Kodi Mungatani Kuti Mawu a Mulungu Azikuthandizani pa Moyo Wanu?
Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kungatithandize kuti tikhale “ozikika mozama” komanso ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:6, 7) Koma kuti Mawu a Mulungu azititsogolera, tiyenera kuganizira kwambiri zimene tawerengazo komanso kuyesetsa kuzitsatira pa moyo wathu. (Aheb. 4:12; Yak. 1:22-25) Lemba la Yoswa 1:8 limatiuza zinthu zitatu zimene tiyenera kuchita. (1) Tiziwerenga Mawu Mulungu “usana ndi usiku.” (2) ‘Tizisinkhasinkha’ zomwe tawerengazo. Kuti zimenezi zitheke, tisamawerenge mothamanga koma tiziwerenga modekha kuti tizitha kuganizira zimene tikuwerengazo komanso mmene zinthu zinaliri pamene mawuwo ankalembedwa. (3) Tiziyesetsa ‘kutsatira zonse zolembedwamo.’ Tikamachita zinthu zitatu zimenezi, tidzakhala “ndi moyo wopambana” komanso tidzachita “zinthu mwanzeru.”