Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 1999 wa “Mawu Aulosi a Mulungu”
1 Pamene Aisrayeli anali m’chipululu, Yehova anauza Mose kupanga malipenga aŵiri asiliva. Ngati analiza lipenga limodzi, akalonga a mafuko anali kusonkhana pakhomo la chihema chokomanako. Kulira kwa malipenga aŵiriwo kunali kutanthauza kuti khamu lonse la Aisrayeli lisonkhane pamodzi. (Num. 10:1-4) Lerolino, mofanana ndi kulira kwa malipenga, kodi sitikhala osangalala pamene timva zilengezo zotisonkhanitsira ku misonkhano yathu yachigawo yochitika pachaka? Kumisonkhano yathu timalandira malangizo ndi chitsogozo cha Yehova kupyolera m’Mawu ake ndi oimira ake oikidwa. Izi zimatithandiza ife kupitirizabe kukhala olimba mu utumiki wa Mulungu. Kodi sitikhala osangalala pamene tiona zikwi—mwinanso zikwi makumi ambiri—za alambiri anzathu atasonkhana pamodzi m’chikondi ndi m’mtendere? Mosakayikira timatero!—Sal. 122:1, 7, 8.
2 Mu August 1998, m’Malaŵi muno munachitika Misonkhano Yachigawo 15 ya “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Banja lina la amishonale linali nafe kuno ku Malaŵi pamisonkhano. Kupezekapo kwawo kunali kolimbikitsa mwauzimu kwa onse. Pamene tikusonkhana pamodzi pamsonkhano wathu wachigawo wa 1999, tidzakhala ndi mwayi wina woona ubale wathu wamtengo wapatali ndi kuthokoza Yehova kaamba ka umodzi umene watipatsa.
3 Makonzedwe a Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amapanga makonzedwe awo okakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’mizinda ya msonkhano. Kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’misasa yogonamo anthu ambiri yomwe antchito odzifunira amakonza. Pamisonkhano ingapo, osonkhana amawapezera malo ogona m’madomitale a pasukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu n’kumangokhalabe komweko masiku ambiri kuti muthere konko tchuthi msonkhanowo utatha. Zipinda zimenezo ndi zanthaŵi ya msonkhano yokha. Amene apatsidwa malo choncho ayenera kuona kuti iwowo pamodzi ndi ana awo akuchita mwaulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kuloŵa malo osayenera iwo kuloŵamo. Ngati eninyumba akuona kuti zina ndi zina zikuwavuta pankhani imeneyi, ayenera kukauza Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
4 Zosoŵa Zapadera: Makonzedwe amenewa ali kokha a ofalitsa amene ali ndi kaimidwe kabwino, kuphatikizapo aja amene ali ndi ana akhalidwe labwino, amene avomerezedwa ndi komiti yautumiki yampingo. Makonzedwe osamalira anthu amene ali ndi zosoŵa zapadera ayenera kupangidwa ndi mpingo umene iwo amasonkhanako, osati kukankhira udindowo kwa oyendetsa msonkhano. Akulu ndi ena omwe akudziŵa za mkhalidwe wa munthu angapereke thandizo mwachikondi. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimafuna kuti ofalitsa alingalire zosoŵa za aja amene ali mu utumiki wanthaŵi zonse, okalamba, athanzi lofooka, mwinanso za ena. Ofalitsa angapereke thandizo mwa kupita nawo oterowo kapena kusamalira zosoŵa zawo m’njira zina.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:4.
5 Aja amene ali ndi zosoŵa zapadera SAYENERA kukapempha chipinda ku msonkhano pamene afika chifukwa Dipatimenti ya Zipinda iyenera kukhala ndi chitsimikizo cha Komiti Yautumiki Yampingo.
6 Kupita ku Msonkhano wa Kwina: Mpingo uliwonse umagaŵidwa ku msonkhano wapafupi. Malinga ndi chiŵerengero cha ofalitsa ogaŵidwa kupita ku msonkhano uliwonse, Sosaite imayerekeza chiŵerengero cha omwe adzapezekapo kotero kuti akonze malo okhala okwanira, mabuku, malo ogona, ndi zina zotero. Komabe, ngati pachifukwa chomveka mudzapite ku msonkhano umene simunagaŵidweko ndipo mudzafuna malo ogona, mlembi wa mpingo angaode ku Sosaite fomu ya Special Needs Room Request imene muyenera kuidzaza kenako kuisainitsa. Ndiyeno itumizeni ku msonkhano umene mudzapite.
7 Kupeŵa Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira, chimene makamaka chimabutsa moto pamisonkhano sindicho kuphika chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa amene amaseŵera ndi moto kapena kuuyang’anira. Chotero, kaamba ka chisungiko chanu ndi cha abale anu, musalole ana anu kuyendayenda okha; musauze ana aang’ono kuti ayang’anire madzi oŵira, kapena kuti ayang’anire moto wophikira. Iwo angathe kuchita bwino lomwe zinthu zimenezi kunyumba, koma malo a msonkhano ndi malo ena ndipo pafunika chisamaliro chachikulu kuti pasachitike ngozi. Anthu ambiri amakhalirana pafupi, ndipo ana amakonda kuseŵera pamene ali ndi ana anzawo. Sachedwa kudodometsedwa ndipo samaona ngozi, choncho sitiyenera kuwapatsa makandulo, macheso kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kukamvetsera mapologalamu ndi kusiya ana aang’ono kumsasa popanda owayang’anira. Ana ayenera kukhala pamodzi ndi makolo awo mkati mwa pologalamu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda okha pamalo a msonkhano, ayenera kuwapititsa kwa makolo awo. Makolo! chonde gwirizanani ndi antchito a msonkhano ndipo mwakutero sonyezani ‘kukonda abale.’—1 Pet. 2:17.
8 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso zapanthaŵi yake zokhudza misonkhano. N’zachisoni kuti pamisonkhano ingapo m’zaka zapitazi, ena opezeka pamisonkhano zinthu zawo zinawonongeka chifukwa cha moto umene ukanapeŵedwa. Abale amene ali ndi udindo pamisonkhano, makamaka makolo, akupemphedwa kusamalira kwambiri mfundo zofunika zimenezi kuti misonkhano yathu idzakhale ya mayanjano omangirira ndi okondweretsa, isadzakhale ya kulira ndi chisoni chifukwa cha kusasamala komwe kungachititse ngozi.
9 Mufunikira Kukhala Wogwirizana: Kuti msonkhano uyende bwino ndi kuti ukhale wachipambano zimadalira kugwirizana kwa onse oloŵetsedwamo. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.) Sosaite imathokoza kwambiri chithandizo chanu cha ndalama ndi zinthu zinanso zimene abale ndi alongo mwakhala mukupereka kuchirikiza makonzedwe a msonkhano wachigawo. Zimenezi zatheketsa kuchita lendi mabwalo a maseŵera abwino m’mizinda ndi kusamalira zowonongedwa pa msonkhano. Zachititsanso kuti musachoke pamalo a msonkhano pakupuma kwachidule kwamasana, ndipo pambuyo pa kupuma, mwakhala wokonzekera kumvetsera pologalamu yauzimu yofunika kwambiri.
10 Mwa kupezeka pa misonkhano ya anthu a Yehova, timalimbitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova ndipo timatetezeredwa ku zinthu za dziko zimene zingawononge chikhulupiriro chathu chachikristu. Tonse tikuthokoza Yehova kuti wapereka nyengo zimenezi zakuti anthu ake odzipatulira atsitsimulidwe mwauzimu m’nthaŵi ino ya mapeto.
11 Labadirani Chitsogozo cha Sosaite: Mfundo imeneyi iyenera kukhala pakati pa zinthu zofunika kwambiri. Ahebri 13:17 amati: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” Pamene abale athu akuchita zambiri kutikonzera msonkhano wachigawo, tikufuna kuti aone kuti tikuwachirikiza mokwanira. Pakuti timapemphedwa kukhala ogwirizana pankhaniyi masiku aŵiri kapena atatu chabe pachaka, ndi njira yabwino yochirikizira khama lawo. Ngakhale ngati timakonda zosiyana, chitsanzo chathu chabwino chimalimbikitsa mzimu wachikondi, waumodzi ndi wochirikizana, monga momwe abale athu aonera pamodzi ndi anthu akudziko.—Afil. 2:1-4.
12 Musalole Chakudya Kukudodometsani: Salmo 119:33 ndi pemphero lochokera pansi pa mtima: “Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake.” Ndithudi, mawu amenewa amasonyeza malingaliro a atumiki odzipatulira onse a Yehova. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” walinganiza masiku atatu okambirana “malemba” a Yehova ndi kuwasonyeza. Kodi mudzakhalapo ndi kutchera khutu pamagawo onse kuyambira pa nyimbo ndi pemphero loyamba pa Lachisanu m’mawa mpaka nyimbo ndi pemphero lomaliza pa Lamlungu masana? Palibe amene angafune kuphonya mbali iliyonse ya pologalamu ya msonkhano. Kungakhale kulakwa kuganiza kuti padzakhala tsiku kapena mbali ya pologalamu imene ili yosafunika kwambiri. Masiku onse atatu tiyenera kuwayesa chakudya chofunika chateokalase, chonse chofunikira kuti tikhale ndi thanzi lauzimu ndi kukula mwauzimu.
13 Takhala tikulandira mawu akuti tifunika kuwongolera khalidwe lathu pamsonkhano. Masiku onse atatu a msonkhano wachaka chatha anthu ambiri anali kumayendayenda, kulankhulana, kuphika ndi kumadya, mapologalamu ali mkati nthaŵi yopuma itatha. Pamsonkhano wina, khamu la anthu linali kumatuluka m’bwalo lamaseŵero kutatsala pafupifupi ola lathunthu kuti apereke pemphero lomaliza. Ndiponso ena anali kumalankhula mokweza ndi munthu woti ali naye pafupi, akumasokoneza ena amene anali kumvetsera pologalamu. Ana ndi achikulire omwe achita zimenezi. Polankhulanapo, anali kumapatsana zakudya ndi zakumwa, mabwenzi ndi a m’banja lawo amene anali nawo pafupi. Nthaŵi zina makambitsirano ndi kuyendayenda mu tinjira toyandikira zimachititsa phokoso kotero kuti amene anakhala pafupi ndi kumbuyo kapena kukhomo lotulukira amapeza vuto kumvera pologalamu. Ndiponso ana ena amasiyidwa osayang’aniridwa, ndipo ngakhale achikulire amene asonyeza kupanda ulemu pamisonkhano yateokalase imeneyi. Kodi tingatani kuti tipewe zimenezi?
14 Tiyenera kukumbukira cholinga chathu chopitira ku msonkhano. Chifukwa kumafuna kupeza nthaŵi ndi ndalama kuti tikapezekeko, kodi sikungakhale kwanzeru kukapindula mokwanira ndi zinthu tawonongazi? Ndithudi inde! Pachifukwa chimenechi, kodi sikwanzeru kufika mofulumira, kukonza chilichonse chofuna chisamaliro, monga chakudya cha mmaŵa ndi chamasana, ndi kukhala pansi pamene mapologalamu ayamba? Izi zidzakupangitsa kukhala womasuka, ndipo simudzadera nkhaŵa ndi nkhani zosakhudzana ndi pologalamu.
15 Chikumbutso ku Bungwe la Akulu: Mlembi wa mpingo ayenera kusamalira nkhani ndi zilengezo zokhudza msonkhano wachigawo m’Misonkhano Yautumiki yam’tsogolo. Akulu onse ayenera kugwirizana mokwanira kuti asamalire mwamsanga, bwino, ndi mogwira mtima nkhani zokhudza msonkhano.
16 Tikukulimbikitsani kuti mukonzekere pakalipano zokapezeka pa Msonkhano Wachigawo wa 1999 wa “Mawu Aulosi a Mulungu” masiku onse atatu. Tikuyembekezera nanu pamodzi kukamvera “mawu akuimbitsa ndi kuyamika” auzimu a awo amene akulambira Mulungu monga gulu logwirizana. (Sal. 42:4) Yehova adalitsetu makonzedwe onse amene akupangidwa kuti thanzi lathu lauzimu lipitirize kumalimba.
[Bokosi patsamba 3]
Nthaŵi ya Mapologalamu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8:45 a.m. – 4:50 p.m.
Lamlungu
8:45 a.m. – 4:50 p.m.
[Bokosi patsamba 6]
CHIDZIŴITSO CHOWONJEZEREKA CHA MSONKHANO WACHIGAWO WA 1999:
Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March tinalengeza kuti madera amene agaŵidwa adzalemberedwa makalata owadziŵitsa za malo a msonkhano amene akuyenera kupitako. Komano, tikukhulupirira kuti kulemba zimenezi mu Utumiki Wathu wa Ufumu kudzathandiza wofalitsa aliyense amene zikum’khudza kudziŵa bwino.
August 6-8
BLANTYRE (Chingelezi)
Mpingo wa Lilongwe 1 M-11, Mpingo wa Blantyre M-23
August 13-15
BLANTYRE (Chichewa)
Mipingo yonse ya mu M-23 idzapite ku Msonkhano wachichewa wa ku Blantyre kupatulapo Mpingo wa Blantyre.
Mu M-20, mipingo iyi idzapite ku Msonkhano wachichewa wa ku Blantyre:
Chibvumbe, Gorden, Kaphikamtama, Machowa
Mipingo yotsala ya mu M-20 idzapite ku Msonkhano wa ku Songani.
Mu M-21, mipingo iyi idzapite ku Msonkhano wachichewa wa ku Blantyre:
Chikwawa 2 Chiromo, 1 Makungu, 1 Mikombo, Mitondo, Mkhate, Namiyala, Naphala, Nchalo, Nsanje, Ntowe, Saopa, Supuni
Mipingo yotsala ya mu M-21 idzapite ku Msonkhano wa ku Nkhonya.
August 20-22
KANDE
Mipingo 14 yotsatirayi ya mu M-3 idzapite ku Msonkhano wa kwa Kande:
Chihame, Chituka, Dyaka, Kachere, Kakwewa, Kande, Lisambe, Liuzi, Lumbiya, Mbamba, Mgodi, Munkhokwe, Mwaya, Tukombo
Mipingo yotsala ya mu M-3 idzapite ku Msonkhano wa ku Mzuzu.
Mipingo inayi yotsatirayi ya mu M-5 idzapite ku Msonkhano wa kwa Kande:
Kapando, Khuyu, Mchenga, Msauka
Mipingo yotsala ya mu M-5 idzapite ku Msonkhano wa ku Nkhotakota.
Misonkhano ina yonse ili monga mmene zinalembedwera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1999.