Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hdu nkhani 31
  • Misonkhano Imene Anthu ‘Amamva ndi Kuona’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Imene Anthu ‘Amamva ndi Kuona’
  • Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zipangizo za Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera Zogwirizana ndi Malo Alionse
  • Kupeza Zipangizo Komanso Kuzisamalira
  • Umboni kwa Anthu Ena Komanso Pulogalamu Yomveka Bwino
  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Zinthu Zimene Zinajambulidwa Kuti Tizimvetsera?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • “Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”
    Galamukani!—2016
  • Mboni Za Yehova—Gulu la Dzinalo
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
hdu nkhani 31
M’bale akuchuna mawu pamene anthu akuonera vidiyo pamasikilini akuluakulu.

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Misonkhano Imene Anthu ‘Amamva ndi Kuona’

1 JULY 2024

A Mboni za Yehova akhala akusonkhana pamisonkhano yachigawo kwa zaka zoposa 130 tsopano. Masiku ano, misonkhanoyi imakhala ndi nkhani zosiyanasiyana zokwana 40, nyimbo, mbali yofunsa mafunso anthu ena komanso mavidiyo. Kuti anthu apindule ndi kulimbikitsidwa ndi misonkhanoyi, ayenera ‘kumva ndi kuona’ zimene akuphunzirazo. (Luka 2:20) Kodi zopereka zanu zimagwiritsidwa ntchito bwanji kuti munthu aliyense apindule ndi misonkhanoyi mosatengera komwe amakhala?

Zipangizo za Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera Zogwirizana ndi Malo Alionse

M’mayiko ena, masitediyamu komanso maholo ambiri amakhala ndi zipangizo za mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera. Ndiye n’chifukwa chiyani timafunikanso kulumikiza zipangizo zathu tikachita lendi malo oterewa? David, yemwe amatumikira mu dipatimenti ya Broadcasting ku Likulu lathu lapadziko dziko lonse ananena kuti: “Pa malo ambiri omwe timapanga lendi, ndi malo ochepa chabe amene ali ndi zipangizo zothandiza anthu omwe asonkhana kumvetsera nkhani zimene anthu akukamba kwa maola 6. Mwachitsanzo, malo ochitirako masewera osiyanasiyana ali ndi zipangizo zongogwiritsa ntchito kwa nthawi yochepa monga kulengeza zinthu mwachidule komanso kuimbira nyimbo zazifupi. Masikilini awo amagwiritsidwa ntchito poonetsa zigoli, malonda komanso mmene anasewerera. Koma mosiyana ndi zimenezi, ife timafuna kuti anthu azionera mavidiyo ataliatali komanso kuti azimvetsera mosavuta nkhani zimene zikukambidwa papulatifomu.”

Malo alionse amene timachitirako misonkhano amakhala osiyana ndi anzake, choncho zipangizo za mavidiyo ndi zinthu zongomvetsera zimakonzedwa mogwirizana ndi mmene zinthu zilili kumalo alionse. Malo ochitirako misonkhano akasankhidwa, Madipatimenti Oulutsa Mawu ku ma ofesi anthambi amasankha mbali imene anthu adzakhale potengera chiwerengere cha anthu omwe akuyembekezereka kudzapezeka pamalowo. Kenako abale amaganizira malo amene masikirini adzaikidwe, kujambula malo amene adzaikidwe komanso kuwerengetsera kuchuluka kwa zipangizo zomwe zidzafunike n’cholinga choti aliyense azidzatha kuona ndi kumvetsera bwinobwino pulogalamu yonse.

Abale awiri a m’dipatimenti ya LBD akulumikiza zipangizo zoulutsira mawu pamsonkhano.

Abale a ku Dipatimenti Youlutsa Nkhani ndi Zinthu Zina (LBD) akutsatira pulani yomwe anapatsidwa

Ngati msonkhano ukufunika kumasuliridwa m’zilankhulo zingapo, pamakhalanso ntchito yaikulu polumikiza zipangizo zoulutsira mawu ndi mavidiyo. Omasulira amafunikira kumvetsera komanso kuonera pulogalamuyo kenako zimene akumasulira zimafunika kutumizidwa pa tchanelo cha anthu amene amamva chilankhulocho. Chifukwa cha mapulogalamu apadera apakompyuta, sizimavuta kuti mavidiyo azionetsedwa nthawi imodzi ku magulu onse a anthu omwe asonkhana ngakhale kuti anthu akumvetsera msonkhanowo m’zilankhulo zosiyanasiyana 8. David ananena kuti: “Pamakhala ntchito yaikulu kuti zipangizozi zilumikizidwe ndipo anthu amene amagwira ntchitoyi amafunika kuphunzitsidwa bwino.”

Maofesi a nthambi ali ndi zipangizo zoulutsira mawu zomwe amagwiritsa ntchito chaka chili chonse. Zikatere, abale amakonza zoti msonkhano wina ukatha, zipangizozi zizitumizidwa m’misonkhano inanso. Ofesi ya nthambi ya United States yokha imagwiritsa ntchito ndalama zopitirira madola 200,000a chaka chilichonse potumiza zipangizo zoulutsira msonkhano m’madera osiyanasiyana. Zimenezi zimathandiza kuti tichepetse ndalama zogulira ndi kukonzera zipangizo zina. Steven, yemwe anathandizira kuyang’anira zipangizo zoulutsira mawu ndi mavidiyo ku msonkhano wa ku Canada, ananena kuti: “Timu yathu inaonetsetsa kuti chipangizo chilichonse kuyambira manati, misomali, nthambo ndi china chilichonse zisamalidwe, kulongedzedwa komanso kusungidwa bwino pokonzekera msonkhano wotsatira.”

Kupeza Zipangizo Komanso Kuzisamalira

Nthawi zambiri timagula zipangizo zimene tikufunikira chifukwa kubwereka zipangizo kumakhala kodula kwambiri ndipo zipangizo zoterezi sizikhala zabwino kwenikweni. Panopa masikilini oonetsera mavidiyo omwe ndi aakulu mamita 5 x 3, amagulidwa ndalama zokwana madola 24,000 ndipo nthambo imodzi ya mamita 15 yolumikizira ku mayikolofoni, imagulidwa ndalama zokwana madola 20. Choncho zipangizozi zisanagulidwe, Dipatimenti Youlutsa Nkhani ndi Mapulogalamu Ena imagwira ntchito limodzi ndi dipatimenti Yogula Zinthu “nʼkuwerengera ndalama” zomwe zikufunikira. (Luka 14:28) Mwachitsanzo, amaganizira kuti kodi zipangizozi zidzathandiza anthu angati? Kodi njira yabwino ingakhale kugula zipangizo zatsopano? Kodi tili ndi malo okwanira osungiramo zipangizozi komanso anthu ongodzipereka omwe anaphunzitsidwa kuzikonza?

Nthawi ndi nthawi timakonza zipangizozi n’cholinga choti zigwiritsidwe ntchito kwa nthawi yaitali komanso kuti tisawononge zopereka za abale ndi alongo. Tikamazitumiza, timazilongedza m’mabokosi olimba bwino n’cholinga choti zisawonongeke ndipo mabokosiwa timawakonza pakafunika kutero.

Abale awiri akukonza zipangizo zoulutsira mawu ndi kuonetsera mavidiyo.

Kukonza zipangizo za mavidiyo ndi zinthu zongomvetsera kumathandiza kuti zigwiritsidwe ntchito nthawi yaitali

Umboni kwa Anthu Ena Komanso Pulogalamu Yomveka Bwino

Anthu omwe si a Mboni amagoma akaona mmene zinthu zongomvetsera komanso mavidiyo zimaulutsidwira pamisonkhano yathu. Mwachitsanzo, pamsonkhano wina, mmodzi mwa ogwira ntchito kukampani ina yaikulu kwambiri youlutsa mawu anagoma kwambiri ndi zinthu zapamwamba zomwe timapanga. Jonathan, yemwe amathandiza nawo kulumikiza zipangizozi pamisonkhano anati: “Bamboyu anachita chidwi kwambiri atazindikira kuti anthu onse amene ankagwira ntchitoyi anali ongodzipereka osati akatswiri. Munthuyo ananena kuti kampani yake ikanatenga masiku 5 kuti imalize kulumikiza zipangizozi, pomwe ife zinangotitengera tsiku limodzi ndi hafu.” Pamalo ena a msonkhano, bwana wa pamalopo ananena kuti: “Akatswiri a za nyimbo komanso mavidiyo akhala akubwera pamalo ano koma sindinaonepo anthu ogwira ntchito mwaluso ngati mmene mwagwiriramu.”

Abale ndi alongo ali pamsonkhano kusitediyamu ndipo akuonera mbali yofunsa mafunso pamasikilini akuluakulua.

Abale ndi alongo akumvetsera msonkhano

Kodi kukhala ndi zipangizo zoonetsera mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera pamsonkhano kwakuthandizani bwanji? N’kutheka kuti nanunso mukumva ngati David wa ku England yemwe anati: “Ndili ndi zaka 88 ndipo ndakhala ndikupita kumisonkhano kwa moyo wanga wonse. Koma kuposa kale lonse, panopa ndimamvetsera mwatcheru kwambiri ndikakhala pamsonkhano. Mavidiyo ooneka bwino kwambiriwa amachititsa kuti tisamaone nthawi kuchedwa ndipo uthenga wake umakhala womveka bwino kwambiri komanso wotsatirika.” Micheal wa ku Nigeria ananena kuti: “Popeza abale athu savutika kumvetsera wokamba nkhani akamalankhula kapena mavidiyo akamaonetsedwa, maganizo awo sayendayenda ndipo amatha kumvetsera mwatcheru msonkhano wonse.”

Chaka chino mukamakachita msonkhano wachigawo kapena wapadera wa mutu wakuti ‘Lalikirani Uthenga Wabwino,’ muzikaganiziranso zimene zinachitika kuti muthe kumvetsera komanso kuonera zinthu za pamsonkhanowo. Tikuthokoza kuti zopereka zanu, kuphatikizapo zomwe munapereka kudzera pa donate.jw.org, zathandiza kuti zimenezi zitheke. Zikomo kwambiri.

a Ndalama zonse za madola zimene zatchulidwa munkhaniyi ndi za ku America.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena