Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 November tsamba 7
  • Achinyamata Musachedwe Kulowa ‘Pakhomo Lalikulu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata Musachedwe Kulowa ‘Pakhomo Lalikulu’
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Achinyamata—Kodi Zolinga Zanu Zauzimu Nzotani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 November tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Achinyamata Musachedwe Kulowa ‘Pakhomo Lalikulu’

Mukhoza kumaganiza kuti mudzakhala wachinyamata mpaka kalekale ndiponso kuti simudzakumana ndi mavuto amene amabwera chifukwa chokalamba. (Mlal. 12:1) Ngati ndinu wachinyamata, kodi mumaona kuti muli ndi nthawi yambiri moti mukhoza kudikira kaye musanakwaniritse zolinga zanu potumikira Yehova?

Kumbukirani kuti “zinthu zosayembekezereka zimagwera” tonsefe, kuphatikizapo achinyamata. (Mlal. 9:11) Komanso “simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.” (Yak. 4:14) Choncho musachedwe kukwaniritsa zolinga zanu potumikira Yehova popanda zifukwa zomveka. Lowani ‘pakhomo lalikulu la mwayi wautumiki’ lidakali lotseguka. (1 Akor. 16:9) Mukachita zimenezi, simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.

Zolinga zina zimene mungakhale nazo:

  • Mtsikana akulalikira m’chinenero china

    Kuphunzira chinenero china kuti muzilalikira anthu achinenerocho

  • Apainiya achinyamata ali mu utumiki

    Kuchita upainiya

  • Abale ndi alongo achinyamata akuchita nawo sukulu yophunzitsa Baibulo

    Kupita kusukulu yophunzitsa Baibulo

  • Abale ndi alongo achinyamata akugwira ntchito zomangamanga

    Kugwira nawo ntchito zomangamanga

  • Mnyamata akutumikira pa Beteli

    Kutumikira pa Beteli

  • Woyang’anira dera wachinyamata

    Kukhala woyang’anira dera

Lembani zolinga zanu:

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena