Tsatirani Chitsanzo cha Yesu
1. Kodi Yesu anasonyeza chitsanzo chotani?
1 Tikamagwira nawo ntchito yopanga ophunzira, tizikumbukira kuti chitsanzo chathu chimakhudza kwambiri anthu amene akutiona. Yesu ankaphunzitsa kudzera m’mawu ndi zochita zake. Anthu anaona kuti anali wachangu, wokonda anthu, wofunitsitsa kuyeretsa dzina la Atate ake ndiponso anali ndi mtima wofuna kukwaniritsa chifuniro cha Atate ake.—1 Pet. 2:21.
2. Kodi chitsanzo chathu chingakhudze bwanji anthu amene timachita nawo utumiki?
2 Muutumiki wa Nyumba ndi Nyumba: Mofanana ndi Yesu, chitsanzo chathu chimakhudza anthu amene timachita nawo utumiki. Ofalitsa atsopano kapena amene sanazolowere kwambiri kulalikira akamaona changu chathu muutumiki, zingawalimbikitse kuganiziranso bwino za mmene iwowo akuchitira ntchito yolalikira. Ndipo akamaona chimwemwe chathu ndiponso chidwi chathu ndi anthu ena, zingawathandize kuona kufunika kosonyeza makhalidwe amenewa muutumiki wawo. Iwo akamaonanso kuti timayesetsa kugwiritsa ntchito Malemba, kupanga maulendo obwereza, ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo, angafunenso kuchita chimodzimodzi.
3. Kodi tingaphunzitse bwanji ophunzira Baibulo ndi chitsanzo chathu ndipo angapindule bwanji?
3 Tikamachititsa Maphunziro a Baibulo: Ophunzira Baibulo athu amaonetsetsa kwambiri zochita zathu. Mwachitsanzo, ngakhale titawafotokozera kuti n’zofunika kukonzekera phunzirolo, kuwerenga malemba, ndi kulemba mizere kunsi kwa mfundo zazikulu, iwowo angathe kuzindikira ngati ife sitichita zimenezi. (Aroma 2:21) Ngati ife timasunga nthawi yoyambira phunziro, iwonso sangafune kuti zochita zina zisokoneze phunziro lawo la Baibulo. Mosakayikira, iwo angaonenso kuti ndife ofunitsitsa kuchita utumiki wathu modzipereka ndiponso kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba. N’zomveka kuti ophunzira a anthu amene amatsatira kwambiri chitsanzo cha Yesu, nthawi zambiri amakhala alaliki achangu ndi obala zipatso.
4. Pamisonkhano ya mpingo, tingaphunzitse bwanji kudzera m’chitsanzo chathu?
4 Pamisonkhano ya Mpingo: Anthu onse amene ali mu mpingo wachikhristu amaphunzitsa pa misonkhano kudzera m’zitsanzo zawo. Anthu achidwi amene ayamba kubwera ku misonkhano amapindula akamaona zitsanzo zabwino za anthu ena mumpingo. Amaona kuti abale amakondana, ali pa umodzi wachikhristu, ndiponso amavala ndi kudzikongoletsa mwaulemu. (Sal. 133:1) Angaonenso chitsanzo chathu chopita ku misonkhano mokhulupirika komanso cha kulengeza poyera chikhulupiriro chathu pamisonkhanoyo. Mlendo wina pamisonkhano yathu anaona mtsikana wamng’ono amene anatha kupeza yekha lemba m’Baibulo lake mwamsanga ndipo ankatsatira bwino pamene lembalo linali kuwerengedwa. Chitsanzo chake chinalimbikitsa mlendoyo kupempha phunziro la Baibulo.
5. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kupeputsa kufunika kwa chitsanzo chathu?
5 Malemba amatilimbikitsa kutsanzira chitsanzo chabwino cha wina ndi mnzake. (Afil. 3:17; Aheb. 13:7) Choncho, tizikumbukira kuti tikamatsatira chitsanzo cha Yesu, anthu ena amaona ndipo amalimbikitsidwa. Pozindikira zimenezi, tiyeni titsatire mawu amene ali pa lemba la 1 Timoteyo 4:16: “Udziyang’anire wekha mosalekeza, ndi kusamalanso zimene umaphunzitsa.”