Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/01 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 10
  • Mlungu Woyambira September 17
  • Mlungu Woyambira September 24
  • Mlungu Woyambira October 1
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 9/01 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 10

Nyimbo Na. 86

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 13: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 22: “Kodi Mukuchita Utumiki Wanu Mokwanira?” Kambani mawu oyamba m’mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndi omvetsera ndime 1-3, sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule za ulaliki wa magazini—gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya September 15. Mukatha kukambirana ndime 4, chitani chitsanzo cha ulaliki umene asonyeza pamenepowo. Gwiritsani ntchito buku la Chidziŵitso.

Nyimbo Na. 124 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 17

Nyimbo Na. 92

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Malipoti a maakaunti.

Mph. 15: “Kodi Mumaloŵa mu Utumiki Wakumunda Nthaŵi Zonse?” Kambani mawu oyamba m’mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

Mph. 12: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhaniyi ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pendani mfundo zazikulu pa lipoti lampingo la chaka chautumiki cha 2001. Yamikirani zinthu zabwino zimene anthu onse anachita. Kambani kwambiri za mmene mpingo wachitira pankhani yopezeka pamisonkhano, yoloŵa mokhazikika muutumiki wakumunda, ndiponso pantchito yochititsa maphunziro a Baibulo, ndipo tchulani zinthu zina zimene zingawathandize kuti apite patsogolo m’mbali zimenezi. Nenani zolinga zimene angathe kukwaniritsa m’chaka chimene chikubwerachi.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani. Pendani ndandanda yampingo ya mlungu ndi mlungu ya misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Fotokozani mmene opezekapo angathandizire kuti zokambirana pamisonkhano imeneyi zizikhala zopindulitsa. Limbikitsani mpingo kuthandiza makonzedwe a utumiki ameneŵa.

Nyimbo Na. 129 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 24

Nyimbo Na. 97

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Sonyezani zitsanzo ziŵiri za ulaliki pogwiritsa ntchito malingaliro a mu “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.”

Mph. 30: Kondani Mulungu—Osati Zinthu za M’dziko. (1 Yoh. 2:15-17) Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera, kupenda pulogalamu ya msonkhano wadera umene unachitika chaka chautumiki chapitacho. Pemphani ofalitsa kunena mfundo zazikulu zimene anaphunzira ndiponso momwe iwo agwiritsira ntchito mfundozo pawokha kapena pabanja. (Mungawauziretu mbali zimene adzakambe.) Kambani mbali za papulogalamu izi: (1) “Kukonda Mulungu Kumatisonkhezera mu Utumiki Wathu.” Chikondi chimenechi chimatithandiza kuthetsa malingaliro olefula monga mantha, kudziona kukhala wosakwanira ndiponso kuopa anthu, zimene zingalepheretse ntchito yathu. (2) “Okonda Yehova Amadana ndi Choipa.” (w99-CN 10/1 28-31) Kuti tikhale paubale ndi Mulungu tifunika kudana ndi choipa—osati zinthu zimene zikudziŵikiratu kuti ndi zolakwika zokha komanso zinthu zosadziŵika bwino kuti n’zolakwa. (3)  “Londolani Njira Yokoma Koposa ya Chikondi.” (w92-CN 7/15 27-30) Akorinto woyamba chaputala 13 vesi 4 mpaka 8 amasonyeza chifukwa chake tifunika kupirira moleza mtima zolakwa zopanda ungwiro za ena, kupeŵa kukhala odzikonda ndi a mpikisano, kusafalitsa miseche yowononga, ndi kukhalabe okhulupirika ku gulu la Mulungu. (4)  “Zinthu za M’dziko—Kodi Timaziona Motani?” Tisakonde zinthu za m’dziko, tisagonjere zilakolako za thupi, tisanyengedwe ndi zilakolako za maso, kapena kusamalira matamandidwe a moyo. (5)  “Kusakhala a Dziko Lapansi Kumatiteteza.” Akorinto wachiŵiri chaputala 6 vesi 14 mpaka 17 amasonyeza momwe miyambo ina, ndi zochita zina zingatipangitsire kukhala osavomerezeka kwa Mulungu. Tiyenera kuzindikira ndi kupeŵa misampha yonyengerera imene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito. (6) “Malonjezo Aumulungu kwa Okonda Mulungu.” (w86 6/15 5-6) Madalitso a Mulungu amawonjezera chisangalalo m’moyo wathu ndipo amatilemeretsa mwauzimu.—1 Tim. 6:17-19.

Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 1

Nyimbo Na. 106

Mph. 5:  Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a September.

Mph. 15:  “Zimene Tingachite Tikafunikira Chithandizo cha Mankhwala cha Mwamsanga.” Kambani mawu oyamba m’mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

Mph. 10: “Kulimbitsa Banja.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu amene amachititsa phunziro la banja mokhazikika.

Mph. 15: “Kodi Ntchito Imakulepheretsani Kulalikira?” Kambani mawu oyamba m’mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tsindikani kufunika kokhala wolingalira bwino pantchito yolembedwa. Kumachita kaye zinthu zimene zimaika Ufumu patsogolo. Pemphani mitu ya mabanja ina mumpingomo kuti isimbe mmene ikuthetsera vuto lopezera banja lawo zinthu zakuthupi popanda kunyalanyaza zosoŵa zawo zauzimu.

Nyimbo Na. 137 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena