Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 February tsamba 5
  • ‘Tikalengeze za Chaka cha Yehova Chokomera Anthu Mtima’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Tikalengeze za Chaka cha Yehova Chokomera Anthu Mtima’
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • “Mitengo ya Mulungu Yadzala ndi Madzi”
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mitengo Imene Imakhalitsa
    Nsanja ya Olonda—2001
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 February tsamba 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 58-62

‘Tikalengeze za Chaka cha Yehova Chokomera Anthu Mtima’

Sikuti “chaka cha Yehova chokomera anthu mtima” ndi chaka chenicheni

61:1, 2

  • Ndi nthawi imene Yehova amapatsa anthu ofatsa mwayi woti alandire ufulu

  • Kale, chaka chokomera anthu mtima chinayamba pamene Yesu anayamba utumiki wake mu 29 C.E. ndipo chinatha pa “tsiku lobwezera” la Yehova pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.

  • M’nthawi yathu ino, chaka chokomera anthu mtima chinayamba pamene Yesu anakhala mfumu kumwamba mu 1914 ndipo chidzatha pa chisautso chachikulu

Tchati chosonyeza chaka cha Yehova chokomera anthu mtima’ kuyambira mu 29 C.E. mpaka mu 70 C.E. komanso kuyambira mu 1914 mpaka pachisautso chachikulu

Yehova amadalitsa anthu ake powapatsa “mitengo ikuluikulu ya chilungamo”

61:3, 4

  • Nthawi zambiri, mitengo ikuluikulu kwambiri imapezeka m’nkhalango

  • Mizu ya mitengoyi imalukana ndipo zimenezi zimathandiza kuti mitengoyi isagwe kukakhala mphepo yamphamvu

  • Mitengo ikuluikuluyi imateteza timitengo ting’onoting’ono ku dzuwa ndipo masamba ake akayoyoka amawonjezera chonde m’nthaka

Anthu onse amumpingo wachikhristu wa padziko lonse amathandizidwa ndiponso kutetezedwa ndi “mitengo ikuluikulu ya chilungamo,” yomwe ikuimira Akhristu odzozedwa amene adakali padzikoli

Mitengo ikuluikulu yomwe ili ndi mizu yamphamvu imateteza timitengo ting’onoting’ono
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena