Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/01 tsamba 1
  • Kodi Mukuchita Utumiki Wanu Mokwanira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukuchita Utumiki Wanu Mokwanira?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Gawirani Magazini Amene Amachitira Umboni Choonadi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Dzikonzereni Ulaliki Wanu wa Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Maulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 9/01 tsamba 1

Kodi Mukuchita Utumiki Wanu Mokwanira?

1 M’buku la Machitidwe, timauzidwa kuti ophunzira a Yesu anakwaniritsa utumiki wawo chifukwa “anachita umboni [“mokwanira,” NW]” kwa anthu. (Mac. 2:40; 8:25; 28:23) Ndithudi, ndicho chinali cholinga cha mtumwi Paulo. (Mac. 20:24) Kodi chimenechi si cholinga chanu monga mtumiki wa uthenga wabwino? Kodi mungachite bwanji zimenezi?

2 Konzekerani Ulaliki Wanu: Kuti muonetsetse kuti mukulalikira zomveka muutumiki, n’kofunika kukonzekera. Izi n’zoona makamaka pogaŵira magazini, popeza nthaŵi zonse nkhani zake zimakhala zosiyanasiyana. Potithandiza kuti tikhale achikwanekwane, Utumiki Wathu wa Ufumu uno uli ndi chinthu chatsopano chomwe ndi danga limene lili kudzanja lamanzere, limene likusonyeza zitsanzo za ulaliki pogaŵira magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! M’kope lililonse muzikhala nkhani ya panthaŵi yake imene ingakope anthu ambiri. Kodi mungagwiritse ntchito motani maulaliki aafupiafupi ameneŵa?

3 Sankhani malingaliro amene mukuona kuti angagwire ntchito kwambiri m’gawo lanu. Ŵerengani bwinobwino nkhani imene atchulayo, ndipo gwirani mfundo zapadera zimene mosapeneka zingadzutse chidwi. Sankhani m’magazinimo lemba limene likugwirizana ndi mfundo zimene mukufuna kukambiranazo komanso limene mungathe kumuŵerengera mwininyumba. Phatikizanipo mawu omaliza achidule olimbikitsa mwininyumba kuŵerenga magaziniyo komanso ngati n’koyenera phatikizanipo mawu achidule akuti angapereke kangachepe kothandizira ntchito ya Mboni za Yehova ya padziko lonse. Ndiyeno, yesererani ulaliki wanuwo.

4 Konzekerani Kugwiritsa Ntchito Baibulo: Nthaŵi zambiri kukonzekera bwino kungakuthandizeni kuti polalikira muziphatikizapo lemba. Mwachitsanzo, m’madera ambiri ofalitsa aluso zikuwayendera bwino mwakupita panyumba ya munthu Baibulo lili m’manja, kupereka moni kwa mwininyumba ndi kunena kuti:

◼ “Tikufunsa anthu ngati amakhulupirira izi . . .” Ŵerengani Genesis 1:1, ndiyeno funsani kuti: “Kodi mukuvomerezana nawo mawu ameneŵa?” Akati inde, nenani kuti: “Inenso ndikuvomerezana nawo. Komabe, kodi mukuganiza kuti ngati Mulungu analenga zinthu zonse, ndiye kuti ndi amenenso akupangitsa kuipa? Mukayamikira yankho lake, ŵerengani Mlaliki. 7:29. Vundukulani buku la Chidziŵitso patsamba 71, ndipo ŵerengani ndime 2. M’limbikitseni munthuyo kuŵerenga bukulo ndipo fotokozani makonzedwe a chopereka.

5 Bwererani kwa Anthu Onse Amene Anasonyeza Chidwi: Simungachite utumiki wanu mokwanira ngati simubwerera kwa anthu achidwi amene munawapeza. Mukakhala ndi makambirano abwino ndi munthu wina, kaya mwam’gaŵira magazini kapena mabuku ena alionse kapena simunam’gaŵire, lembani dzina ndi adiresi yake. Yesetsani kuwonjezera chidwi chake mwa kubwererako mofulumira. Musakayike, m’pempheni kuphunzira naye Baibulo.

6 Ophunzira a m’zaka za zana loyamba ankadziŵa kuti Yesu anawalamula kuti ‘achitire umboni [“mokwanira,” NW].’ (Mac. 10:42) Lamulo limeneli likugwiranso ntchito pa ife, popeza ndi njira yokhayo imene tingapangire ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tichite utumiki wathu mokwanira.—2 Tim. 4:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena