Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 February tsamba 4
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • “Ndilandira Mabuku Anuwo, Inunso Mukalandira Athu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 February tsamba 4
Mayi akumvetsera pamene a Mboni za Yehova akumugawira kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini

Yesu ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mat. 10:8) Timatsatira malangizowa chifukwa sitilipiritsa anthu tikawapatsa Baibulo kapena mabuku ena. (2 Akor. 2:17) Komabe tizikumbukira kuti mabukuwa ndi amtengo wapatali chifukwa amakhala ndi mfundo zochokera m’Mawu a Mulungu. Pamafunikanso ndalama zambiri komanso pamakhala ntchito yaikulu kuti mabukuwa asindikizidwe ndiponso kutumizidwa kumipingo padziko lonse. Choncho tiyenera kungotenga mabuku ndi magazini omwe tingagwiritsedi ntchito.

Tizichita zinthu mozindikira tikamagawira mabuku ndi magazini ngakhale pamene tikulalikira pamalo opezeka anthu ambiri. (Mat. 7:6) M’malo mongogawira zinthu kwa anthu amene akudutsa, ndi bwino kukambirana nawo kaye kuti tione ngati ali ndi chidwi. Mafunso amene ali m’bokosili angatithandize pa nkhaniyi. Ngati tingayankhe kuti inde pa funso limodzi, zingasonyeze kuti munthuyo ali ndi chidwi. Ngati tikukayikira kuti ali ndi chidwi, ndi bwino kungomupatsa kapepala. Komabe munthu akapempha magazini kapena buku linalake, tikhoza kumupatsa.​—Miy. 3:27, 28.

KODI MUNTHUYO . . .

  • akumvetsera mwachidwi pamene tikulankhula?

  • akunena maganizo ake?

  • wavomera kuti awerenga?

  • wapereka kangachepe?

  • akukhudzidwa ndi zimene tikuwerenga m’Baibulo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena