Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” wa Mboni za Yehova
1 “Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.” (Sal. 84:10) Pamene wamasalmo analambira pakachisi wa Yehova, anali kumva kukhalapo kwa Mulungu wamphamvuyonse. Pamene mtunduwo unasonkhana pamadyerero apachaka ndipo alambiri oona atadzaza m’Yerusalemu, Aisrayeli anasangalala ndi mayanjano mmene anasonkhana m’bwalo la kachisi. Zinali kuwakumbutsa umodzi wa mtundu wawo monga anthu okha padziko lapansi amene Yehova anawadalitsa ndi kuwayanja. Chaka ndi chaka, timakhala ndi mwaŵi wa kusangalala ndi mayanjano ofananawo a umodzi ndi chimwemwe limodzi ndi zikwi za abale ndi alongo athu. Lerolino misonkhano yachigawo yapachaka ndiyo imodzi ya njira zimene Yehova amasonkhanitsira anthu ake kaamba ka chilangizo ndi mayanjano.
2 Kusamalira anthu a Yehova ambirimbiri okhala m’Yerusalemu ndi kunja kwake m’nyengo ya madyerero kunafuna makonzedwe abwino. Kusunga bata ndi mtendere mwachionekere kunafuna kupereka malangizo a malo ogona, nthaŵi zosonkhana, ndi zofunika zina. Pakuti nkhani zimenezi zinakhudza kulambira kwawo koona, Aisrayeli anasangalala kutsatira malangizo ameneŵa.—Sal. 42:4; 122:1.
3 Pamene makonzedwe akupita patsogolo a Msonkhano wathu Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu,” pali zinthu zina zomwe tikufuna kuti muzisamalire ndi kuzilingalira mosamalitsa. Kukhala kwanu wogwirizana kudzasonyeza chiyamikiro chanu pamakonzedwe onse opangidwa kaamba ka inu. Ngakhale kuti zinthu zina mwa zimenezi tinazifotokozapo kale, nkofunika kuti aliyense wa ife akhale akudziŵa bwino lomwe thayo lathu pamaso pa Yehova pakuchirikiza makonzedwe a msonkhano wachigawo.
4 Makonzedwe a Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amapanga makonzedwe awoawo a kukhala ndi achibale kapena mabwenzi m’mizinda ya misonkhano yachigawo. Kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’mipanda yaikulu yomangidwa ndi antchito odzifunira a msonkhano wachigawo. Pamisonkhano yachigawo yoŵerengeka amagwiritsira ntchito zipinda za sukulu monga malo ogona ena opezekapo. Pamene tikukhala panyumba za abale kapena za achibale, sikoyenera kwa nthumwi kudyerera kuchereza kwa abale athu mwa kuganiza kuti adzatisunga masiku enanso pambuyo pa msonkhano wachigawo kuti tichite tchuthi. Zipindazi ndi za nyengo ya msonkhano wachigawo chabe. Aja opatsidwa malo ogona ayenera kutsimikizira kuti iwo ndi ana awo akulemekeza nyumba ya wocherezayo ndi kuti sakuwononga zinthu kapena kusanthulasanthula katundu kapena kuloŵa m’malo amene sayenera kuloŵamo. Ngati eni nyumba apeza vuto lililonse pankhaniyi, ayenera mwamsanga kudziŵitsa Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzafuna kuthandiza.
5 Zosoŵa Zapadera: Makonzedwe ameneŵa ali kokha a ofalitsa amene ali ndi kaimidwe kabwino, kuphatikizapo aja okhala ndi ana odzisunga bwino, amene avomerezedwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo. Makonzedwe osamalira anthu okhala ndi zosoŵa zapadera ayenera kupangidwa ndi mpingo umene amasonkhanako, osati kukankhira thayoli kwa oyendetsa msonkhano. Akulu ndi ena omwe akudziŵa za mkhalidwe wa munthu angapereke thandizo mwachikondi. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimafuna kuti ofalitsa alingalire zosoŵa za aja a mu utumiki wanthaŵi zonse, okalamba, athanzi lofooka, ndipo mwina enanso. Ofalitsa angapereke thandizo mwa kupita nawo oterowo kapena kusamalira zosoŵa zawo m’njira zina.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:4.
6 Aja amene ali ndi zosoŵa zapadera SAYENERA kukapempha chipinda ku msonkhano wachigawo pamene afika chifukwa Dipatimenti ya Zipinda iyenera kukhala ndi chitsimikizo cha Komiti Yautumiki Yampingo.
7 Kukaloŵa Msonkhano Kwina: Mpingo uliwonse unagaŵidwa ku msonkhano wapafupi. Malinga ndi chiŵerengero cha ofalitsa ogaŵidwa kukaloŵa msonkhano uliwonse, Sosaite imayerekezera chiŵerengero cha omwe adzapezekapo kotero kuti akonze malo okhala okwanira, zipinda, mabuku, ndi zina zotero. Komabe, ngati pachifukwa chomveka mudzaloŵa msonkhano umene simunagaŵidweko ndipo mudzafuna malo ogona, mlembi wa mpingo angaode Fomu Yopemphera Chipinda ku Sosaite imene muyenera kudzaza ndi kusaina. Ndiyeno itumizeni kumalikulu a msonkhano umene mudzapezekako.
8 Kupeŵa Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira, chimene makamaka chimabutsa moto pamisonkhano sindicho kuphika chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa oseŵera ndi moto kapena kuuyang’anira. Chotero, kaamba ka chisungiko chanu ndi cha abale anu, musalole ana anu kuyendayenda okha; musasiyire ana aang’ono madzi oŵira kuti awayang’anire, kapena kuti ayang’anire moto wophikira. Iwo angathe kuchita bwino kwambiri zinthu zimenezi kunyumba, koma malo a msonkhano ndi malo ena ndipo pafunika chisamaliro chachikulu kuti pasachitike ngozi. Anthu ambiri amakhalirana pafupi, ndipo ana amakonda kuseŵera maseŵero pamene ali ndi ana anzawo. Amacheutsidwa mosavuta ndipo samaona ngozi, choncho sitiyenera kuwapatsa makandulo, macheso kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kukamvetsera maprogramu tsikulo nasiya ana aang’ono kumsasa popanda wowayang’anira. Ana ayenera kukhala pamodzi ndi makolo awo mkati mwa programu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda okha pamalo a msonkhano, ayenera kubweza anawo kwa makolo awo. Makolo, chonde gwirizanani ndi antchito a msonkhano ndipo mwakutero sonyezani ‘kukonda abale.’—1 Pet. 2:17.
9 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso zapanthaŵi yake zokhudza misonkhano. Nzachisoni kuti pamisonkhano ingapo m’zaka zapitazi, ena obwera kumisonkhano anataya zinthu zawo chifukwa cha moto umene ukanapeŵedwa. Abale amene ali ndi mathayo pamisonkhano, ndipo makamaka makolo, akupemphedwa kusamala kwambiri mfundo zofunika zimenezi kuti misonkhano yathu idzakhale ya chiyanjano chomangirira ndi chokondweretsa, ndipo isadzakhale ya kulira ndi chisoni chifukwa cha kusasamala kochititsa ngozi.
10 Mufunikira Kukhala Wogwirizana: Kuti msonkhano uyende bwino ndi kuti ukhale wachipambano zimadalira pa kugwirizana kwa onse oloŵetsedwamo. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.) Sosaite imathokoza kwambiri chichirikizo chanu m’zandalama ndi m’mbali zinanso zimene abalenu ndi alongo mwakhala mukupereka pamakonzedwe a msonkhano wachigawo. Zimenezi zatheketsa kuchita lendi masitediyamu abwino m’mizinda ndi kusamalira zowonongedwa pa msonkhano. Zakutheketsaninso inuyo kusachoka pamalo amsonkhano pakupuma kwachidule kwamasana, ndipo pambuyo pakupuma, mwakhala wokonzekera kumvetsera programu yauzimu yofunika kwambiri.
11 Mwa kukhalapo pa misonkhano ya anthu a Yehova, timalimbitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova ndipo timatetezeredwa ku ziyambukiro zakunja za dziko zimene zingawononge chikhulupiriro chathu chachikristu. Tonsefe tikuthokoza kuti Yehova wapereka nyengo zimenezi zakuti anthu ake odzipatulira atsitsimulidwe mwauzimu m’nthaŵi ino ya mapeto.
12 Labadirani Chitsogozo cha Sosaite: Mfundo imeneyi iyenera kukhala pakati pa zinthu zofunika kwambiri. Ahebri 13:17 amati “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” Pamene abale athu akuchita zambiri kutikonzekera msonkhano wachigawo, tikufuna kuti aone kuti tikuwachirikiza mokwanira. Pakuti timapemphedwa kukhala ogwirizana pankhaniyi pamasiku aŵiri kapena atatu chabe pachaka, ndi njira yabwino yochirikizira khama lawo. Ngakhale ngati chifuno chathu chingakhale chosiyana, chitsanzo chathu chabwino chimalimbikitsa mzimu wachikondi, waumodzi ndi wochirikizana, monga momwe abale athu aonera limodzi ndi a kudziko omwe.—Afil. 2:1-4.
13 Musalole Chakudya Kukucheukitsani: Salmo 119:33 limapereka pemphero lochokera pansi pamtima: “Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; Ndidzaisunga kufikira kutha kwake.” Ndithudi, mawuŵa amasonyeza malingaliro a atumiki odzipatulira onse a Yehova. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” walinganiza masiku atatu okambitsirana “malemba” a Yehova ndi kuwasonyeza. Kodi mudzakhalapo ndi kutchera khutu pamagawo onse kuyambira panyimbo ndi pemphero loyamba pa Lachisanu mmaŵa mpaka nyimbo ndi pemphero pa Sande masana? Palibe amene angafune kuphonya mbali iliyonse ya programuyi. Kungakhale kulakwa kuganiza kuti pangakhale tsiku kapena mbali ya programu imene ingakhale yosafunika kwambiri. Masiku onse atatu tiyenera kuwayesa chakudya chofunika chateokrase, chonse chofunikira kuti tikhale ndi thanzi lauzimu ndi kukula mwauzimu.
14 Pamsonkhano wathu wachigawo wa chaka chatha, tinaona kuti pali kufunika kwa kuwongolera khalidwe lathu pamsonkhano. Anthu ambiri anali kuyendayenda, kulankhula, kuphika ndi kudya, pamene maprogramu anali mkati pambuyo pa kupuma kwamasana masiku onse atatu. Pamsonkhano wina, khamu lalikulu la anthu linaonedwa likutuluka m’sitediyamu kutatsala ola limodzi programu isanathe ndi pemphero lomaliza. Ndithudi, ena anali kulankhula mokweza mawu kwa ena okhala pafupi nawo, akumadodometsa ena m’malowo omwe anali kuyesa kumvetsera programu. Achikulire ndi achichepere omwe akhala akuchita zimenezi. Pomakambitsirana, panalinso kupatsirana zakudya ndi zakumwa pakati pa mabwenzi ndi achibale omwe anakhala pafupi nawo. Nthaŵi zina kukambitsirana ndi kuyendayendako m’njira zapafupi kunakhala kwaphokoso kwambiri kwakuti okhala chakumbuyo kwenikweni kapena pafupi ndi potulukira analephera kumva bwino programu. Choncho ana ena sanayang’aniridwe nthaŵi zina, ndipo ngakhale achikulire ena asonyeza kupanda ulemu pamisonkhano yateokrase imeneyi. Kodi tingachitenji kuti tipeŵe mikhalidwe imeneyi?
15 Tifunikira kukumbukira cholinga chathu chofikira pamsonkhano. Pokhala kuti timatayirapo nthaŵi ndi ndalama kuti tifikepo, kodi si kwanzeru kuti tipindule mokwanira pa zimene timatayazi? Ndithudi nkwanzeru! Motero, kodi sibwino kuti tifike mwamsanga, kuti asamalire zinthu zonse zofunika, monga ngati kuphika chakudya chammaŵa ndi chamasana, moti programu itipeza titakhala kale? Zimenezi zidzakupatsani mpumulo, maganizo anu ali omasuka ku nkhaŵa zina zosakhudza programu. Izi zidzakuthandizani kukhala omvetsera otchera khutu. Nchifukwa ninji kumvetsera kuli kofunika?
16 Pa Yesaya 55:2 Yehova analamula Israyeli kuti: “Mverani Ine mosamalitsa.” Liwu lakuti “mosamalitsa” limamasuliridwa kuti “kusumika maganizo mosamalitsa kapena mofunitsitsa.” Israyeli anali ndi chifukwa chabwino chomverera mosamalitsa chifukwa chakuti Yehova anali kupereka uthenga wa chimasuko womwe unali monga chakudya chomanga thupi ndi chakumwa chotsitsimula. Uthenga umene Yehova akupereka kwa anthu ake lerolino ulinso ndi phindu lofananalo. Kwenikweni uli wamtengo wapatali kwambiri chifukwa chakuti ndiwo uthenga wonena za moyo wosatha. Kodi ndani yemwe samafuna kudziŵa za zifuno za Yehova kulinga kwa mtundu wa munthu? Ngati titchera khutu pamsonkhano ‘tidzamvetsera ndi kuwonjezera kuphunzira.’ (Miy. 1:5) Kumvetsera ndi kuphunzira pamsonkhano wachigawo kaŵirikaŵiri kumafuna khama ndi kutchera khutu kokulirapo kuposa pa Nyumba ya Ufumu. Koma mapindu ake auzimu ali oyenerera.
17 Chikumbutso ku Bungwe la Akulu: Mlembi wa mpingo ayenera kusamalira nkhani zonse zokhudza msonkhano wachigawo ndi zilengezo pa Misonkhano Yautumiki ilinkudza. Akulu onse ayenera kugwirizana bwino kuti nkhani zokhudza msonkhano wachigawo zisamaliridwe mwamsanga, motenthedwa maganizo ndi mogwira mtima.
18 Mawu Omaliza: Yesaya 33:20 amati: “Tayang’ana pa Ziyoni, mudzi wa mapwando athu.” Titha kulingalira za makamu a anthu osangalala omwe anali kudzaza Yerusalemu amene anavomereza ndi mtima wonse lamulo la Yehova lakuti ‘mukondwere monsemonse.’ (Deut. 16:15) Misonkhano yathu yachigawo ya pachaka imatipatsa mpata wabwino koposa wakulandira malangizo aumulungu ndi wakusangalala ndi mayanjano ndi abale ndi alongo athu. Yehova adalitsetu zoyesayesa zanu pamene mukukonzekera kudzaloŵa umodzi wa misonkhano yachigawo ya 1997 ya “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”!