Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb16 tsamba 177
  • Mwambo wa Chikumbutso—Lachisanu pa 3 April, 2015

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwambo wa Chikumbutso—Lachisanu pa 3 April, 2015
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 1
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 22
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Ziwerengero Zonse za 2015
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
yb16 tsamba 177
Wa Mboni za Yehova akugawira kapepala koitanira kumwambo wa Chikumbutso

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Lachisanu pa 3 April, 2015

MIPINGO inayamba kugawira timapepala toitanira anthu kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu komanso kuti adzamvetsere nkhani yosonyeza mmene imfa imeneyi imatithandizira. Ntchitoyi inayamba Loweruka pa 7 March, 2015 ndipo inatenga milungu 4. Abale ndi alongo anaitanira anthu ambiri kumwambowu powapatsa timapepala, powaimbira foni komanso powalembera kalata. Kodi ntchito imene abale ndi alongo anagwirayi inathandizadi? Inde inathandiza kwambiri. Tikutero chifukwa pa tsiku la mwambo wapaderawu, Lachisanu pa 3 April, panabwera anthu okwana 19,862,783. Panopo abale ndi alongo akuyesetsa kuthandiza anthu achidwi amene anabwera pamwambowu kuti apitirizebe kusonkhana nafe. Zimenezi zingawathandize kuti azilambira Mulungu woona komanso kuti akhale naye pa ubwenzi, n’kudzalandira madalitso amene watikonzera m’tsogolomu.—Mika 4:2.

Abale ndi alongo anagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana poitanira anthu kumwambo wa Chikumbutso cha 2015 ndipo anthu 19,862,783 anapezeka pamwambowu
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena