NKHANI YOPHUNZIRA 45
NYIMBO NA.111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
Zimene Mungachite Kuti Muzisangalalabe Mukamasamalira Wachibale Amene Akudwala Kapena Wachikulire
“Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu adzakolola akufuula mosangalala.”—SAL. 126:5.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tikambirana zimene anthu amene akusamalira wachibale amene akudwala kapena wachikulire angachite kuti azipirira mavuto amene akukumana nawo n’kumasangalalabe.
1-2. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene akusamalira ena? (Miyambo 19:17) (Onani zithunzi.)
M’BALE wina wa ku Korea dzina lake Jin-yeol anati: “Ine ndi mkazi wanga takhala m’banja zaka 32. Kwa zaka 5 zapitazo, ndakhala ndikusamalira mkazi wanga amene akudwala matenda aakulu moti amavutika kusuntha thupi lake. Mkazi wanga ndimamukonda komanso kumunyadira ndipo ndimasangalala kumusamalira. Usiku uliwonse amagona pabedi lakuchipatala kunyumba kwathu, ineyo ndimagona pambali pake ndipo timagwirana manja tikamagona.”
2 Kodi mukusamalira munthu amene akudwala monga makolo anu, mwamuna kapena mkazi wanu, mwana wanu kapena mnzanu? Ngati ndi choncho n’zosakayikitsa kuti mumayamikira mwayi womuthandiza komanso kumusonyeza chikondi. Ndipotu mukamasamalira munthu amene akudwala, mumasonyeza kuti mumakonda Yehova. (1 Tim. 5:4, 8; Yak. 1:27) Komabe mumakumana ndi mavuto amene anthu ena sangathe kuwaona. Nthawi zina mungamamve ngati palibe amene akumvetsa mavuto anu. Mungamamwetulire koma mukakhala panokha n’kumalira. (Sal. 6:6) Nthawi zonse Yehova amadziwa mavuto anu ngakhale kuti anthu ena sangadziwe. (Yerekezerani Ekisodo 3:7.) Misozi komanso kudzipereka kwanu ndi zamtengo wapatali kwa iye. (Sal. 56:8; 126:5) Iye amaona kuti chilichonse chimene mukuchita posamalira wodwala, mukuchitira iyeyo ndipo akulonjeza kuti adzakubwezerani.—Werengani Miyambo 19:17.
Kodi mukusamalira winawake? (Onani ndime 2)
3. Kodi Abulahamu ndi Sara ayenera kuti ankakumana ndi mavuto ati pamene ankasamalira Tera?
3 M’Baibulo muli nkhani za amuna ndi akazi amene ankasamalira ena. Taganizirani za Abulahamu ndi Sara. Pochoka ku Uri, bambo awo, a Tera, anali ndi zaka pafupifupi 200, koma anapita nawo limodzi. Iwo anayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 960 kukafika ku Harana. (Gen. 11:31, 32) N’zosakayikitsa kuti Abulahamu ndi Sara ankawakonda kwambiri a Tera, komatu sizinali zophweka kuti aziwasamalira pa ulendowu. Iwo ayenera kuti ankayenda pangamira kapena pabulu zomwe ziyenera kuti zinali zovuta kwa a Tera omwe anali achikulire. N’zodziwikiratu kuti Abulahamu ndi Sara ankatopa kwambiri. Koma Yehova ankawapatsa mphamvu zimene ankafunikira. Mofanana ndi Abulahamu ndi Sara, inunso Yehova adzakuthandizani ndi kukupatsani mphamvu.—Sal. 55:22.
4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
4 Kukhalabe wachimwemwe kungakuthandizeni kuti muzipirira mukamasamalira ena. (Miy. 15:13) Munthu wachimwemwe amakhalabe wosangalala posatengera mmene zinthu zilili. (Yak. 1:2, 3) Kodi mungatani kuti muzisangalala choncho? Njira imodzi ndi kudalira Yehova ndipo mungamupemphe kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wosangalala. Munkhaniyi tikambirana zinthu zinanso zimene anthu amene akusamalira ena angachite kuti azisangalalabe. Tionanso mmene ena angawathandizire. Koma choyamba tiyeni tione chifukwa chake anthu amene akusamalira ena akuyenera kumasangalalabe komanso zimene zingawapangitse kuti asamasangalale.
ZIMENE ZIMAPANGITSA KUTI AMENE AKUSAMALIRA ENA ASAMASANGALALE
5. N’chifukwa chiyani amene akusamalira ena amafunika kupitiriza kukhala osangalala?
5 Ngati amene akusamalira ena sakusangalala, zikhoza kumawafooketsa. (Miy. 24:10) Ndipotu akatopa zimakhala zovuta kuti azichita zinthu mokoma mtima komanso kuthandiza moyenera anthu amene akuwasamalira. Kodi ndi mavuto ati amene angapangitse anthu amene akusamalira ena kuti asamasangalale?
6. N’chifukwa chiyani anthu ena amene akusamalira achikulire kapena odwala amatopa kwambiri?
6 Anthu amene akusamalira ena amatha kutopa kwambiri. Mlongo wina dzina lake Leah ananena kuti: “Kusamalira wachibale kumapangitsa kuti ukhale ndi nkhawa ngakhale patsiku limene zinthu zayenda bwino. Tsiku likamatha ndimamva kuti ndatheratu moti palibenso chimene ndingachite. Nthawi zina sindikhala ndi mphamvu ngakhale zoyankhira meseji.” Ena zimawavuta kuti apume kapena kugona mokwanira. Mlongo wina dzina lake Inés ananena kuti: “Zimandivuta kuti ndizigona mokwanira. Nthawi zambiri ndimadzuka pambuyo pa maola awiri alionse kuti ndisamalire apongozi anga aakazi. Ndipo patenga zaka zambiri ine ndi mwamuna wanga tisanapite kuholide.” Anthu ena sakwanitsa kucheza ndi anzawo kapena kuchita zinthu zina zokhudza kutumikira Yehova chifukwa amafunika kusamalira achibale awo nthawi zonse. Zotsatira zake amamva kuti ali okhaokha ndipo sangathe kuchita zimene akufuna.
7. N’chifukwa chiyani anthu ena amene akusamalira ena amadziimba mlandu komanso amakhala achisoni?
7 Anthu amene akusamalira ena akhoza kumavutika ndi kudziimba mlandu komanso chisoni. Mlongo wina dzina lake Jessica ananena kuti: “Ndimavutika chifukwa cha zinthu zimene sindingakwanitse. Ndikati ndipume pang’ono ndimadziimba mlandu komanso ndimadziona ngati ndine wodzikonda.” Ena amadziimba mlandu chifukwa amaona kuti sakuchita zokwanira posamalira wachibale wawo, ndipotu nthawi zina amaona kuti sangakwanitse kupitiriza kuwasamalira. Komanso ena amadziimba mlandu chifukwa pa nthawi ina analankhula zinthu zimene zinakhumudwitsa munthu amene akumusamalira. (Yak. 3:2) Ndipo ena amamva chisoni chifukwa wachibale wawoyo akulephera kuchita zinthu zimene ankachita poyamba. Mlongo wina dzina lake Barbara anati: “Chinthu chimene chimandipweteka kwambiri ndi kuona munthu amene ndikumusamalira, matenda ake akukulirakulira tsiku ndi tsiku.”
8. Perekani chitsanzo cha mmene munthu amene akusamalira ena amamvera akayamikiridwa.
8 Anthu ena amene akusamalira ena amaona kuti sakuyamikiridwa. Zili choncho chifukwa anthu sawayamikira pantchito yaikulu imene amagwira komanso kudzipereka kwawo. Munthu amasangalala akayamikiridwa ngakhale ndi mawu ochepa. (1 Ates. 5:18) Mlongo wina dzina lake Melissa ananena kuti: “Nthawi zina ndimalira chifukwa chotopa komanso kukhumudwa. Koma anthu amene ndikuwasamalirawo akandiuza kuti, ‘Zikomo kwambiri chifukwa cha zimene mumandichitira,’ ndimasangalala. Mawu amenewa amandithandiza kuti tsiku lotsatira ndidzuke ndili wokonzeka komanso wofunitsitsa kuwasamalira.” M’bale wina dzina lake Ahmadu anafotokoza mmene amamvera akayamikiridwa. Iye ndi mkazi wake amasamalira mdzukulu wawo wamng’ono yemwe amakhala naye ndipo amadwala matenda akugwa. Iye ananena kuti: “Ngakhale kuti mwanayu sangamvetse zonse zimene timachita kuti tizimusamalira, mumtima mwanga mumadzaza chimwemwe akanena mawu osonyeza kuti amatiyamikira kapena akalemba mawu akuti, ‘Ndimakukondani.’”
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALABE
9. Kodi munthu amene akusamalira ena angatani kuti asamachite zinthu zimene sangakwanitse?
9 Muzichita zimene mungakwanitse. (Miy. 11:2) Tonsefe timakhala ndi nthawi komanso mphamvu zochepa. Choncho muzidziwa zimene mungakwanitse kuchita. Nthawi zina muzikana kuchita zinthu zina ndipo palibe vuto ndi zimenezo chifukwa zingasonyeze kuti ndinu wodzichepetsa. Ena akadzipereka kuti akuthandizeni muzivomera mosangalala. M’bale wina dzina lake Jay ananena kuti: “Anthufe timangokwanitsa kuchita zochepa pa nthawi imodzi. Kudziwa malire anu kungakuthandizeni kuti muzisangalalabe.”
10. N’chifukwa chiyani anthu amene akusamalira ena ayenera kukhala ozindikira? (Miyambo 19:11)
10 Muzikhala ozindikira. (Werengani Miyambo 19:11.) Mukakhala ozindikira zingakhale zosavuta kuti muzikhala odekha ena akakukhumudwitsani. Munthu wozindikira amamvetsa chimene chapangitsa munthu kuchita zinthu mwanjira inayake. Ndipotu matenda ena okhalitsa amapangitsa munthu kuchita zimene sachita nthawi zonse. (Mlal. 7:7) Mwachitsanzo, munthu amene ndi wachifundo komanso woganizira ena akhoza kuyamba kukonda zokangana komanso kulusa. Kapena akhoza kuyamba kuvuta, kusachedwa kupsa mtima kapena kumangodandaula zilizonse. Ngati mukusamalira munthu amene akudwala matenda aakulu, mungachite bwino kudziwa zambiri zokhudza matendawo. Zimenezi zingakuthandizeni kumvetsa kuti zimene wodwalayo akuchita, akupangitsa ndi matendawo osati kuti ndi mmene alili.—Miy. 14:29.
11. Kodi amene akusamalira ena amafunika kukhala ndi nthawi yochitira zinthu ziti zofunika tsiku lililonse? (Salimo 132:4, 5)
11 Muzikhala ndi nthawi yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Nthawi zina mungafunike kusiya zinthu zina kuti muchite zinthu zimene ndi “zofunikadi kwambiri.” (Afil. 1:10) Chimodzi mwa zinthu zimenezi ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mfumu Davide ankaona kuti kulambira Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. (Werengani Salimo 132:4, 5.) Inunso mungachite bwino kuti muzikhala ndi nthawi tsiku lililonse yowerenga Baibulo ndi kupemphera. Mlongo wina dzina lake Elisha ananena kuti: “Ndimakhalabe wosangalala chifukwa ndimapemphera komanso kuganizira mozama mfundo za m’buku la Salimo. Kupemphera kumandithandiza kwambiri. Ndimapemphera kambirimbiri pa tsiku kuti mtima wanga ukhale m’malo.”
12. N’chifukwa chiyani anthu amene akusamalira ena ayenera kukhala ndi nthawi yosamalira thanzi lawo?
12 Muzikhala ndi nthawi yosamalira thanzi lanu. Anthu amene amatanganidwa monga amene akusamalira ena zimawavuta kuti azidya chakudya chopatsa thanzi chifukwa amakhala ndi nthawi yochepa yogula komanso kukonza chakudya. Kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse n’kofunika kuti mukhale ndi thanzi komanso kuti musamakhale ndi nkhawa. Choncho muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yochepa imene muli nayo podya chakudya chopatsa thanzi komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. (Aef. 5:15, 16) Muziyesetsanso kuti muzigona mokwanira. (Mlal. 4:6) Kafukufuku amasonyeza kuti kugona kumathandiza kuti zinthu zoipa zizichoka mu ubongo. Nkhani ina ya zaumoyo yakuti “Mmene Kugona Kumachepetsera Nkhawa” inanena kuti: “Munthu akamagona mokwanira nkhawa zake zimachepa ndipo amakhala wokonzeka kulimbana ndi zokhumudwitsa.” Muzipezanso nthawi yochitira zosangalatsa. (Mlal. 8:15) Munthu wina amene amasamalira ena anafotokoza zimene zimamuthandiza kuti azisangalalabe. Iye ananena kuti: “Nyengo ikakhala bwino ndimatuluka kukawothera dzuwa komanso kamodzi pamwezi ndimakhala ndi tsiku lochita zosangalatsa ndi mnzanga.”
13. N’chifukwa chiyani kuseka kumathandiza? (Miyambo 17:22)
13 Muzichitako tinthabwala. (Werengani Miyambo 17:22; Mlal. 3:1, 4) Kuseka kumathandiza kuti tikhale ndi thanzi labwino komanso tisamakhale ndi nkhawa. Mukamasamalira ena si nthawi zonse pamene zinthu zimayenda mmene mukufunira. Koma mukapeza chinachake choseketsa pa zimene zachitikazo, zingakuthandizeni kuti musakhumudwe kwambiri. Ndipotu mukamaseka ndi munthu amene mukumusamalirayo zingakuthandizeni kuti muzigwirizana kwambiri.
14. Kodi kuuza mnzanu wapamtima mmene mukumvera kungakuthandizeni bwanji?
14 Muziuza mnzanu wapamtima nkhawa zanu. Ngakhale mutayesetsa kuti muzisangalala, nthawi zina mukhoza kumakhalabe ndi nkhawa. Choncho mungachite bwino kuuza mnzanu wapamtima amene angakumvetseni m’malo mokuweruzani. (Miy. 17:17) Iye angakumvetsereni komanso kukuuzani mawu olimbikitsa zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalalabe.—Miy. 12:25.
15. kKodi kuganizira zimene tikuyembekezera kungakuthandizeni bwanji kuti muzisangalala?
15 Muziganizira zimene mudzachitire limodzi m’Paradaiso. Muzikumbukira kuti ntchito imene mukugwira posamalira ena ndi yakanthawi ndipo si zimene Mulungu ankafuna. (2 Akor. 4:16-18) “Moyo weniweniwo” ukubwera. (1 Tim. 6:19) Mungamasangalale kwambiri mukamakambirana zimene mudzachitire limodzi m’Paradaiso. (Yes. 33:24; 65:21) Mlongo wina dzina lake Heather anati: “Nthawi zambiri ndimauza amene ndikumusamalira kuti pompano tizidzasoka, kuthamanga ndi kukwera njinga limodzi. Tizidzapanga buledi ndi kuphika chakudya choti amene aukitsidwa adzadye. Timathokoza Yehova potipatsa chiyembekezochi.”
MMENE ENA ANGATHANDIZIRE
16. Kodi tingathandize bwanji amene akusamalira ena mumpingo mwathu? (Onaninso chithunzi.)
16 Muzithandiza amene akusamalira ena kuti azichita zinthu zina. Abale ndi alongo amumpingo angadzipereke kuti asamalire wodwala m’malo mwa anthu amene amamusamalira. Zimenezi zingawathandize kuti apume komanso kuchita zinthu zina. (Agal. 6:2) Ena amakonza ndandanda ya mlungu uliwonse kuti azichita zimenezi. Mlongo wina dzina lake Natalya, amene amasamalira mwamuna wake amene anapanga sitiroko, anati: “M’bale wina mumpingo mwathu amabwera kamodzi kapena kawiri pa mlungu kudzacheza ndi mwamuna wanga. Amalowa muutumiki limodzi, kucheza komanso kuonera mafilimu limodzi. Nthawi imeneyi imakhala yosangalatsa kwa mwamuna wanga ndipo imandipatsa mpata wopuma ndi kuchita zinthu zina monga kukayenda.” Nthawi zina mungakasamalire wodwalayo usiku kuti amene amamusamalirayo agone mokwanira.
Kodi mungathandize bwanji amene akusamalira ena mumpingo mwanu? (Onani ndime 16)a
17. Kodi tingathandize bwanji amene amasamalira ena pa nthawi ya misonkhano?
17 Muzithandiza amene akusamalira ena pa nthawi ya misonkhano. Amene akusamalira ena sangapindule mokwanira ndi misonkhano ya mpingo, ya dera ndi yachigawo chifukwa amatanganidwa ndi kuthandiza anthu amene amawasamalira. Abale ndi alongo angadzipereke kuti akhale pafupi ndi wodwalayo pa nthawi yamisonkhano kapena pambali zina za misonkhanoyo. Ngati wachikulire kapena odwala sachoka panyumba, mungapite kwawo kukalumikiza misonkhanoyo kuti amene amawasamalira akasonkhane pamasom’pamaso.
18. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tingachitire amene akusamalira ena?
18 Muziyamikira ndi kupempherera amene amasamalira ena. Akulu angachite bwino kupanga maulendo aubusa nthawi ndi nthawi kwa anthu amenewa. (Miy. 27:23) Kaya zinthu zili bwanji, tonse tingamayamikire amene amasamalira ena nthawi ndi nthawi. Tingapempherenso kuti Yehova apitirizebe kuwapatsa mphamvu ndi kuwathandiza kuti azisangalala.—2 Akor. 1:11.
19. Kodi tikuyembekezera zinthu zotani?
19 Posachedwapa Yehova achotsa zopweteka ndi kupukuta misozi yonse. Matenda ndi imfa sizidzakhalaponso. (Chiv. 21:3, 4) “Munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala.” (Yes. 35:5, 6) Mavuto a ukalamba komanso ululu umene timamva tikamasamalira wodwala zidzakhala “zinthu zakale [zimene] sizidzakumbukiridwanso.” (Yes. 65:17) Ngakhale panopa pamene tikudikira malonjezowa, Yehova sangatisiye. Tikamapitiriza kumudalira kuti atipatse mphamvu iye adzatithandiza kuti tithe “kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.”—Akol. 1:11.
NYIMBO NA. 155 Chimwemwe Chosatha
a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Alongo awiri achitsikana apita kukaona mlongo wachikulire kuti amene amamusamalira akhale ndi nthawi yokawongola miyendo.