MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhala Okhulupirika Mukakumana ndi Mayesero
Onerani vidiyo yakuti Muzikhala Okhulupirika Ngati mmene Yesu Analili—Pamene Mukuyesedwa (imapezeka pamene palembedwa kuti BAIBULO), kenako yankhani mafunso otsatirawa:
Kodi Segi anakumana ndi mayesero otani amene akanamuchititsa kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu?
Kodi n’chiyani chinathandiza Segi kuti akhalebe wokhulupirika?
Kodi kukhulupirika kwake kunathandiza bwanji kuti Yehova alemekezedwe?