Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 6/8 tsamba 3-4
  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kututa Kowoneka kwa Kuipitsa
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa
    Galamukani!—1988
  • Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!
    Galamukani!—1988
  • Bwenzi Kukanakhala Mpweya Wabwino!
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 6/8 tsamba 3-4

Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa

PAMENE katswiri wodziŵa kung’ung’udza nyimbo Tom Lehrer anayimba ponena za kuipitsa kubwerera m’mbuyo m’ma 1960 ndi kuchenjeza alendo opita ku United States kusamwa madzi kapena kupuma mpweya, chinatanthauzidwa kukhala choseketsa.

Masiku ano palibe aliyense amene akuseka. Ndiko nkomwe, kuipitsa sikuli nkhani yoseketsa. Mpweya wathu ukuipitsidwa ndi zotulutsidwa zotenthetsa ndi maindastri, utsi wochokera ku mainjini, ndi kugwa kwa zidutswa za radioactive; madzi athu ndi mankhwala ndi kutaika kwa mafuta; ndipo nthaka yathu ndi mvula ya acid ndi zotaidwa zopanda ntchito zokhala ndi ululu. Panali nthaŵi pamene maina onga Chernobyl, Love Canal, Amoco Cadiz, ndi Bhopal sankakumanizidwa ndi nkhope zozizwitsidwa. Tsopano iwo amaitanira kuyang’ana kodandaula. Kutsungula kwasokera, kukuwopsyeza mamiliyoni a anthu ndi masinthidwe oipa a matenda okhalitsa kapena imfa ya mwadzidzidzi.

Kuipitsa kuli mwapadera kochititsa mantha chifukwa mochulukira kaŵirikaŵiri iko sikumawonedwa. Mpweya ungawoneke kukhala wabwino ndi woyera ndipo komabe ungakhale ndi zidutswa za radioactive; chakudya ndi madzi zingawoneke zabwino ndipo komabe zingakhale zodzaza ndi mankhwala a ululu! Kunena zowona, kuipitsa kuli kaŵirikaŵiri wakupha wosawoneka.

Kututa Kowoneka kwa Kuipitsa

Ngakhale kuti kuipitsa kungakhale kosawaoneka, kututa kwake kwakupha sikuli tero. Mungakuwone kulikonse kumene mungayang’ane: anthu akufa ndi kansa ndi matenda a dongosolo lopumira; nyumba zowonongedwa ndi malo a zikumbutso; kuwonongedwa kwa mbali yokulira ya moyo wa nyama ndi zomera; mitsinje yopanda nsomba; nkhalango zakufa ndi zomafa.

Mbali ina tsopano yapanga kuwonekera kwake, mwachiwonekere ikumasunga dzina lotchuka la kuipitsa. Asayansi apeza chiboo mu mpweya wochinjiriza chilengewe m’mlengalenga wokuta dziko lapansi. Ndipo icho chikukulirakulirabe. Ena akudzimva kuti kuipitsa kwa ululu wa mankhwala akupha tizirombo otsekeredwa m’chitini kuli mwachiwonekere chochitika, chotulukapo kuchokera ku kugwiritsira ntchito kopambanitsa kwa kuwaza mankhwala akupha tizirombo otsekeredwa m’chitini. Kodi kuwononga kwa mpweya wa mumlengalenga wochinjiriza chilengedwe umenewu, womwe umathandizira kuziziritsa mbaliwali zovulaza zochokera kumwamba, kudzapangitsa kuwonjezeka kwa kansa ya khungu? Kapena mwinamwake kupangitsa ngakhale chinachake choipirapo?

Kuipitsa kwafikira ku mlingo wa ngozi chotere kotero kuti chinachake chifunikira kuchitidwa—ndipo mwamsanga—ngati ngozi ya dziko lonse idzafunikira kupewedwa. Kugalamuka kokulira kwa kuipa kwa vutolo kwatsogolera ku kupangidwa kwa magulu odziŵa za maunansi a zotizungulira ndipo kwakhoza ngakhale kufulumiza zipani zatsopano za ndale zadziko zomwe zikupita m’malo a mphamvu. Mu Federal Republic of Germany, mwachitsanzo, munthu wa chiyambi chodziŵa za maunansi a zotizungulira ndipo wopatsidwa moyenerera dzina lakuti Greens anapeza 8.3 peresenti ya kusankhidwa kwa lamulo kwa voti yotchuka pa January 1987.

Kodi mwinamwake tikuyembekeza kuti kudera nkhaŵa kwa anthu kungakhoze mopita patsogolo kusinthidwira m’kugwira ntchito kwenikweni kokhoza kuchotsa kuipitsa pa pulaneti yathu, wakupha wosawoneka? Kodi tingadzichinjirize ife eni mwaumwini kuchoka ku zopangidwa zake zakupha?

[Bokosi patsamba 4]

Pulaneti Yathu Yoipitsidwa

Brazil: “Anthu omwe amakhala [mu Cubatão] amakutcha iko ‘Chigwa cha Imfa.’ . . . Mitengo ndi nthaka ziri zopanda moyo ndipo, m’chiŵerengero chomawonjezereka, ana akubadwa akufa kapena kumwalira. Chomwe chiri chamoyo chiri kuipitsa.”—Latin America Daily Post.

China: “Yochulukira ya mizinda ya kumpoto koma cha kummawa kwa China [imavutika] ndi kuipitsidwa kwa mpweya koipa kwambiri chakuti pofika madzulo kwambiri kokha okhala kumaloko opirira angakhoze kuyenda m’makwalala popanda kuwononga mapapo ndi kutulutsa misozi.”—Time.

Denmark: “Kokha kutsatizana kwa kuzizira, chirimwe cha mphepo chokhala ndi mkuntho wa kaŵirikaŵiri wochokera ku mpoto koma cha kumadzulo ungakhoze kupulumutsa doko la Danish kuchokera ku tsoka la malo otizungulira. . . . [M’malo amodzi, chifukwa cha] kusoweka kwa mpweya womwe timalowetsa mkati, nsomba ndi zamoyo za m’nyanja sizidzakhoza kupulumuka.”—Basler Zeitung.

Federal Republic of Germany: “Msanganizo wa ululu unathiridwa mu Rhine [kuchokera ku nyumba yosungiramo za mankhwala a moto pafupi ndi Basel, Switzerland], ukumapha nyengo ya zaka 15 ya kuchira kwa Rhine [ndi matani a nsomba]. . . . Ngozi ya ku Sandoz yapangitsa kuvulazika koipa ku malo otizungulira kufika ku makilomita 280 a Rhine.”—Der Spiegel.

Soviet Union: “Kuchititsidwa kwa ngozi mu Chernobyl . . . kunali posinthira pa zinthu m’mbiri ya kutsungula kwamakono. Ndipo inali ngozi yomwe mofalikira idzatiyambukira kwa mazana angapo. . . . Ndikuti anthu a ku Europe 570 miliyoni, m’mlingo wosiyanasiyana, anali, ali, ndipo adzapitirizabe kuwunikiridwa ku zidutswa zowonjezereka zakupha kwa zaka 300 ndipo adzakhala ndi zotulukapo zosawonedweratu.”—Psychologie Heute.

United States: “Asayansi . . . [akhoza] kulongosola kudera nkhaŵa kwatsopano komwe mvula ya acid, m’kuwonjezera ku kupha nyanja, yaipitsa kukula kwa nkhalango ndipo mothekera kudzetsa ngozi ku umoyo wa anthu mwa kuipitsa madzi akumwa.”—Maclean’s.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena