Kodi Mapeto a Kuipitsa Ali Pafupi?
CHIYEMBEKEZO cha dziko lapansi laudongo chiridi chosangalatsa. Koma kodi chiri chenicheni? Chabwino, maiko ena akuyesera mwamphamvu kuwongolera mkhalidwe wa kuipitsa. Kuchepa kwa kuipitsa mpweya tsopano kukusimbidwa kaamba ka miyezo yamphamvu ya kuchepetsa mtovu wokhala mu utsi wa magalimoto. M’malo ena, kuipitsa kwa maindasitale kukuwoneka kuti kwatsikanso. Komabe, zimenezi sizimakhala tero nthaŵi zonse chifukwa cha zoyesayesa zosamalitsa. M’malomwake, nthaŵi zina zimakhala chotulukapo cha kusintha kwa maindasitale kochititsidwa ndi vuto ladziko lazachuma.
Dziko Lapansi—Lolinganizidwa Kudziyeretsa Lokha?
Kuwonjezerapo, pali zipangizo zoyeretsa mwachibadwa zogwira ntchito. Mwachitsanzo, zomera zapanyanja zotchedwa phytoplankton ziri chimodzi cha zoletsa kuipitsa panyanja, molingana ndi Dr. Aubert wa ku Medical Oceanography Center mu Nice, France. Tamoyo tating’onoting’ono timeneti timatulutsa mankhwala achibadwa amene amawononga kuyambukira. Mwatsoka, ito tikugonjetsedwa. Mu Italy, Venice ndi Nyanja ya Adriatic yapafupi ziri zokutidwa ndi ndere. Mu Adriatic kuipitsa kumatulutsa “ndere, yonunkha ndi yoterera, yayelo, yofiira modera ndi yotumbuluka, imene imafalikira kulinga kum’mwera kwa makilomita mazanamazana” m’chirimwe. (The Globe and Mail, Toronto, Canada) Chimodzi cha zochititsa ndicho ngalande yochokera ku mtsinje wa Po, “yokhala ndi zonyansa zosasukulutsidwa zochokera kwa anthu oposa 15 miliyoni, zotaidwa zochokera ku maindasitale ambiri aakulu a Italy . . . ndi ndowe za nkhumba zoposa mamiliyoni asanu.”
Bwanji ponena za kuipitsa kwa nthaka? Kufufuza kochitidwa ndi kampani yaikulu ya zamankhwala mogwirizana ndi U.S. Department of Energy kunavumbula kukhalapo kwa mitundu yambirimbiri ya tizirombo ta bacteria, fungi, ndi amoebas m’nthaka, tina topezeka pa mamita 260 kunsi kwa nthaka. Dr. David Balkwell wa ku Florida State University anachitira ndemanga kuti: “Zamoyo zakuya pansi zimenezi zingakhale zikuyeretsa aquifer [madzi am’nthaka achilengedwe].” Mosiyanitsa, Dr. Balkwell ali ndi chiyembekezo chakuti ainjiniya a majini adzakhala okhoza kuchititsa zamoyo zakunsi kwanthaka zimenezi “kuwononga zoipitsa zachindunji.”
Ngakhale ndi tero, m’chenicheni tiyenera kumaliza kuti mkhalidwe wa nthaŵi ino sumalinga bwino mapeto amwamsanga a kudetsedwa kwa zinthu za dziko lapansi. Chikhalirechobe, tingakhale otsimikiza kuti mapeto a kuipitsa ali pafupi. Chifukwa ninji?
Kuchotsapo Kuipitsa Kwamakhalidwe
Kuti pulanetili likhaledi mudzi waudongo wa mtundu wa anthu, nzika zake ziyenera kukhala anthu audongo, mwamakhalidwe limodzinso ndi mwakuthupi. Anthu ayenera kugonjetsa kudzikonda kwawo kwakukulu ndi kukulitsa mikhalidwe yopanda dyera, akumasonyeza kulingalira anthu anzawo ndi zinyama. Kodi zimenezi zingachitidwe?
Kwa zaka makumi ambiri, Mboni za Yehova zapeza kuti zingatero. Izo zayesa mphamvu youmba umunthu ya Baibulo, ndipo zapeza kuti bukhu limeneli liri ndi mphamvu yokhoza kusintha anthu, ndi ziyambukiro zaphindu ku malo otizinga. Mwachitsanzo, akuluakulu a masitediyamu amasangalala ponena za dongosolo ndi udongo wa magulu opezeka pa misonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova. Ndemanga yakaŵirikaŵiri njakuti ‘sitediyamu inasiidwa yaudongo kuposa pamene Mboni zinaloŵamo.’
Membala wa ogwira ntchito pa bwalo la zamaseŵera mu Lisbon, Portugal, analongosola kwa mmodzi wa Mboni za Yehova kuti: “Pamene anthu andifunsa zimene ndimaganiza ponena za inu, sindinganene bodza. Ndimawauza kuti Mboni za Yehova ziri ndi makhalidwe abwino kwambiri, udongo ndi dongosolo. . . . Ngati mwadetsa chinthu chimodzi, mumayeretsa 99! ”
Kuumirira kwa Mboni pa udongo wakuthupi kumagwirizanitsidwa ndi malamulo awo apamwamba amakhalidwe abwino. Malamulo amakhalidwe abwino otani? Aja ofotokozedwa m’Baibulo, limene liri Mawu olembedwa a Mulungu. Ponena za obwerera kumbuyo, Baibulo limanena kuti njira za Mulungu ‘ziri zapatali kupambana njira zawo, ndi maganizo ake kupambana maganizo awo.’ (Yesaya 55:7-9) Komabe, tingaphunzire njira za Mulungu chifukwa chakuti Mulungu iyemwini amapereka malamulo ake kwa okhumba kuwatsatira. Maphunziro aumulungu ameneŵa ali ofunika kaamba ka mtsogolo mwathu.
Mamiliyoni a Mboni lerolino amayesera zolimba kutsatira miyezo imeneyi ya makhalidwe oyera, ndipo amapindula mokulira. Ngakhale ndi tero, kwa ambiri zimenezi zatanthauza kupanga masinthidwe aakulu m’zizoloŵezi zawo ndi njira zamoyo.
Mankhwala Ogodomalitsa, Kumenyedwa, ndi Chilakiko
Tiyeni titenge chochitika cha Marie, mmodzi wam’banja la anthu 13 la ku malo okanthidwa ndi upandu mu m’zinda wa mu England.
“Banja langa linali lotchuka kwambiri kaamba kokhala lovuta, ndipo mofanana ndi ena onse, ndinali wovutitsa wodziŵika. Pa msinkhu wa zaka 15, ndinapititsa padera. Zaka ziŵiri pambuyo pake, mwana wanga wamkazi anabadwa, ndipo ndinasiidwa kumsamalira pandekha. Tsamwali wanga anagwidwa ku sukulu [yolangirako]. Iye anathawa, ndipo ndinakhalanso ndi pakati. Ndinayesera njira zonse kuti nditaye mimbayo ndipo pomalizira ndinapambana, koma ndinatsala pang’ono kutaya moyo wanga.
“Tsamwali wanga anayamba kusuta chamba ndipo anakhala wachiwawa kwambiri kwa ine, ngakhale kuti ndinalinso ndi pakati. Nanenso ndinadziloŵetsamo, ponse paŵiri kusuta ndi kugulitsa chambacho. Panthaŵiyi ndinkakhala m’nyumba yodzala akazi achigololo. Ndinkawalerera ana awo.
“Pamene ndinakondweretsedwa mwa mnyamata wina, tsamwali wanga woyamba anaimitsa unansiwo mwakumpyoza ndi mpeni kasanu ndi katatu. Pachimenechi anamangidwanso. Pambuyo pa kutulutsidwa kwake kundende tinakwatirana ndipo aŵirife tinamwerekeratu m’mankhwala ogodomalitsa.”
Pambuyo pokumana ndi Mboni za Yehova ndi kuphunzira nawo Baibulo, wachichepere ameneyu anayamba kupezeka ku misonkhano Yachikristu ndipo pang’onopang’ono anasintha. Marie akulongosola kuti:
“Ndinayamba kuzindikira kuti kusuta ndi kumwa mankhwala ogodomalitsa kunali kolakwa. Pambuyo pouza mwamuna wanga kuti ndinali kuleka zonsezi, iye ankauzira utsi wa ndudu yake ya chamba pa nkhope panga, kuyesera kundikopa kuti ndiyambenso kumwa mankhwala ogodomalitsa. Ndinakhalanso ndi pakati. Mwamsanga pambuyo pake, mwamuna wanga anayamba kugona kunja.
“Miyezi isanu ndi itatu pambuyo pake iye anatenga zinthu zake zonse m’nyumba ndi kundisiya. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuiŵala zimenezi, ndipo anatero. Kenaka, pambuyo pa miyezi itatu, mwamuna wanga anabweranso. Ndinapemphera kaamba ka nyonga ya kuchita zimene zinali zolondola. Kachiŵirinso ndinayesera kupanga chipambano cha ukwati wanga, koma mkati mwa miyezi isanu ndi umodzi ndinali wosokedwa mfundo 14 pa chironda mozungulira diso, chotulukapo cha chiwawa cha mwamuna wanga; mankhwala ogodomalitsa anali adakali chikondi chake choyamba. Nyumba yathu inakhala depo yaikulu ya mankhwala ogodomalitsa ya dera lonselo. Inali yodzaza ndi ‘mabwenzi’ ake, ambiri a iwo oledzera ndi mankhwala ogodomalitsa.
“Ndi thandizo la Yehova, ndinalimba mtima ndi kuyang’anizana ndi amunawo. Ndinawapempha mwaulemu kupita kunja ngati anafuna kupitiriza kusuta mankhwala awo ogodomalitsa. Pamene mwamuna wanga anamva zimenezo, anapsya mtima, anandiitanira mu kitchini, ndikuyamba kugunditsa mutu wanga kuchipupa. Ndinalimbikira kumuuza kuti ndinali wodera nkhaŵa kaamba ka ana ndipo ndinafuna kuwapatsa mwaŵi wakukulira m’malo abwino, audongo. Mwamuna wanga anatuluka mofulumira kupita kwa mabwenzi ake. Ndinayembekeza, ndikumapemphera. Anabweranso m’kitchini, ndipo ndinaganiza kuti adzandipha.
“Ngakhale ndi tero, kuchokera nthaŵi yomweyo zinthu zinabwerera pansi mokulira. Pambuyo pake tinasamuka. Pamene omwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa anadzacheza, iwo sankatukwana kapena kulankhula za miyoyo yawo yachisembwere monga poyamba. Zinawoneka kuti anatipatsa ulemu.”
Kaimidwe ka Marie kaamba ka makhalidwe audongo ndi moyo wosaipitsidwa kanagwira mtima wa mwamuna wake, ndipo nayenso m’kupita kwa nthaŵi anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Onse aŵiri Marie ndi mwamuna wake tsopano ali Mboni zobatizidwa ndipo ali otanganitsidwa kuthandiza ena kuyeretsa miyoyo yawo ndi thandizo la chidziŵitso cha Baibulo. Marie akunena kuti:
“Pamene ndimamva mwamuna wanga akupemphera, kapena pamene ndimamumva akulongosola chikondi chake cha Yehova, mtima wanga umagunda motani nanga! Kusintha m’mawonekedwe ake kumazizwitsa mabwenzi ake akale. Tsopano banja lathu nlogwirizanadi. Sindinakhalepo wachimwemwe motero, ndipo sindinaleke kuyamikira Yehova kaamba ka kutitulutsa m’dongosolo la zinthu iri loipitsidwa.”
Chipambano choterocho m’kulimbana ndi kuipitsa makhalidwe chimavumbula mphamvu ya Mawu a Mulungu. Ndiponso, chimaloza ku chiyembekezo cha mapeto amwamsanga a mitundu yonse ya kuipitsa. Kodi Baibulo limanenanji ponena za zimenezi?
Dziko Laudongo—Lotsimikizirika
Phunziro losamalitsa la Baibulo limavumbula kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo iri la zinthu. (2 Timoteo 3:1-5) Mkhalidwe wa malo otizinga uli kokha mbali imodzi ya umboni wotsimikizira zimenezi. Kodi zimenezi zikutanthauzanji ponena za chiyembekezo chathu kaamba ka dziko laudongo?
Zimatanthauza kuti Mulungu posachedwapa adzaloŵerera m’zochitika za mtundu wa anthu. Iye posachedwapa adzachita mwa njira yamphamvu kuchotsapo kuipitsa konse kwamakhalidwe ndi kwakuthupi pa pulaneti lathu. M’bukhu la Chibvumbulutso iye akulonjeza “kuwononga iwo akuwononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:18.
Ndithudi, Mulungu yekha ndiye ali ndi mphamvu ya kubweretsa dziko lapansi laudongo, losaipitsidwa. Nkochititsa nthumanzi kudziŵa kuti iye akufuna kuchitadi tero. Pamene adzachitapo kanthu, mtsogolo posachedwapa, zidzakhala monga mmene iye mwini akunenera kuti: “Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” (Chibvumbulutso 21:5) Kenaka, pomalizira pake, pulaneti lathu lidzakhala mudzi woyenera wa anthu audongo, olungama, amene adzasangalala ndi zochuluka zake kosatha.