Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/10 tsamba 2
  • Kodi Anthu Ena Angaphunzire Chiyani Poona Zochita Zanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Anthu Ena Angaphunzire Chiyani Poona Zochita Zanu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsa Ntchito Sukulu Kuwongolera Utumiki Wakumunda
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Tsatirani Chitsanzo cha Yesu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Ofalitsa Atsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 4/10 tsamba 2

Kodi Anthu Ena Angaphunzire Chiyani Poona Zochita Zanu?

1. Kodi ophunzira a Yesu anaphunzira chiyani poona zochita zake?

1 Yesu anati: “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine.” (Mat. 11:29) N’zoonekeratu kuti Yesu anaphunzitsa ena mwa zochita zake, osati mwa mawu okha. Taganizirani zimene ophunzira a Yesu anaphunzira poona zimene iye ankachita. Iye anali woleza mtima, wokoma mtima ndiponso wachikondi. (Mat. 8:1-3; Maliko 6:30-34) Ndiponso iye analidi wodzichepetsa zenizeni. (Yoh. 13:2-5) Poyenda ndi Yesu mu utumiki, ophunzira ake anaona kuti iye anali wolimbikira ntchito ndipo ankaphunzitsa anthu choonadi mogwira mtima. (Luka 8:1; 21:37, 38) Ndiyeno kodi anthu ena angaphunzire chiyani akationa tikulalikira?

2. Kodi kuvala bwino ndiponso khalidwe lathu labwino zingathandize bwanji eninyumba?

2 Eninyumba: Eninyumba angaphunzire zambiri poona mmene tavalira, makhalidwe athu abwino ndiponso poona mmene tikuwasonyezera chidwi. (2 Akor. 6:3; Afil. 1:27) Iwo amaona kuti timakonda kugwiritsa ntchito Baibulo. Anthu ena amakopeka akaona kuti tikumvetsera zimene iwo akunena. Choncho, musaganize kuti kusonyeza chitsanzo chabwino mwa njira imeneyi sikungathandize anthu kumvetsera uthenga wa Ufumu.

3. Kodi zochita zathu zabwino zingathandize bwanji abale athu?

3 Abale Athu: Ganiziraninso mmene zochita zathu zabwino zingathandizire abale athu. Anthu ena angayambe kulimbikira utumiki chifukwa choona kuti ndife olimbikira utumiki. Monga mmene chitsulo chimanolera chitsulo chinzake, tikamakonzekera bwino ulaliki, anthu ena angalimbikitsidwe kuti nawonso azikonzekera. (Miy. 27:17) Kuyesetsa kwathu kusunga mayina a anthu achidwi ndiponso kuyesetsa kuchita maulendo obwereza mofulumira, kungathandize abale athu kuchita chimodzimodzi. Tikamakwaniritsa utumiki wathu, tidzathandiza abale ndi alongo athu kuti azikondanso utumiki.—2 Tim. 4:5.

4. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi ndi nthawi tiyenera kuona zochita zathu ndiponso zolankhula zathu?

4 Ndibwino kuti nthawi ndi nthawi tiziganizira mmene zochita ndiponso zolankhula zathu zikukhudzira anthu ena. Zochita zanu zabwino zimasangalatsa Yehova ndipo zimatithandiza kugwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.”—1 Akor. 11:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena