tsamba 7
  • Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Zokumbutsa za Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Zofunika Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Zikumbutso za pa Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 3/02 tsamba 7

Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso

Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lachinayi, March 28. Akulu asamalire zinthu izi:

◼ Poika nthaŵi ya msonkhano, onetsetsani kuti musapereke zizindikiro dzuŵa lisanaloŵe.

◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthaŵi yeniyeni ndi kumene kudzachitikire mwambowu.

◼ Mupezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.

◼ Mbale, matambula, tebulo labwino ndi nsalu za patebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthaŵi yabwino.

◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayeretsedweretu bwinobwino.

◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi operekera zizindikiro ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti afunika adzavale zovala zopatsa ulemu ndiponso kudzikonza bwino.

◼ Konzani kukapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo satha kupezekapo.

◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena