Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 19-tsamba 23 ndime 1
  • Baibulo Lolimba Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo Lolimba Kwambiri
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zikuto Zopindika
  • Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2014
  • Umboni wa Chikondi, Chikhulupiriro, ndi Kumvera
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Ntchito Yomasulira Buku Lofunika Kwambiri
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 19-tsamba 23 ndime 1
Chithunzi patsamba 19

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Baibulo Lolimba Kwambiri

A MBONI ZA YEHOVA amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambiri kuposa buku lina lililonse. Nthawi zonse, timaliphunzira komanso kuligwiritsa ntchito pophunzitsa ena za uthenga wabwino. (Mat. 24:14) Choncho, pokonza Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limene linatuluka mu 2013, abale anayesetsa kuti Baibuloli likhale lokongola komanso lolimba kwambiri.

Choncho abale ogwira ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill, anapita kukakambirana za mapulani osindikiza Baibuloli ndi mkulu wa kampani ina yopanga mabuku. Abalewo atamuuza mapulaniwo mkuluyo anati: “N’zosatheka kupanga Baibulo limene mukufunalo.” Iye ananenanso kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti Mabaibulo ambiri amakhala okongola koma osalimba. Amangokonzedwa m’njira yakuti azioneka bwino akasiyidwa patebulo kapena pashelefu basi.”

Mabaibulo ena a Dziko Latsopano amene anasindikizidwa m’mbuyomu anali osalimba. Choncho abale amene amagwira ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill anayamba kufufuza njira yoti asindikize Mabaibulo olimba zedi, amene sangawonongeke ngakhale atamagwiritsidwa ntchito mwakathithi m’nyengo iliyonse. Atafufuza, anasindikiza Mabaibulo angapo omwe anawatumiza m’madera osiyanasiyana, n’cholinga choti abale akawagwiritse ntchito mongoyeserera.

Patatha miyezi 6, anaitanitsa Mabaibulo aja, kuti awaonenso. Mabaibulowo anali okwana 1,690. Ndipotu panachitika zinthu zina zimene zinayesadi kulimba kwa Mabaibulowa. Mwachitsanzo, Baibulo lina linapondedwa ndi galimoto, lina linaiwalidwa panja n’kunyowa ndi mvula usiku wonse, ndipo lina linamira m’madzi osefukira.

Pa nthawi imene ntchito yoyesa Mabaibulo inali m’kati mu 2011, tinagula makina apamwamba kwambiri osindikizira mabuku komanso okonzera zikuto, omwe tinawaika ku Ebina m’dziko la Japan ndiponso ku Wallkill. Cholinga chake sichinali kungosindikiza Mabaibulo ambiri chabe nthawi imodzi, koma kuti Mabaibulo omwe angasindikizidwe m’malo awiri onsewa azioneka mofanana.

Zikuto Zopindika

Chithunzi patsamba 21

Poyamba zikuto zinkapindika

Chakumayambiriro kwa 2012, ntchito yosindikiza Mabaibulo a Dziko Latsopano amene anatulutsidwa mu 1984 inayambika ku Ebina, m’dziko la Japan komanso ku Wallkill. Mabaibulowa anapangidwa pogwiritsa ntchito zikuto zatsopano. Koma poikira zikuto, makina atsopanowa anagwiritsa ntchito guluu ndi kansalu kenakake, zinthu zomwe sanazigwiritse ntchito pa Mabaibulo omwe anayesedwa aja. Choncho kansalu kameneka ndi guluu zinachititsa kuti zikuto za Mabaibulowo zizipindika. Zonse zimene anthu ogwira ntchito yokonza Mabaibulowo anachita pofuna kuthana ndi vutoli zinakanika, moti ntchitoyi inaima.

Kampani ina inavomereza kuti nthawi zambiri zikuto zofewa zimapindika ndipo n’zovuta kuthana ndi vutoli. Koma abale sanasinthe kuti ayambe kusindikiza Mabaibulo a zikuto zolimba. Iwo anayesetsabe kufufuza njira yoti asindikizire Mabaibulo a zikuto zofewa, omwe sangawonongeke msanga. Patapita miyezi pafupifupi 4 akuyesera njira zosiyanasiyana, anapeza kansalu kena komanso guluu wamtundu wina. Iwo anatulukira zoti ngati atagwiritsa ntchito zinthu zimenezi, zikutozo zingakhale zokongola, zofewa ndiponso sizingapindike. Choncho ntchito yosindikiza Mabaibulo ija inayambikanso.

Chithunzi patsamba 22

Makina osindikizira mabuku ku Wallkill

Panakonzedwa zoti Baibulo la Dziko Latsopano, lomwe linakonzedwanso lidzatulutsidwe pa October 5, 2013, pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Pa August 9, 2013, mafailo a Baibulo anatumizidwa ku Wallkill ndi ku Ebina kudzera pa Intaneti kuti ntchito yosindikiza iyambike. Ndipo tsiku lotsatira, ntchitoyo inayamba. Abale anamaliza kusindikiza komanso kuikira chikuto Baibulo loyamba pa August 15. Kenako kwa masiku 7 otsatira, anthuwo anagwira ntchito mwakhama, masana ndi usiku. Ankafuna kuti asindikize, aike zikuto, ndiponso atumize Mabaibulo oposa 1,600,000, kuti munthu aliyense amene angakafike pamsonkhano wapachakawo alandire.

Mabaibulo atsopanowa ndi okongola komanso olimba zedi. Koma chomwe chikuchititsa kuti Mabaibulowa akhale apadera kwambiri ndi uthenga wake wosavuta kumva, womwe ungathandize anthu kudzapeza moyo wosatha. Patangotha tsiku limodzi chilandirireni Baibuloli, mlongo wina ku United States analemba kuti: “Panopa ndikumvetsa mawu a Mulungu mosavuta chifukwa ndikugwiritsa ntchito Baibulo latsopanoli.”

Ntchito Yomasulira Baibulo Pofika

pa August 31, 2014, Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa m’zilankhulo 124. Tchatichi chikusonyeza Mabaibulo amene anatuluka m’chaka chautumiki cha 2014.

DETI LIMENE MALO AMENE

ANATULUTSA ANATULUTSA

CHILANKHULO

BAIBULO LAKE

September 6, 2013

South Africa

Chiswati

Malemba Achigiriki

September 20, 2013

Paraguay

Chigarani

Malemba Achigiriki

January 17, 2014

Timor-Leste

Chitetamu

Malemba Achigiriki

July 5, 2014

Ukraine

Chiyukireniya

Baibulo Lathunthu

August 8, 2014

Estonia

Chiesitoniya

Baibulo Lathunthu

August 22, 2014

Britain

Chiperisiya

Malemba Achigiriki

August 22, 2014

Zambia

Chitonga

Baibulo Lathunthu

August 22, 2014

Zambia

Chikaonde

Baibulo Lathunthu

August 29, 2014

Kenya

Chiluo

Malemba Achigiriki

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena