Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 1
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kuti munthu akhale paubwenzi wolimba ndi Mulungu Wamphamvuyonse? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Machitidwe 17:27.] Nkhani iyi ikufotokoza chifukwa chake tikutsimikiza kuti Mulungu amafuna kuti tikhale mabwenzi ake.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 10.
Galamukani! July
“Zosangalatsa zambiri masiku ano zimasonyeza kuti anthu ambiri akuchita chidwi ndi zamizimu. Kodi mukuganiza kuti palibe vuto lililonse kuchita nawo zamizimu? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Deuteronomo 18:10-12.] Nkhani iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena zokhudza kuopsa kwa kukhulupirira mizimu.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 10.
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Anthu ambiri akuda nkhawa za tsogolo la dzikoli chifukwa cha nkhani zoopsa za kuwonongeka kwa zachilengedwe. Kodi maganizo anu ndi otani? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Salmo 37:11.] Magazini iyi ikupereka zifukwa za m’Malemba zotithandiza kusadera nkhawa.”
Galamukani! Aug.
“Anthu ambiri akukhulupirira kuti zamoyo padziko lapansi zitha chifukwa cha kutentha kwa dziko. Kodi mukuganiza kuti vuto limeneli lingathetsedwe bwanji? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Yesaya 11:9.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake sitiyenera kukayika ngakhale pang’ono kuti anthu adzapitirizabe kukhala pa dziko lapansi.”