Ndandanda ya Mlungu wa December 24
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 24
Nyimbo Na. 7 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 16 ndime 13-18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Zekariya 9-14 (Mph. 10)
Na. 1: Zekariya 11:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mulungu Amakhala Wofunitsitsa Kumva Mapemphero a Anthu Otani?—rs tsa. 339 ndime 3-tsa. 340 ndime 6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingagwiritse Ntchito Mfundo ya pa Miyambo 15:1 pa Nthawi Iti? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 30: Mmene Tingagwiritsire Ntchito Webusaiti Yathu Yovomerezeka. Nkhani yokambirana yochokera patsamba 3 mpaka 6. Pokambirana tsamba 4, chitani chitsanzo kwa mphindi zitatu chosonyeza banja likumaliza Kulambira kwa Pabanja. Bambo afunse banjalo nkhani imene angadzakambirane mlungu wotsatira ndipo ana asankhe kuti adzakambirane nkhani zopezeka pamalo amene alemba kuti “Achinyamata” pa Webusaiti yathu. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene akugwiritsira ntchito Webusaiti ya jw.org, kapena mmene akuganizira kuti angaigwiritse ntchito pophunzira paokha kapena pophunzira ndi banja lawo. Pokambirana tsamba 5, chitani chitsanzo kwa mphindi zitatu chosonyeza wofalitsa amene ali ndi foni yokhala ndi Intaneti akugwiritsa ntchito Webusaiti yathu kuyankha funso la mwininyumba lokhudza zikhulupiriro zathu. Pokambirana tsamba 6, chitani chitsanzo kwa mphindi zinayi chosonyeza wofalitsa akulankhula ndi munthu wachidwi amene akufuna kuwerenga m’chinenero chosiyana ndi cha wofalitsayo. Wofalitsa akuonetsa mwininyumbayo Webusaiti ya jw.org m’chinenero cha mwininyumbayo pogwiritsa ntchito foni yake kapena kompyuta ya mwininyumbayo ndipo akutsegula tsamba la kapepala kakuti Kudziwa Choonadi, m’chinenero chake ndipo akukambirana naye. Pemphani omvera kufotokoza mmene agwiritsira ntchito Webusaiti ya jw.org mu utumiki. Ngati kudera kwanuko mulibe mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti, tikukupemphani kuti mungofotokoza mfundo zikuluzikulu za m’zitsanzozi komanso m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero