Ntchito Yosangalatsa Kwambiri
1. Kodi ndi ntchito yochiritsa mwauzimu iti imene ikuchitika masiku ano?
1 M’nthawi ya atumwi, zinali zosangalatsa kwambiri kuona anthu akuchiritsidwa mwakuthupi. (Luka 5:24-26) Masiku ano, timasangalala kugwira ntchito yochiritsa anthu mwauzimu. (Chiv. 22:1, 2, 17) Zimakhala zosangalatsa kwambiri tikamawerenga nkhani zofotokoza mmene Mawu a Yehova ndi mzimu wake zathandizira anthu ambiri kusintha moyo wawo. Koma chosangalatsa kwambiri ndi chakuti, tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito imeneyi mwa kuchititsa phunziro la Baibulo lopita patsogolo.
2. Kodi ndi zinthu ziti zimene timasangalala nazo tikamaphunzitsa munthu wina choonadi?
2 Kodi dzina la Mulungu ndani? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu azivutika? Kodi Ufumu wa Mulungu udzawachitira chiyani anthu? Timasangalala kuyankha mafunso amenewa komanso kuona wophunzira wathu akusangalala chifukwa chophunzira choonadi chimenechi. (Miy. 15:23; Luka 24:32) Wophunzira wathu akamapita patsogolo, angayambe kugwiritsa ntchito dzina la Yehova, angasinthe kavalidwe kake ndiponso mmene amadzikongoletsera, angasiye makhalidwe oipa komanso angayambe kulalikira kwa anthu ena. Ngati atapitirizabe kupita patsogolo mpaka kudzipereka ndi kubatizidwa, amakhala m’bale wathu komanso mnzathu wogwira naye ntchito. Kuona wophunzira wathu akuchita zimenezi kumatipatsa chimwemwe.—1 Ates. 2:19, 20.
3. Kodi tingatani kuti tiyambitse phunziro la Baibulo?
3 Kodi Mungagwire Nawo Ntchitoyi? Ngati mungakonde kugwira nawo ntchito yosangalatsayi, pemphani Yehova kuti akupatseni mwayi wokhala ndi phunziro la Baibulo. Ndiyeno muzichita zinthu zogwirizana ndi pemphero lanulo. (1 Yoh. 5:14) Muzilalikira pa nthawi komanso kumalo oti mungapeze anthu. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse kuyambitsa phunziro la Baibulo. (Mlal. 11:6) Mukapeza munthu wachidwi n’kubzala mbewu ya choonadi, muzibwererako kuti mukaithirire.—1 Akor. 3:6-9.
4. N’chifukwa chiyani tikufunika kuchita changu kuyambitsa maphunziro a Baibulo?
4 Pali anthu ambiri amene adakali ndi njala komanso ludzu la chilungamo. Kodi ndani angawathandize kuthetsa njala komanso ludzu lauzimu pophunzira nawo Baibulo? (Mat. 5:3, 6) Tiyeni tidzipereke kuti tithandize kumaliza ntchito yolalikira komanso yopanga ophunzira imeneyi nthawi yokolola isanathe.—Yes. 6:8.