Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 24-tsamba 27 ndime 1
  • Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • Mboni Za Yehova—Gulu la Dzinalo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Vidiyo Yatsopano Yothandiza Poyambitsa Maphunziro a Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Misonkhano Imene Anthu ‘Amamva ndi Kuona’
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • “Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 24-tsamba 27 ndime 1
Chithunzi patsamba 24

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova

Msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania wa nambala 129, unachitika Loweruka pa October 5, 2013. Anthu okwana 257,294 ochokera m’mayiko 21 anapezekapo kapena kuonerera kudzera pa Intaneti, pa nthawi yomwe msonkhanowu unkachitika. Kenako msonkhanowu anauonetsanso pa vidiyo. Anthu onse amene anaonera msonkhanowu anali ochokera m’mayiko 31 ndipo analipo 1,413,676. Msonkhano wapachakawu unali waukulu kwambiri kuposa misonkhano ina yonse imene inachitikapo m’mbuyomu.

Kuyambira m’ma 1920, tinayamba kulumikiza misonkhano yathu pa telefoni komanso kuiulutsa pa wailesi n’cholinga choti anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana azitha kumvetsera misonkhanoyo. Koma masiku ano kuli Intaneti ndipo ikuthandiza kuti anthu a m’mayiko ndi madera osiyanasiyana, ngakhale akutali kwambiri, azitha kuona ndi kumvetsera misonkhano pa nthawi imene ikuchitika kapena ikangotha kumene.

Panali ntchito yaikulu zedi yokonzekera kuti msonkhanowu udzaonetsedwe. Pa tsiku limene msonkhanowu unachitika komanso pa tsiku lotsatira, abale ena analumikiza makina oonetsera vidiyo pa Intaneti, ndipo ankayendetsa zonse ali ku ofesi ya ku Brooklyn, ku New York. Iwo anaonetsetsa kuti kwa masiku onse awiri, masana ndi usiku womwe, pali anthu amene akuyendetsa zinthu pamakina. Izi zinali choncho chifukwa msonkhanowu unaonetsedwa m’madera ndi mayiko osiyanasiyana ndipo nthawi inali yosiyananso kwambiri.

Mfundo Zachidule​—Malo Amene Anthu Ankaonera Vidiyo pa Intaneti

  • Pamalo amene pankachitikira mwambowu: Malo a Msonkhano ku Jersey City, U.S.A. Kunali anthu: 4,732

  • Kumene anthu anasonkhana ambiri: Perth, Australia. Kunali anthu: 7,186

  • Kumpoto kwenikweni: Fairbanks, Alaska, m’dziko la United States. Kunali anthu: 255

  • Kum’mwera kwenikweni: Invercargill, New Zealand. Kunali anthu: 190

  • Dera lakutali kwambiri: Perth, Australia. Pali mtunda wa makilomita pafupifupi 18,700 kuchokera ku Jersey City

Zimene Zimachitika Kuti Aonetse Msonkhano

  1. Pamakhala makamera ambirimbiri amene amajambula mavidiyo msonkhano uli mkati.

  2. Anthu oyendetsa zinthu pamakina amatha kuona mavidiyo onsewo nthawi imodzi ndipo amasankha vidiyo imene ili bwino kwambiri.

  3. Vidiyoyo amaitumiza m’kompyuta yaikulu.

  4. Makina ena amaikonza kuti ikhale ndi makolite osiyanasiyana.

  5. Vidiyoyo imadulidwa n’kukhala ya tizigawo ta masekondi 10 n’cholinga choti isavute kutumizidwa pa Intaneti.

  6. Tizigawoto timaikidwa pa Intaneti.

  7. Ndiyeno akatswiri oyendetsa zinthu pamakina amene ali m’madera osiyanasiyana omwe akufuna kuonera msonkhanowu amakhala ndi makina ena amene amapanga dawunilodi tizigawo ta vidiyo ija kuchokera pa Intaneti. Makinawo nthawi yomweyo amalumikiza tizigawoto ndipo vidiyoyo imayamba kuoneka bwinobwino.

  8. Anthu amaonera komanso kumvetsera bwinobwino msonkhano.

Chithunzi pamasamba 26, 27
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena