CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 47-51
Kumvera Yehova Kumabweretsa Madalitso
Yehova amatisonyeza mwachikondi ‘njira imene tiyenera kuyendamo’ n’cholinga choti tizikhala osangalala. Tikamamumvera zinthu zimatiyendera bwino.
“Mtendere . . . ngati mtsinje”
Yehova akulonjeza kuti tingakhale ndi mtendere wochuluka ndiponso wosatha ngati mtsinje womwe susiya kuyenda
“Chilungamo . . . ngati mafunde a m’nyanja”
Tidzatha kuchita zinthu zachilungamo zosawerengeka ngati mafunde a m’nyanja