February 13-19
YESAYA 52-57
Nyimbo Na. 148 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khristu Anavutika Chifukwa cha Ife”: (10 min.)
Yes. 53:3-5—Ananyozedwa ndiponso kuphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu (w09 1/15 26 ¶3-5)
Yes. 53:7, 8—Anapereka yekha moyo wake kuti atipulumutse (w09 1/15 27 ¶10)
Yes. 53:11, 12—Popeza kuti Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa, tili ndi mwayi woti Mulungu akhoza kutiona kuti ndife olungama (w09 1/15 28 ¶13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yes. 54:1—Kodi “mkazi wosabereka” amene akutchulidwa mu ulosiwu ndi ndani, nanga “ana” ake ndi ndani? (w06 3/15 11 ¶2)
Yes. 57:15—Kodi Yehova “amakhala” bwanji ndi anthu “opsinjika” ndiponso “onyozeka”? (w05 10/15 26 ¶3)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 57:1-11
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) bm—Siyani funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) bm 30-31—Siyani funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 13-14 ¶16-17—Ngati n’zotheka, chitsanzochi chikhale cha bambo akuphunzira ndi mwana wake.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikhulupirira Kwambiri Mlengi”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Zimene Achinyamata Anzanu Amanena—Kukhulupirira Kuti Kuli Mulungu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 17 ¶14-22 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 152
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero