Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 6/8 tsamba 5-8
  • Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Chirichonse Chikukula”
  • Chidziŵitso Chosakwanira
  • Zolephera ndi Polekezera pa Anthu
  • Zoperewera Zowonjezereka Zowopsya
  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa
    Galamukani!—1988
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!
    Galamukani!—1988
  • Kodi Zatiyendera Bwanji Pankhani Yoteteza Chilengedwe?
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 6/8 tsamba 5-8

Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa

OH, INDE, ena a ife tiri ndi mawailesi a kanema, microwave ovens, ndi makompyuta aumwini. Koma kodi mpweya wathu watsopano uli kuti, zakudya zaudongo, ndi madzi audongo? Nchifukwa ninji kukhoza kwa nzeru za zopangapanga kwa kutumiza munthu ku mwezi kukuwonekera kukhala kosakhoza kutipatsa ife zinthu zimenezi, zofunika zathu zazikulu? Nchifukwa ninji, m’chenicheni, unyinji wa kupha kwa kuipitsa ukuchulukirachulukirabe?

“Chirichonse Chikukula”

Profesa Kurt Hamerak, akumalemba m’magazini ya sayansi ya ku Germany, anadzinenera kuti “mavuto a malo otizungulira onse ali kwenikweni ochititsidwa ndi kukula, pamwamba pa zonse ndi kukula kwa chiŵerengero cha anthu chosayembekezereka kofulumira.” Chiŵerengero cha anthu cha dziko chawirikiza kuposa kaŵiri kokha chiyambire 1950. M’kuwonjezerapo, tikukhala m’chimene phunziro la Mitundu Yogwirizana imachitcha “dziko la mizinda yophulika.” Podzafika chaka cha 2000, kuyerekezedwa kwa atatu mwa anthu anayi okhala m’malo otukuka adzakhala m’mbali za ku matauni. Pamene unyinji wa chiŵerengero cha anthu ukuwonjezeka, kumateronso kuthekera kwa kuipitsa.

Monga mmene paliri kukula m’chiŵerengero cha anthu omwe akufuna zinthu zomwe nzeru zowonjezereka ndi zopangapanga zimazipanga kukhalako, zotulutsidwa za mu maindastri ndi zamalonda nazonso zimakula. Ichi chimatanthauza mafakitale atsopano ndi malo opangirako zamankhwala—magwero atsopano a kuipitsa. Ndipo izi pambuyo pake zimafunikira magetsi, chotero malo a magetsi atsopano afunikira kumangidwa. Kuzungulira dziko lonse, chifupifupi 400 a iwo ali ochirikiza nyukliya.

Ndiponso womwe ukukula uli unyinji wa nthaŵi ya pambali yomwe anthu ali nayo. Iyi imawapatsa iwo nthaŵi yowonjezereka ndi mwaŵi wa kuchezera mbali ya dziko, nthaŵi zambiri kuipitsa mtunda, mpweya, ndi madzi, limodzinso ndi kuika m’ngozi zomera ndi umoyo wa nyama m’dongosolo lawo.

M’malo mwa kuchinjiriza kuipitsa, kutsungula kwamakono m’chenicheni kwathandiza kupanga iko mwa kuchirikiza kawonedwe ka zinthu za kuthupi komwe kwenikeni kali dalitso losakanizika. Anthu a mathayo ochulukira akuchenjeza tsopano kuti kukula kosaletsedwa kukutsogolera ku kuwonongeka. G. R. Taylor mu The Doomsday Book watsiriza kuti: “Kufika tsopano chawoneka kuti kawonedwe ka zinthu za kuthupi . . . kayenera kugonjetsa. Mwadzidzidzi chayamba kuwonekera kuti sikangagonjetse.”

Inde, “chirichonse chikukula,” watero profesa Hamerak, “kuphatikizapo mavuto.” Koma pali zifukwa zowonekera zowonjezereka zina pa zimene kumenyera molimbana ndi kuipitsa sikukuchitikira bwino.

Chidziŵitso Chosakwanira

Mwachitsanzo, “mogwira ntchito palibe chirichonse” chomwe chikudziŵika, latero The Doomsday Book, “ponena za kusokoneza komwe kukuchitika pakati pa zoipitsa zosiyanasiyana zomwe ziripo pa nthaŵi imodzimodziyo.” Ndiponso chosatsimikizirika chiri unyinji wa zinthu za ululu kapena zidutswa zakupha zimene munthu angawunikiridweko asanavutike ndi ziyambukiro zowopsya. Katswiri wa za ululu L. Horst Grimme wa ku Yunivesite ya Bremen wadzinenera kuti “sichiri chotheka kulongosola ukulu wa ngozi yomwe imabuka m’kupanga, kugwiritsira ntchito, ndi kugawira kwa zoipitsa.” Iye akudzimva kuti kulibe njira iriyonse ya kudziŵira kwenikweni pa mlingo umene choipitsa chimadutsa mzere pakati pa kusavulaza ndi kuvulaza. “M’zitsanzo zambiri,” iye watero, “akatswiri ali kokha osakwanira mwa chidziŵitso kukhoza kutsimikizira milingo yolandirika.” Mowonjezera, kufufuza kuli kwa posachedwapa kotero kuti palibe aliyense yemwe akudziŵa ndithudi chimene ziyambukiro za nyengo ya nthaŵi yaitali za “mlingo wolandirika” zingakhale nazo.

Kodzetsanso funso kuli mmene angawonongere zotaidwa za ululu. Iri si vuto laling’ono chifukwa chakuti unyinji wa zotaidwa za ngozi zopangidwa ku Madzulo kwa Europe kokha zimafika mu mamiliyoni a matani chaka chimodzi. (Onani tchati.) Njira zisanu ndi imodzi za kutaira zinthu zikugwiritsiridwa ntchito: (1) kutaira m’nyanja; (2) kutaira pa mtunda; (3) kusunga kwa nyengo yaitali; (4) kuchita nazo mwakuthupi, mwa mankhwala, kapena zaumoyo zina; (5) kuthira pa mtunda kapena m’nyanja, ndi (6) kugaya ndi kuzigwiritsiranso ntchito. Palibe ndi imodzi yonse ya njira zimenezi yomwe iri yokhutiritsa kwenikweni kapena chitsimikiziro chotheratu.

Zolephera ndi Polekezera pa Anthu

Pa usiku wa March wa mkuntho mu 1978, chiwiya chosungiramo mafuta chokulira cha Amoco Cadiz chinataya kusamalira kwake kwa chochinjirizira ndi kuthira pa nthaka kudzera ku doko la Britain ya France. Matani oposa 200,000 a mafuta osayengedwa anathiridwa m’nyanja, akumapha mbalame zoposa pa 10,000, kusokoneza indastri ya oyster, kuipitsa mtunda woposa pa makilomita 160 wa doko, ndi kupanga unyinji wa mafuta okhaokha. Kusasamala kwa munthu kunapatsidwa mlandu.

Chitsanzo chowopsya kwenikweni cha kulephera kwa munthu chinachitika mu April 1986. Ngozi yowopsya pa kampani yopangira nyukliya mu Chernobyl, U.S.S.R., inapha anthu 30, kuika m’ngozi mazana osaneneka, ndi kukakamiza kutuluka kwa nzika 135,000 za Soviet. The Wall Street Journal yasimba kuti: “Asayansi ambiri anena kuti ziyambukiro za umoyo za nyengo yotalikira za mbaliwali zosungidwa ndi anthu a ku Soviet ndi Europe pambuyo pa ngozi ya nyukliyayo zidzakhalapo zosadziŵika kwa zaka. . . . [Iwo] akuyembekeza matenda owonjezereka a kutha kwa mwazi ndi mapapo, kansa ya maere ndi pam’mero.” Mogwirizana ndi ripoti la Pravda, ngoziyo inachititsidwa ndi “kusoweka kwa thayo, kukulira kwa ntchito yosasamaliridwa, ndi kusoweka kwa kulangizidwa.”

Ngozi yofananayo inachitikapo kale. Der Spiegel yanena kuti “mtundu wa anthu wapulumuka pang’ono ngozi za kumbuyo m’nthaŵi zosiyanasiyana.” Magazini ya ku Germany imeneyi yadzinenera kukhala ikupeza kufikira ku maripoti 48 pa 250 a kusokoneza kongochititsidwa kosungidwa ndi International Atomic Energy Organization, zophophonya m’malo osiyanasiyana onga Argentina, Bulgaria, ndi Pakistan. Ambiri a amenewa, kuphatikizapo theka la kusungunuka mu March 1979 pa Three Mile Island mu United States, zinadziŵidwa kukhala kuphophonya kwa munthu.

Osati kokha kuti munthu ali wokhoterera ku kuphophonya koma alinso ndi polekezera m’kulamulira kwawo pa zopangapanga zawozo. Popeza kuti kukhoterera kwa kachitidwe ka nthaŵi zonse ku mbali ya pakati pa Europe kukuchokera kumadzulo kupita kummawa, Federal Republic of Germany idzafunikira kupirira ndi mpweya woipitsidwa wowulutsidwira kumeneko kuchokera ku England, pamene kuli kwakuti German Democratic Republic ndi Czechoslovakia amapirira ndi vuto la kuipitsidwa kwa mpweya kuchokera ku Federal Republic. Koma mpweya ungakhoze kusintha. Mwachitsanzo, m’nthaŵi ya tsoka ya Chernobyl, iwo unasamuka, ukumapangitsa Poland, maiko a Baltic, ndi Scandinavia—osanena za Soviet Union iyemwini—kukhala oipitsidwa kwenikweni ndi zidutswa zakupha za mpweya kuposa mbali zina za Europe.

Zoperewera Zowonjezereka Zowopsya

Anthu kaŵirikaŵiri amasowa kuwona mtima ndi kulunjika m’kulongosola nsonga ponena za kuipitsa. Pamene kuli kwakuti otetezera a malo otizungulira angakhoze kukonda mbali zosakhala zenizeni m’kuchirikiza kutsutsana kwawo, anzawo angachite mbali yawo yeniyeni. Mwachitsanzo, ulamuliro umodzi wanena ponena za mitsinje yoipitsidwa: “Mbali yabwino ya Elbe, inakhala ndi mlingo wokulira posinthira pa zana lina pakati pa nyanja za ku Europe m’kutulutsa kwake nsomba zochulukira, wakhala wopanda zamoyo kwa nthaŵi yaitali.” Chodzinenera chimodzimodzicho chapangidwa ponena za Rhine, makamaka pambuyo pa tsoka la pa Sandoz. Wolankhulira kaamba ka indastri ya zamankhwala, kumbali ina, wadzinenera kuti “ngakhale pambuyo pa moto wa pa Sandoz, Rhine ikali mu mkhalidwe wabwino kuposa mmene inaliri zaka khumi zapitazo.”

Kulankhula molunjika, ichi chingakhale chowona chifukwa chakuti zizindikiro mu 1983 zinali zakuti zoletsa kuipitsa za lamulo za boma zinkatsimikizira kukhala zophulapo kanthu ndi kuti Rhine inkapanga kuchira kodabwitsa. Ndipo ponena za Mtsinje wa Thames mu Britain, magazini ya National Geographic yasimba kuti: “M’zaka 30 zapitazo kuipitsa kwachepetsedwa ku 90 peresenti.” Kupita patsogolo kumeneku kwakhala kokha kothekera chifukwa cha kuyesayesa kogwirizana. Koma mogwirizana ndi mtola nkhani Thomas Netter, ichi chikusoweka m’maiko ambiri chifukwa chakuti “tsoka la malo otizungulira likuwonedwabe mofala monga vuto la wina.”

Mosakaikira ichi chiri chifukwa chimodzi chimene maboma akukhalira ndi mavuto ochulukira a kutsatira kulamulira kuipitsa kwa dziko lonse. Kwa zaka zingapo Canada ndi United States analephera kufikira chimvano chirichonse m’kumenyera mvula ya acid. Potsirizira pake, kupita patsogolo kodekha kunapangidwa mu 1986. Kufikira pamenepo, monga mmene nduna ya ku Canada inanenera, “mvula ya Acid inatha m’madzi, monga nsomba.” Ndipo ngakhale kuti mitundu 31 inavomerezana mu 1987 kuti ichepetse kufika ku theka kutulutsidwa kwa mankhwala owaza akupha tizirombo otsekeredwa mu zitini omwe akuwonekera kukhala akuwononga mpweya wochinjiriza chilengedwe wa dziko lapansi, chonulirapo chimenechi sichidzafikiridwa kufikira posinthira pa zana lino. Kuti ipititse patsogolo kugwirizana kowonjezereka kwa mitundu yonse, European Community inalamulira 1987 kukhala “Chaka cha Malo Otizungulira.”

Kupita patsogolo kochepera kudzapangidwa, ngakhale ndi tero, malinga ngati anthu aumbombo aipitsa mwadala kaamba ka chifuno cha kulemera mwa ndalama, kapena anthu a dyera kaamba ka chifuno cha kuwakomera. Kupita patsogolo kumadalira pa kudera nkhaŵa kaamba ka kukhala bwino kwa wina ndi m’nzake ndi kufunitsitsa kulandira thayo laumwini. “Kulamulira kuipitsa kumayambira pa nyumba—ponena za ichi ndine wokhutiritsidwa,” inatero nduna ya boma ya ku Germany ya malo otizungulira Klaus Töpfer. Chotero nzika iriyonse ifunikira kuchita mbali yake. Munthu wachichepere modzilungamitsa angaloze chala pa munthu wachikulire—makampani a zamankhwala ndi mafakitale—koma kodi munthu wachichepere ali wabwinopo ngati zala zakezo ziri zotanganitsidwa kumwaza zinyalala?

Baibulo linaneneratu kuti “m’masiku otsiriza” anthu adzakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayanjanitsika, . . . osakonda chabwino.” (2 Timoteo 3:1-5) Popeza kuti iyi iri mikhalidwe yeniyeniyo yomwe imachirikiza kuipitsa, mkhalidwewo ungawoneke kukhala wopanda yankho. Chikhalirechobe, tiri ndi chifukwa cha kukhulupirira kuti zokhumudwitsa zomwe ziri m’njira ya dziko lopanda kuipitsidwa zidzachotsedwa—ndipo mwamsanga!

[Bokosi patsamba 6]

Zokhumudwitsa m’Kumenyera kwa Munthu Molimbana ndi Kuipitsa

◼ Kukula kosalamulirika

◼ Chidziŵitso chosakwanira

◼ Zolephera za munthu

◼ Kusoweka kwa kulamulira zopangapanga

◼ Kusasamala kwa dyera kaamba ka makhalidwe abwino a ena

[Tchati/Mapu patsamba 7]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Matani Oyerekezedwa a Ululu Wotaidwa Wotulutsidwa mu Chaka Chimodzi cha Posachedwapa

Norway 120,000

Finland 87,000

Sweden 550,000

Netherlands 280,000

Britain 1,500,000

F. R. of Germany 4,892,000

Switzerland 100,000

France 2,000,000

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena