Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 May tsamba 13
  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Zinthu Zimene Zinajambulidwa Kuti Tizimvetsera?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Gwiritsani Ntchito Webusaiti Yathu Yovomerezeka Pothandiza Munthu Wolankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kodi Munayamba Mwadzifunsapo?
    Galamukani!—2019
  • Chakudya pa Nthawi ya Njala
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 May tsamba 13
Zithunzi zosonyeza anthu akumvetsera Baibulo. 1. M’bale ali panja ndipo akumvetsera Baibulo pafoni yake. 2. Mayi ndi mwana wake wamng’ono akumvetsera Baibulo pachipangizo chawo kwinaku akutsatira mu Baibulo losindikizidwa. 3. Mlongo ali m’basi ndipo akumvetsera Baibulo pafoni yake.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?

Kodi Baibulo longomvetsera ndi chiyani? Ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lochita kujambula. Baibuloli likutulutsidwa mwapang’onopang’ono m’zilankhulo zambiri. Chosangalatsa kwambiri ndi Baibuloli n’chakuti limamveka ndi mawu osiyanasiyana a anthu opezeka m’Baibulo omwe analankhula. Mawuwa amawerengedwa ndi mzimu wa nkhaniyo komanso amawatsindika moyenera kuti uthenga wa m’Baibulo umveke molondola.

Kodi Baibulo longomvetserali likuthandiza bwanji anthu? Ambiri amene amamvetsera Baibuloli amalikonda chifukwa limawathandiza kuona kuti mawu a Mulungu ndi amoyo. Amaona kuti akamamvetsera mawu a anthu osiyanasiyana, zimawathandiza kuona m’maganizo mwawo zimene zinkachitika komanso amamvetsa bwino zimene zinalembedwa m’Baibulo. (Miy 4:5) Amaonanso kuti kumvetsera Baibuloli, kumawakhazika mtima pansi akakhala ndi nkhawa.​—Sl 94:19.

Kumva mawu a Mulungu akuwerengedwa mokweza kumakhala ndi mphamvu kwambiri. (2Mb 34:19-21) Ngati Baibulo longomvetsera lilipo lathunthu kapena mbali yake chabe m’chilankhulo chimene mumamva, mukhoza kukonza zoti muzilimvetsera nthawi zonse mukamachita zinthu zokhudza kulambira.

ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI ZIMENE ZINACHITIKA POJAMBULA BAIBULO LONGOMVETSERA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

N’chiyani chakuchititsani chidwi mukaona zimene zinachitika pojambula Baibulo longomvetsera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena