Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 143
  • Kodi Kusuta Ndi Tchimo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kusuta Ndi Tchimo?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Baibulo limanenapo chilichonse pa nkhani yosuta chamba kapena kugwiritsa ntchito mankhwala aliwonse osokoneza bongo?
  • Ndudu za Fodya Kodi Mumazikana?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Mumadziwa Zotani pa Nkhani ya Fodya?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti N’kulakwa Kusuta Fodya?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 143
Akusuta fodya

Kodi Kusuta Ndi Tchimo?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silinena chilichonse pa nkhani ya kusutaa kapena kunenapo chilichonse pa njira zina zogwiritsira ntchito fodya. Komabe, lili ndi mfundo zosonyeza kuti Mulungu amadana ndi zinthu zomwe zimawononga moyo komanso kuipitsa thupi la munthu. Choncho ndi zodziwikiratu kuti kusuta ndi tchimo.

  • Kulemekeza moyo. Baibulo limati, “Mulungu . . . amapatsa anthu onse moyo, [ndi] mpweya.” (Machitidwe 17:24, 25) Popeza kuti moyo ndi mphatso imene Mulungu anatipatsa, sitiyenera kuchita chilichonse chomwe chingawononge moyo wathu. Kusuta ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa kuti anthu azifa ndi matenda omwe akanatha kuwapewa.

  • Kukonda anzathu. Baibulo limati, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Kusuta fodya anthu ena ali pomwepo, n’kupanda chikondi. Ndipotu anthu amene nthawi zambiri amapuma mpweya wa fodya chifukwa chokhala pafupi ndi munthu yemwe akusuta, amakhala pangozi yoti akhoza kudwala matenda ofanana ndi omwe anthu osutawo amavutika nawo.

  • Kufunitsitsa kukhala oyera. Baibulo limati, “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Limanenanso kuti, “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Munthu amene amasuta amaipitsa thupi lake ndipo sakhala woyera. Tikutero chifukwa choti mu fodya mumakhala poizoni yemwe amawononga thupi la munthu.

Kodi Baibulo limanenapo chilichonse pa nkhani yosuta chamba kapena kugwiritsa ntchito mankhwala aliwonse osokoneza bongo?

M’Baibulo mulibe mawu akuti chamba kapena dzina lililonse la mankhwala osokoneza bongo. Komabe muli mfundo zomveka bwino zosonyeza kuti kugwiritsa ntchito mankhwala a mtundu umenewu ndi kolakwika. Kuwonjezera pa mfundo zomwe tazitchula kale, taonaninso mfundo zotsatirazi:

  • Kukhala oganiza bwino. Baibulo limati, “Uzikonda Yehova Mulungu wako . . . ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37, 38) Limanenanso kuti, “Khalanibe oganiza bwino.” (1 Petulo 1:13) Munthu amalephera kuganiza bwinobwino akamagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndipo anthu ambiri omwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, sangathe kuchita chilichonse popanda mankhwalawo. Anthuwa amangokhalira kuganiza zosuta komanso mmene angapezere mankhwala ena m’malo moganizira zinthu zofunika kwambiri.​—Afilipi 4:8.

  • Kumvera malamulo a boma. Baibulo limati, ‘Muzimvera maboma ndiponso olamulira.’ (Tito 3:1) M’mayiko ena, boma limaika malamulo okhwima pa nkhani zokhudza kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mulungu amasangalala tikamamvera akuluakulu a bomawa.​—Aroma 13:1.

Mmene Fodya Amawonongera Thanzi la Munthu

Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse, linanena kuti chaka chilichonse anthu pafupifupi 6 miliyoni amafa chifukwa chosuta fodya. Ndipo chiwerengerochi chikukhudzanso anthu oposa 600,000 omwe sasuta koma amangopuma utsi wa fodyawo. N’zoonekeratu kuti kusuta kumawononga thanzi la osutawo komanso la anthu ena ongopuma nawo utsi wa fodyawo. Tiyeni tione mavuto ena omwe anthuwa amakumana nawo.

Khansa. Mu utsi wa fodya mumapezeka poizoni. Buku lina linanena kuti “anthu 90 pa 100 aliwonse omwe amapezeka ndi khansa ya m’mapapo, amapezeka ndi matendawa chifukwa chosuta fodya.” (Encyclopædia Britannica) Utsi wa fodya umayambitsa khansa ya m’ziwalo ngati mkamwa, pakhosi, chiwindi, kapamba komanso m’chikhodzodzo.

Kubanika. Utsi wa fodya umayambitsa mavuto ena ngati zibayo ndi chimfine. Ana omwe amapuma utsi wa fodya chifukwa chokhala pafupi ndi anthu omwe akusuta, amakhala pangozi yodwala chifuwa cha asima (mphumo), kutsokomola komanso mapapo awo amalephera kukula ndi kugwira ntchito bwino.

Matenda a mtima. Nthawi zambiri anthu amene amasuta amakhala pangozi yodwala matenda ofa ziwalo kapena a mtima. Utsi wa fodya uli ndi mpweya wapoizoni ndipo umadutsa m’mapapo mpaka umakafika m’mitsempha ya magazi. Zimenezi zimachititsa kuti mpweya wabwino wa oxygen usakhale wokwanira m’magazi. Zotsatira zake mtima umavutika kuti utumize mpweyawu kumbali zonse za thupi.

Mayi woyembekezera. Mayi woyembekezera akamasuta fodya, nthawi zambiri amabereka mwana wosakwanitsa masiku, wokhala ndi sikelo yotsika kwambiri kapenanso wobadwa ndi zilema zosiyanasiyana monga kupunduka milomo. Ana oterowo akhozanso kudwala matenda obanika ndipo nthawi zina amamwalira adakali akhanda.

a Mawu akuti kusuta akutanthauza kupuma mwadala utsi wa fodya kaya kudzera m’ndudu kapena m’mapaipi. Ndipo mfundo za m’Baibulo zimagwiranso ntchito kwa anthu amene amachita kutafuna fodya, kununkhiza kapena kwa amene amagwiritsa ntchito mankhwala aliwonse osokoneza bongo..

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena