Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 6/8 tsamba 8-10
  • Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wakupha Wopanda Chifundo Aletsedwa Pomalizira Pake!
  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa
    Galamukani!—1988
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kupeza Njira Yabwino
    Galamukani!—1996
  • Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 6/8 tsamba 8-10

Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!

“MAPETO sangapewedwe kuti malo otizungulira ali opanda chisungiko mowonjezereka kuposa mmene afunikira kukhalira.” Ngati mawu amenewa anali owona kumbuyoko mu 1970 pamene mkonzi wake wotchuka G. R. Taylor anawalemba, iwo ali otero mowonjezereka chotani nanga lerolino! Mwaŵi wakuti munthu angachotsepo zokhumudwitsa zomwe zaima m’njira ya yankho losatha ku kuipitsa ukuzimiririka. Chowonadi chenicheni chiri chakuti anthu afunikira chithandizo chaumulungu.

Pamene Mulungu analenga anthu, iye anawalangiza iwo kusamalira kaamba ka dziko lapansi. (Genesis 1:28; 2:15) M’malomwake, m’kusadziŵa ndi kudzikuza, iwo aliipitsa ilo. Koma Mlengi walonjeza “kuwononga owononga dziko.” Mwamsanga oipitsa mwadala a dziko lapansi atabweretsedwa ku chiwonongeko ndi boma la Ufumu wa Mulungu, zochititsa kuipitsa zingakhoze kuchotsedwa.—Chivumbulutso 11:18.

Kupereka malingaliro a mmene ichi chidzakwaniritsidwira, Yesaya 11:9 yanena kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza mu phiri langa lonse loyera chifukwa kuti dziko lapansi lizadzala ndi odziŵa Yehova.” Mosakaikira Mlengi adzaphunzitsa anthu chirichonse ponena zadziko lapansi ndi malo ake olizungulira omwe iwo afunikira kudziŵa m’malo mwakuti achite monga olisamalira achikondi omwe adzapewa kuliipitsa kulikonse ilo kapena kupangitsa kuwononga kulikonse.

Mulungu adzabwezeretsa munthu ku ungwiro, mkhalidwe mu umene analengera munthu woyamba. Malingaliro aungwiro, odzala ndi chidziŵitso cholongosoka ndi olamuliridwa ndi kuŵeruza kwa ungwiro, sadzakhoterera ku kuphophonya kwa umunthu. Kusasamala ndi zolephera zina za thupi monga mmene tsopano tikuzidziŵira izo zidzachotsedwa. Kuchinjiriza kwa umulungu kudzachotsapo ngozi zazing’ono. Ngakhale zopangapanga zidzasungidwa m’kulamulira kwangwiro.—Yerekezani ndi Marko 4:39.

“Chidziŵitso cha Yehova” chidzaikanso mwa anthu kusamalira kwachikondi kaamba ka ena ndi kulemekeza ndi kuyamikira kaamba ka chilengedwe cha Mulungu chomwe chidzaletsa aliyense payekha kufuna kuipitsa. M’chenicheni, icho chayamba kale kutulutsa anthu a mtundu wotere, anthu omwe achotsa “umunthu wakale ndi zochitachita zake” ndi omwe akukalamira kukhala ndi moyo mwa malamulo a Chikristu. “Uzikonda m’nzako monga udzikonda mwini,” mwachitsanzo. Kapena, “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma.” China: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za m’nzake.”—Akolose 3:9, 10; Marko 12:31; Ahebri 13:5; 1 Akorinto 10:24.

Wakupha Wopanda Chifundo Aletsedwa Pomalizira Pake!

Kufikira tsopano palibe kutchulidwa kulikonse komwe kwapangidwa kwa wochirikiza wamkulu wa kuipitsa. Iye ali wakupha wosawoneka, Mdani wamkulu wa Mulungu, Mdyerekezi. (Yohane 8:44; Ahebri 2:14) Malingaliro opotozeka a Satana ali okhoterera pa kulingalira njira za kugwetsera Mulungu ndi kuwononga chilengedwe cha Mulungu. Dziko lapansi loipitsidwa ndi lowonongedwa silimabweretsa kulemekeza kwa Mlengi, yemwe analilinganiza ilo kuti likhale loyera mowonekera ndi la udongo; kapena ngakhale anthu omwe analengedwa mu chifaniziro cha Mulungu omwe amalola Mdyerekezi kuwasokeretsa iwo m’kuchita zikhoterero zake. (Aefeso 2:2) Malinga ngati Satana apitirizabe kukhalapo, kumenyera molimbana ndi kuipitsa kudzapitirizabe kulephera. Koma yembekezani!

Lonjezo la Mulungu liri lakuti: “Ndipo ndinawona mngelo akutsika kumwamba . . . ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi . . . kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:1-3) Mngeloyo ali Ambuye Yesu Kristu, yemwe adzamanga Satana ndipo kenaka kuchotsapo pa chilengedwe kuyambukira kwake kwa zaka chikwi, chotero kuchotsapo chokhumudwitsa chachikulu pa dziko lopanda kuipitsidwa.

Mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu, pulaneti ya Dziko Lapansi idzakhala ndi nthaŵi yokwanira ya kuchira kuchokera ku zolemetsa za kuipitsa. Ufumu wa Mulungu ungakhoze kuchotsa mopepuka kuvulaza komwe kwachitidwa kale. Pa nthaŵi ino, m’kayang’anidwe ka zotutidwa zakupha za kuipitsa, ife tingakhoze mwanzeru kudzichinjiriza ife eni ku zotopetsa zake monga mmene tingathere. Ndithudi, njira za kuchitira ichi ziri ndi polekezera, ndipo chiri chovuta kutenga langizo losamalitsa la Tom Lehrer lakuti: ‘Musamwe madzi ndipo musapume mpweya.’ Koma njira zina zingatengedwe. (Onani bokosi pa tsamba 9.)

Pamene titenga njira zoterozo, tiyenera kukumbukira kuti kuchinjiriza kwabwino kwambiri molimbana ndi zoipitsa zotopetsa kuli kuika chikhulupiriro chathu mu Ufumu wa Mulungu. Iwo wokha udzathetsa mavuto kosatha. Chaka chatha Mboni za Yehova zinatsogoza maphunziro a Baibulo oposa pa mamiliyoni atatu mlungu ndi mlungu kwa anthu ofunitsitsa kuphunzira zifuno za Mulungu za kukhala m’dziko lathu latsopano lopanda zoipitsa. Kodi mungafune kutenga mwaŵi wa utumiki umenewu, womwe ukuchitidwa popanda malipiro?

Ndi chisangalalo chotani nanga kudziŵa kuti kumenyera kwathu molimbana ndi kuipitsa—wakupha wopanda chifundo—kudzatha posachedwapa! Mofananamo kudzakhala tero kumenyera kwathu kwa kuchita ndi zotutidwa zodzetsa imfa za kuipitsa. Kuipitsa ndi wochirikiza wake wamkulu, Satana Mdyerekezi, onsewo akupha, kudzaletsedwa potsirizira pake—kuferatu m’malo awo!

[Bokosi patsamba 9]

Chitetezo Chaumwini Molimbana ndi Kuipitsa

◼ Samalirani umoyo wanu wachisawawa, mukumachita maseŵera olimbitsa thupi okwanira ndi kupuma pa maziko okhazikika

◼ Pewani kusuta, kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa ndi anamgoneka, kapena zizoloŵezi zina zomwe zimatopetsa dongosolo la kuchinjiriza la thupi

◼ Pewani kuwunikiridwa kopambanitsa ku dzuŵa

◼ Gwiritsirani ntchito zochotsa zinyalala m’madzi ngati ngozi ya kuipitsidwa kwa madzi iripo m’dera lanu

◼ Pewani monga mmene kungathekere zakudya zomwe ziri ndi zomwereketsa za mankhwala

◼ Pewani mankhwala osayenera, popeza kuti chifupifupi mankhwala aliwonse ali ndi ziyambukiro za pambali

◼ Gwirizanani ndi miyezo ya lamulo yolinganizidwa kuthetsa kuipitsa

[Chithunzi patsamba 10]

Sipadzakhala chirichonse chonyenga ponena zadziko latsopano la Mulungu lokongola lopanda kuipitsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena