Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira October 26, 2015.
Kodi lemba la 2 Mafumu 13:18, 19 likusonyeza bwanji kuti kutumikira Mulungu mwakhama komanso ndi mtima wonse n’kofunika? [Sept. 7, w10 4/15 tsa. 26 ndime 11]
Kodi ndani anali mfumu ya Isiraeli pa nthawi yomwe Yona anali mneneri, nanga zomwe zili pa 2 Mafumu 14:23-25 zikusonyeza bwanji kuti anagwira ntchito yake pa nthawi yovuta? [Sept. 7, w09 1/1 tsa. 25 ndime 4]
Kodi Ahazi anasonyeza bwanji kuti sanakhulupirire zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yesaya? Nanga ifeyo tiyenera kudzifunsa funso liti tikamafuna kusankha zochita? (2 Maf. 16:7) [Sept. 14, w13 11/15 tsa. 17 ndime 5]
Kodi ndi njira iti imene Rabisake anagwiritsa ntchito, yomwe imafanana ndi imene adani a anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito masiku ano? Nanga ndi khalidwe liti lomwe lingatithandize kukana kutsatira mfundo za anthuwa? (2 Maf. 18:22, 25) [Sept. 14, w10 7/15 tsa. 13 ndime 3-4]
Kodi chitsanzo cha Yosiya cha kudzichepetsa chingatithandize bwanji kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga komanso kuphunzira Baibulo? (2 Maf. 22:19, 20) [Sept. 21, w00 3/1 tsa. 30 ndime 2]
Kodi akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza zinthu ziti, zomwe zikusonyeza kuti mafumu awiri otchulidwa pa 2 Mafumu 25:27-30 analikodi? [Sept. 28, w12 6/1 tsa. 5 ndime 2-3]
Kodi Yabezi anapempha zinthu zitatu ziti kwa Yehova, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (1 Mbiri 4:9, 10) [Oct. 5, w10 10/1 tsa. 23]
Kodi zotsatira za nkhondo yotchulidwa pa 1 Mbiri 5:18-22 zingatilimbikitse bwanji kuti tipitirizebe kumenya nkhondo yathu yauzimu molimba mtima? [Oct. 12, w05 10/1 tsa. 9 ndime 7]
Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kumvetsa mfundo ya m’lamulo la Yehova pa nkhani ya kupatulika kwa magazi? Nanga tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Davidechi? (1 Mbiri 11:17-19) [Oct. 19, w12 11/15 tsa. 6 ndime 12-14]
Kodi Davide analephera kuchita chiyani pamene ankafuna kubweretsa likasa la pangano ku Yerusalemu? Nanga ifeyo tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? (1 Mbiri 15:13) [Oct. 26, w03 5/1 tsa. 10-11 ndime 11-13]