Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Maulaliki ena ali m’munsimu sangagwire ntchito pa magazini ya Nsanja ya Olonda ya m’Chitumbuka. M’madera amene amalankhula Chitumbuka, mungagaŵire magazini a Chicheŵa kapena a Chingelezi kapena mutha kusintha maulalikiwa kuti agwirizane ndi nkhani za m’magazini a Chitumbuka.
Nsanja ya Olonda Sept. 15
“Pafupifupi m’zipembedzo zonse muli anthu okonda choonadi. Komabe, nthaŵi zambiri zipembedzo zimagaŵanitsa anthu. Kodi chofunika n’chiyani kuti anthu oona mtima agwirizane? [Akayankha, ŵerengani Zefaniya 3:9.] Magazini iyi ikusonyeza momwe kudziŵa Mulungu woona kukugwirizanitsira anthu padziko lonse.”
Galamukani! Oct. 8
“Ambirife timaganiza kuti sizidzatheka kuti dziko lisoŵe chakudya. Koma tsopano anthu akuda nkhaŵa kuti sayansi ingawononge chakudya. Magazini iyi ikufotokoza zina mwa zimene zikudetsa nkhaŵa komanso ikufotokoza chiyembekezo cha m’Baibulo chomwe chingathetsedi vuto limeneli.
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“Mungandivomereze kuti masiku ano kukhulupirira Mulungu sinkhani yofala kwa anthu ambiri. Koma kodi n’chifukwa chiyani zili motero? [Akayankha, ŵerengani Ahebri 11:1.] Magazini iyi ikulongosola tanthauzo la chikhulupiriro chenicheni ndiponso phindu lokhala ndi chikhulupiriro.”