Ndandanda ya Mlungu wa November 2
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 2
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 21 ndime 1-8 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 16-20 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 17:15-27 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulalikira Mwakhama?—bt tsa. 152 ndime 12-13 (5 min.)
Na. 3: Yehova Amadana ndi Anthu Achinyengo—lv tsa. 168-169 ndime 15-17 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “ozikika mozama” ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’—Akol. 2:6, 7.
10 min: Zimene Munganene Pogawira Magazini a November. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani zitsanzo za ulalikizo.
10 min: Zofunika pampingo.
10 min: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Anthu Amene Mumaphunzira Nawo Baibulo Kuti Azikonda Kuphunzira Paokha.” Kenako apempheni kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo.
Nyimbo Na. 140 ndi Pemphero
Kumbukirani izi: Muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo. Ngati simungakwanitse, imbani nyimbo nambala 44.