Tchalitchi cha Chikatolika mu Spanya—Zitsutsano
Ndi mlembi wa Galamukani! mu Spanya
“Zinthu sizimakhaladi monga mmene zimawonekera.” Kawonedwe kameneka kochitidwa ndi Bwana William Gilbert kamafotokoza moyenerera kachisi wa Sagrada Familia mu Barcelona (wosonyezedwa pa tsamba 10). Nsanja zake zazikuluzo zimabisa mkati mwake mopanda kanthumo—pambuyo pa zaka mazana za kumangidwa, kachisiyo adakalidi chikhokhombe. Chikatolika cha ku Spanya nachonso chiri kokha kusakanizikana kwa nyonga ndi kupanda kanthu, monga momwe ndemanga zothiriridwa ndi Aspanya otsatirapoŵa zikuvumbulira:
“John XXIII? Dzinalo likumveka kukhala lozoloŵera. Kodi iye anali mfumu?” anatero Cristina, wachichepere Wachispanya, amene anali asanamvepo za papa wotchukayo.
Woyendetsa takisi wa ku Madrid wotchedwa José Luis ndi mkazi wake, Isabel, anafika mwakamodzikamodzi kutchalitchi chapamalopo kuti achititse mwana wawo wamwamuna kubatizidwa. “Kodi nchifukwa ninji mukufuna kubatizitsa mwana wanuyo?” anafunsidwa. “Chifukwa ndife Akatolika,” anayankha atateyo. Komabe, atapanikizidwa, anavomereza kuti chifukwa chachikulu chinali kupeŵa mavuto ndi banjalo.
MUNTHU amene amafika ku Spanya m’nthaŵi ya Mlungu Wopatulika angasangalatsidwedi ndi maligubo ochitidwira m’mizinda m’dziko lonselo. Koma Aspanya ena—makamaka achichepere—angakhale akudziŵa zochepera, ngati zingakhalepo, zonena za chipembedzo chimene iwo amadzinenera.
Umbuli wa chipemebedzo kaŵirikaŵiri umaphatikizidwa ndi mphwayi za chipembedzo. Ngakhale kuli kwakuti Aspanya ambiri amabatizidwa, kukwatitsidwa, ndi kuikidwa ndi tchalitchi—ndipo amadzilingaliradi kukhala Akatolika—kukhala mogwirizana ndi malamulo Aroma ndinkhani ina.
Makolo angabatizitse ana awo koma samalingaliradi kukhala ndi thayo la kuwaphunzitsa chiphunzitso Chachikatolika. Okwatirana mosakaikira amachititsa zowinda zawo kutsimikiziridwa ndi tchalitchi koma samawona kukhala omangika kutsatira ziphunzitso za tchalitchi pa nkhani zaukwati. Ndipo 10 peresenti ya awo amene amanena kuti ndiwo Akatolika samakhulupiriradi Mulungu weniweni.
Mkhalidwewu suli wodabwitsa kotheratu, polingalira unansi wa Spanya wokhalitsa koma wotsutsana ndi tchalitchi. Yofotokozedwa kalelo kukhala “nyali ya [upo] wa Trent, nyundo yotsutsa chikhulupiriro ndi lupanga la Roma,” Spanya yakhalanso ndi “chizunzo chamwazi koposa cholandiridwa ndi Tchalitchi Chachikatolika m’kukhalapo kwake konse,” akutero profesa wa mbiri yapanthaŵiyo pa Unirvesiti ya Deusto, Vizcaya.
M’zaka za zana la 16, ndalama Yachispanya ndi magulu ankhondo Achispanya anatetezera Chikatolika cha ku Ulaya ku funde la Chiprotesitante, koma mu 1527 Roma ndi Vatican yeniyeniyo anafunkhidwa mopanda chifundo ndi gulu lankhondo la mfumu Yachispanya ndi Wolamulira Woyera Wachiroma Charles V.a Charles, mofanana ndi olamulira ena Achispanya, ananyalanyaza poyera malamulo aliwonse a Vatican amene iye sanawakonde.
Kudziimira kwa Spanya chikhalirechobe mtundu watsopano wa Chikatolika kwapeza zitsutsano zimenezi kuchokera kuunansi wapadera wa Tchalitchi ndi Boma, wopangidwa pamene zonse ziŵirizo zinali pakaindeinde wa ulamuliro wawo.
[Mawu a M’munsi]
a Pambuyo pa kufunkhidwa kwa Roma mu 1527, Charles anakhazika Papa Clement VII muukaidi weniweni wapanyumba mu Castel Sant’ Angelo, Roma, kwa miyezi isanu ndi iŵiri.