Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Zinthu Zimene Zinajambulidwa Kuti Tizimvetsera?
1. Kupatula pa kuwerenga, tchulani njira ina yomwe ingathandize anthu kudziwa choonadi.
1 Anthu ambiri amasangalala kuwerenga mawu olondola a choonadi pa webusaiti yathu. (Mlal. 12:10) Koma kodi inuyo mumamvetsera zinthu zimene zinajambulidwa? Tikamamvetsera zinthu zimenezi, timadziwanso zinthu zambiri. Koma kodi tingazigwiritse ntchito bwanji?
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zinthu zimene zinajambulidwa?
2 Patokha Komanso ndi Banja Lathu: Munthu amagwiritsa ntchito bwino nthawi ngati amamvetsera zinthu monga Baibulo, magazini kapena mabuku ena akakhala pa ulendo kapena akamachita zinthu zina. (Aef. 5:15, 16) Kulambira kwa Pabanja kukhoza kukhalanso kosangalatsa ngati mutamamvetsera zimene mukuphunzirazo uku mukutsatira m’mabuku anu. Kumvetsera pophunzira patokha kumathandizanso kuti tiziwerenga bwino komanso kuti tiphunzire chilankhulo.
3. Kodi ndi ndani angakonde zinthu zomvetsera m’gawo lanu?
3 Mu Utumiki: Anthu amene amati alibe nthawi yowerenga angalandire zinthu zomvetsera. Tikakumana ndi anthu achidwi koma achilankhulo china angasangalale kumva uthenga wa Ufumu mu chilankhulo “chimene anabadwa nacho.” (Mac. 2:6-8) M’madera ena anthu amakonda kwambiri zinthu zomvetsera. Mwachitsanzo, anthu a kum’mwera chakummawa kwa Asia amangouzana mbiri yawo ndipo saiwala. Anthu ambiri ku Africa amakonda kuuzana nthano.
4. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa kuti tithandize anthu mu utumiki?
4 Kodi zingatheke kuti mwininyumba amvere zinthu ngati zimenezi mu chilankhulo chake? Kodi mukuganizira winawake amene angakonde zinthu zomvetserazi kuti timutumizire? Nanga tingazichite dawunilodi n’kuziika pa CD kuti tizipereka kwa anthu pamodzi ndi buku kuti azikatsatira akamakamvetsera? Mukatumiza buku, kabuku kapena magazini kwa munthu muyenera kuperekera lipoti. Zinthu zomvetserazi zinajambulidwa kuti tizizigwiritsa ntchito patokha komanso polalikira.—1 Akor. 3:6.