Ndandanda ya Mlungu wa October 26
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 26
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 20 ndime 16-21 ndi bokosi patsamba 207 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 12-15 (8 min.)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (20 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “ozikika mozama” ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’—Akol. 2:6, 7.
10 min: Mabuku Ogawira M’mwezi wa November. Nkhani yokambirana. Limbikitsani omvera kuti m’mwezi umenewu, adzayesetse kugawira timapepala komanso buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kambiranani mwachidule mfundo zina zothandiza zimene zikupezeka m’nkhani yakuti, “Timapepala Tatsopano Anatikonza Bwino Kwambiri” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2014. Kenako chitani chitsanzo chogwirizana ndi gawo la mpingo wanu.
20 min: “Kodi Mungatani Kuti Mawu a Mulungu Azikuthandizani pa Moyo Wanu?” Nkhani. Mukamaliza kunena mawu anu oyamba, abale 4 awerenge mwa sewero lemba la Yona 1:4-15; 3:1-10 ndi 4:1-11. Abale amene awerenge mavesiwa muwadziwitsiretu. M’bale wina awerenge mawu a wofotokoza, wina awerenge mawu a Yehova, wina a Yona ndipo wina awerenge mawu a woyendetsa chombo. Abalewa ayenera kukonzekera bwino kuti adzakwanitsedi kuwerenga mwa sewero. Akamaliza kuwerenga, fotokozani zimene tikuphunzira pa mavesi amenewa. Fotokozaninso mmene kusinkhasinkha zomwe tawerenga m’Mawu a Mulungu kungatithandizire kupeza mfundo zomwe tingazigwiritse ntchito pa moyo wathu. Pomaliza limbikitsani mabanja kuti pa kulambira kwawo kwa pabanja, nawonso aziwerenga Baibulo mwa sewero ngati mmene abalewo achitira.
Nyimbo Na. 113 ndi Pemphero