Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/97 tsamba 8
  • Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Gaŵirani Buku la Chimwemwe cha Banja kwa Anthu a Misinkhu Yonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Kuuzako Ena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 3/97 tsamba 8

Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa

1 “Umbombo ndi wabwino,” wazachuma wina anauza kalasi lina lomaliza maphunziro pakoleji, nawonjezera kuti: “Ungakhale waumbombo ndi kudzisungirabe ulemu wako.” Ndimo mmenedi dziko limachirikizira dyera monga njira yotsimikizira mtsogolo mwa munthu. Mosiyana kotheratu ndi zimenezo, Yesu anaphunzitsa kuti Mkristu ayenera kuti “adzikane yekha, . . . pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake?” (Mat. 16:24-26) Kuti munthu amange mtsogolo mokhalitsa, ayenera kuzika moyo wake wonse pa kuchita chifuniro cha Mulungu—chonulirapo chofunika koposa m’mabanja lerolino. (Sal. 143:10; 1 Tim. 4:8) Uthengawo waperekedwa m’mutu womaliza wa buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Chofalitsa chatsopano chimenechi chimathandiza anthu kuona chimene chilidi chofunika m’moyo ndi zimene angachite kuti apindulitse mabanja awo. Pamene tipitiriza kulalikira uthenga wabwino kulikonse, kodi tinganene chiyani chimene chidzalimbikitsa awo amene tikumana nawo kuŵerenga buku la Chimwemwe cha Banja? Nazi njira zina:

2 Pakhomo ndi m’khwalala momwe, mungayese kugwiritsira ntchito trakiti la “Sangalalani ndi Moyo wa Banja” poyambitsa makambitsirano. Mungafunse kuti:

◼ “Pokhala ndi nkhaŵa zonse zimene moyo wamakono umadzetsa pa ife, kodi mukuganiza kuti nkotheka kukhala ndi moyo wa banja wosangalatsadi? [Yembekezerani yankho.] Trakitili limatitsimikiza kuti nkotheka. Kodi mungakonde kuliŵerenga?” Ngati alilandira, mungapitirize mwa kunena kuti: “Popeza mwaikonda nkhaniyi, mwina mungasangalalenso ndi buku ili limene limapereka uphungu watsatanetsatane ponena za mmene mungapezere mtendere m’banja.” Sonyezani mpambo wa zamkati m’buku la Chimwemwe cha Banja. Sonyezani mitu ingapo yokopa. Tsegulani patsamba 10, ndipo yambani kuŵerenga chiganizo chomaliza cha ndime 17 mpaka kumapeto a ndime 18. Gaŵirani bukulo pachopereka chamasiku onse. Fotokozani kuti muli ndi zambiri zogaŵana nawo, funsani pamene mungadzalankhulenso nawo.

3 Mungapitirize makambitsirano anu oyamba a moyo wa banja mwa kunena kuti:

◼ “Ndikufuna kukusonyezani kenakake m’buku limene munatenga kamene ndiganiza kuti mudzakakonda. Mutu womaliza ukunena kwambiri za chinsinsi chenicheni cha chimwemwe cha banja. [Ŵerengani ndime 2 patsamba 183.] Mwaonatu kuti kugwira ntchito pamodzi kuti muchite chifuniro cha Mulungu ndiko kiyi yake. Timalimbikitsa mabanja kuti aziphunzira Baibulo pamodzi kuti adziŵe chifuniro cha Mulungu ndi mmene angachichitire m’mabanja. Tikupereka kosi yaulere yophunzitsa Baibulo imene imatha miyezi yochepa chabe. Ngati mudzandilola, ndidzakusonyezani mmene imachitikira.” Bwereraniko ndi brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena buku la Chidziŵitso, lililonse limene lingakhale loyenera kwambiri.

4 Polankhula ndi anzanu a m’kalasi kusukulu kapena kwa achinyamata m’gawo, mwina angakuyankheni funso ili:

◼ “Kodi nkofunika motani kuti makolo ndi ana awo azilankhulana momasuka? [Yembekezerani yankho.] Taonani zimene bukuli lolangiza za moyo wa banja likunena pankhani ya ‘Kulankhulana Koona Mtima ndi Komasuka.’ [Ŵerengani ndime 4 yonse ndi chiganizo choyamba cha ndime 5 patsamba 65 m’buku la Chimwemwe cha Banja.] Ndime zotsatira zimapereka njira zogwira ntchito zimene mungawongolere kulankhulana m’banja. Bukuli lili ndi mutu wakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Ngati mukufuna kuliŵerenga, kopeli lingakhale lanu pachopereka cha K12.00 basi.” Fotokozani kuti mudzabweranso nthaŵi ina kudzamva ndemanga zake pazimene waŵerenga.

5 Mungapitirize makambitsirano anu oyamba ndi wachinyamata pa kulankhulana kwa makolo ndi ana mwa kunena izi:

◼ “Ndinayamikira chidwi chimene munasonyeza pa kufunika kwa kulankhulana bwino m’banja lanu. Kodi munganene kuti nkhani yofunika koposa imene makolo ndi ana angakambitsirane ndi yotani?” Yembekezerani yankho. Kenako tsegulani patsamba 68 m’buku la Chimwemwe cha Banja, ndipo ŵerengani yankho limene likupezeka m’theka loyamba la ndime 11. “Kukhala ndi phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu ndiko njira yabwino koposa yopezera chidziŵitso cha Mulungu.” Perekani brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Longosolani kuti maphunziro ake 16 amapereka mfundo zoyambirira za uthenga wa Baibulo. Ŵerengani mawu oyamba patsamba 2. Gaŵirani broshalo pachopereka chamasiku onse, kenako pemphani kuyamba phunziro mwa kukambitsirana phunziro loyamba.

6 Ngati mwakumana ndi kholo m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kapena m’paki kapena pabwalo lamaseŵero, mungadzutse chidwi mwa kunena kuti:

◼ “Ndikhulupirira mukuvomereza kuti kulera ana lerolino ndi vuto lalikulu. Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chingatetezere banja lanu ku zisonkhezero zoipa? [Yembekezerani yankho.] Nawu uphungu wina wabwino kwambiri umene wandikondweretsa.” Longosolani fanizo la m’ndime 1, ndipo ŵerengani ndime 2 patsamba 90 m’buku la Chimwemwe cha Banja. Fotokozani mmene limaperekera chitsogozo chabwino chimene chimagwiradi ntchito kutetezera mabanja ku zisonkhezero zowononga. Gaŵirani bukulo pachopereka chamasiku onse, ndipo dziperekeni kuyankha mafunso alionse amene angabuke.

7 Paulendo wanu wachiŵiri kwa kholo limene linalandira buku la “Chimwemwe cha Banja,” mungapitirize makambitsiranowo motere:

◼ “Paja tinakumana poyamba, ndinatha kuona kuti mumasamaladi za ana anu ndi kuti mukufuna kuchita zonse zimene mungathe kuwatetezera ku zisonkhezero zoipa. M’buku limene munaombola muli mfundo ina ndipo mwina simunaiŵerengebe, koma ndi yofunika kwambiri imene muyenera kuiona. [Ŵerengani ndime 19 patsamba 59.] Kukulitsa unansi ndi Mulungu kumafuna kuti timdziŵe kudzera m’Mawu ake olembedwa, Baibulo. Kodi mungakonde kuti ndikusonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo monga banja?”

8 Aphungu akudziko satha kusonyeza mabanja njira yopezera chimwemwe koma ndithudi amangowasiya atagwira mwala. Tiyeni tiligaŵire kwambiri buku la Chimwemwe cha Banja kotero kuti anthu kulikonse athandizidwe ndi Mawu a Mulungu kumanga mtsogolo mokhalitsa.—1 Tim. 6:19.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena