Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 5/8 tsamba 13-16
  • Chikhulupiriro Chinandithandiza Kuyang’anizana ndi Opareshoni ya Ubongo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhulupiriro Chinandithandiza Kuyang’anizana ndi Opareshoni ya Ubongo
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chosankha Changa Nchosakambitsirana
  • Kukonzekera Opareshoni
  • Kuchira kwa Pambuyo pa Opareshoni
  • Mautumiki a Maliro Akonzedwa
  • Moyo Wanga Tsopano Wabwerera M’malo Mwake
  • Sitili Amatsenga Kapena Milungu
    Galamukani!—1994
  • Sanaleme
    Galamukani!—1998
  • Kuyang’anizana ndi chothetsa Nzeru cha Matenda
    Galamukani!—1996
  • Mabanja Amene Zinthu Zikuwayendera Bwino—Chigawo Choyamba
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 5/8 tsamba 13-16

Chikhulupiriro Chinandithandiza Kuyang’anizana ndi Opareshoni ya Ubongo

“ULI ndi chotupa kumbuyo kwa diso lako lakumanzere.” Mawu ameneŵa, olankhulidwa ndi Dr. Stewart, katswiri wa matenda a mitsempha, anandipangitsa kudzimva ngati kuti ndinali mkati mwa loto loipa. Mawu ake otsatira anasintha lotolo kukhala lowopsya: “Ndiyenera kulankhula ndi banja lako kotero kuti tingakuike m’chipatala mwamsanga.”

Zinandidabwitsa. Sizingakhale zowona. Ndinali kumva bwino! Kodi msungwana waumoyo wa zaka 22 zakubadwa angakhale bwanji ndi chotupa cha mu ubongo? Maganizo anga anatsutsa mawu a dokotalawo amene anandichotsa pa njira imene ndinazikhazikitsira m’moyo. Ndine mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo m’mawa wapitawo, ndidalandira telefoni yondiitana kukagwira ntchito pa malikulu a Watchtower Society mu Brooklyn kwa miyezi itatu. Chinali chimene ndinayembekezera ndi kupempherera. Pamene ndinachoka panyumba m’mawa umenewo kupita kukawonana ndi katswiri wa matenda a maso, ndinadzimva bwino kwabasi.

Tsopano, maola 29 pambuyo pake, kudzimva koteroko kunachoka m’maganizo mwanga. Panalibe chikaikiro ponena za chotupacho. Ndinathera mphindi 50 nditatsekeredwa mu makina a MRI (Magnetic Resonance Imagery), monga chiwiya choponyera mabomba mkati mwa chipinda, chodikirira kuti chiponyedwe. Ndimachita mantha ndi malo obindikiritsidwa, ndipo kuutali umene ndinali mkatimo, ndinakhala wamantha mowonjezereka. Ndinapempherera bata, kung’ung’udza nyimbo Zaufumu, ndi kubwereza malemba a Baibulo. Ndinapeza mpumulo. Posakhalitsa ndinali kubwerera ku ofesi ya katswiri wa matenda a mitsempha ndi chithunzi. Icho chinavumbula chotupa cha ukulu wa lalanje lalikulu, ndipo anabweretsa nkhani yoipayo—ndinayenera kukhala m’chipatala pa nthaŵi yomweyo. Anatuluka kupita kukaitana makolo anga.

Chosankha Changa Nchosakambitsirana

“Makolo ako akubwera,” iye anatero pamene anabwerera. “Sunandiuze kuti ndiwe mmodzi wa Mboni za Yehova. Tidzakambitsirana. Ndithudi opareshoniyo idzafunikira kuthiridwa mwazi.”

“Palibe zokambitsirana,” ndinatero. “Chosankhacho chapangidwa kale. Sindifuna mwazi.”

“Chabwino, tingalankhule zimenezo pamene makolo ako afika pano.”

“Ayi,” ndinatero ndikupukusa mutu wanga, “nzosakambitsirana.”

Pamene makolo anga anafika, anatsimikizira kaimidwe kanga pa mwazi. Katswiri wa matenda a mitsemphayo anavomereza chosankhacho nanena kuti akudziŵa katswiri wochita opareshoni amene mwinamwake angalemekeze chosankha changa. Motero tinakumana ndi katswiri wochita opareshoni ya mitsempha, Dr. H. Dale Richardson.

Tinakumana naye mu ofesi yake Lachinayi madzulo, September 30, 1988, mwamuna ameneyu amene akakhala mbali yofunika ndipo yolemekezedwa kwambiri m’miyoyo yathu kwa miyezi ingapo yotsatira. Iye anali adakambitsirana ndi Dr. Stewart ndipo anadziŵa za kaimidwe kathu pa mwazi.

“Tidzidzadula mbali ya mitsempha yambiri,” iye anatero. “Chotupacho chazungulira sagittal sinus (mtsempha waukulu wa mwazi wa ubongo), kuti ndi kuukulu wotani sitingadziŵe kufikira titafika pamenepo.”

“Ngakhale zitafika poipa,” ndinatero, “ndipo ndikumvetsetsa kuti zingatero, sindikufunabe kuti mugwiritsire ntchito mwazi.” Amayi anga ndi atate anga anatsimikiza kuti kaimidwe kanga ndiko kaimidwe kawo. Tinawona maso ake akudzaza ndi misozi, ndipo pambuyo pake tinadziŵa kuti anali ndi ana aamuna aŵiri ndi wamkazi ake ake.

“Mwina sindingagwirizane ndi zikhulupiriro zanu,” iye anatero, “koma ndidzalemekeza chopempha chanu. Tiri ndi mwaŵi wa chipambano wokwanira 70 peresenti popanda mwazi. Muyenera kumvetsetsa kuti mwina sitingachotse chotupa chonsecho kwa nthaŵi yoyamba. Sizachilendo ndi chotupa cha ukulu umenewu kuchita maopareshoni aŵiri kapena atatu.”

Kukonzekera Opareshoni

Ndinapita ku chipatala pa Sande, October 2. Lolemba ndi Lachiŵiri anatanganidwa ndi zochita opareshoni isanayambike, choyamba kupeza ndipo kenaka kuchepetsa mwazi woperekedwa ku chotupacho. Lachiŵiri lonse mabwenzi ananditumizira foni, ndipo madzulo amenewo ambiri anandichezera. Onse anadziŵa zimene zidzachitika tsiku lotsatira, koma mkhalidwe unali wabwino ndipo wachimwemwe.

Ndinagona tulo pasanapite nthaŵi yaitali usiku umenewo koma ndinadzuka pafupi ndi pakati pa usiku ndikuyamba kuda nkhaŵa. Zimenezi sizinali zabwino. Ndinaseŵera makaseti tepi angapo a nkhani za magazine a Watchtower. Pa 5:30 m’mawa, nesi anabwera ndipo anadabwa kupeza kuti ndinali wabata ndipo wachidaliro. Mabwenzi aŵiri apamtima anafika mwamsanga pambuyo pake, ndi Atate pambuyo pawo. “Osandipatsa zinthu zoipa,” ndinatero pamene amkanditsanzika.

Pansipo anayamba kundikonzekeretsa kaamba ka opareshoni, kuika masingano, kumeta tsitsi langa. Pamene ndinaligone pamenepo, ndinapemphera kwa Yehova kuti: “Ndikuyamikani chifukwa chondithandiza kutsimikizira kuti Satana sapambana nthaŵi zonse. Ndidziŵa kuti ndidzauka, kaya likhale lero lomwe kapena m’dziko lanu latsopano. Chonde, lolani kuti likhale tsopano apa.” Pamene ankandipititsa ku chipinda chochitira opareshoni, ndinawona Dr. Richardson akuwona chithunzi changa.

“Wadzuka bwanji, Bethel,” iye anatero. “Unagona bwanji?”

“Ndinagona bwino,” ndinayankha motero, “koma ndikudera nkhaŵa za mmene munagonera inuyo.”

Kenaka Dr. Ronald Pace, katswiri wa mankhwala oletsa kumva kupweteka, anaika chophimba kumaso kwanga nandiuza kuti ndikoke mpweya wambiri ndikumaŵerenga chafutambuyo. Kudikirira kwanga kunatha.

Kuchira kwa Pambuyo pa Opareshoni

Chinthu chotsatira chimene ndinadziŵa chinali chakuti ndinamva kuzizira kwambiri. Ndinalimbikira kuchoka mu nkhungu yochititsidwa ndi mankhwala. Inali 10:10 p.m. Lachitatu, maola 15 pambuyo pake. Atate anali m’chipinda cha odwalitsa, akumandilimbikitsa. Ndinali wodera nkhaŵa ngati malingaliro anga onse anali bwino. “Ndiyeseni Atate,” ndinatero, ndipo ndinayamba kupanga masamu: “Ziŵiri kuwonjeza ziŵiri ndi zinayi, zinayi kuwonjeza zinayi ndi zisanu ndi zitatu, . . . ” Pamene ndinafika 512, iwo anati, “Ha! Ukuthamanga mondiposa!” Amayi anandikupatira monga mmene akanathera, ndipo mlongo wanga, Jonathan, anandibweretsera zotulukapo zaposachedwa za maseŵera a baseball.

Dr. Richardson anasimba kuti anachotsa 80 peresenti ya chotupacho. Anawoneka wotopa—nzosadabwitsa, pambuyo pa maola 13 1/2 a zofunika zosamalitsa zoterozo pa luso lake! Pambuyo pake ndinadziŵa kuti anawauza bambo anga kuti: “Anakhala pang’ono kutisiya. Pamene tinafika pa sagittal sinus, anayamba kukha mwazi wambiri. Tinali ndi mwaŵi kuti tinakhoza kuuletsa.” Mwanjira iriyonse, ayenera kubweranso, mwinamwake koposa kamodzi. “Odwala meningioma [mtundu wa chotupa chimene ndinali nacho] ena ayenera kukhala ndi opareshoni pambuyo pa zaka zitatu kapena zisanu zirizonse,” iye anatero. “Mwinamwake sitidzakhala okhoza kuchita zonsezo.”

Nkhani imeneyi inandithetsa nzeru! Ndinawona ziyembekezo zanga za moyo wa utumiki Wachikristu wa nthaŵi zonse ukuswedwa. Ndinayamba kulira, chifukwa cha mantha. Atate anaika manja awo mozungulira Amayi ndi ine ndikuyamba kupemphera. Zinali ngati kuti chovala cha bata chavekedwa pa ine. “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse” unatenga malo. (Afilipi 4:7) Ndinaŵerengapo za ena amene anamva mtendere umenewu wa Mulungu ukuwadzera ndikudabwa mmene umamvekera. Tsopano ndinadziŵa. Sindingafune kupitanso m’chokumana nacho cha usiku umenewo, koma chimene ndinadziŵa kuchokera ku chokumana nachocho chiri chinachake chimene ndidzayamikira nthaŵi zonse.

Pamene ndinali m’chipatala, ndinalankhula kwa anthu ambiri ponena za chiyembekezo changa cha Ufumu wa Mulungu ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Ndinagaŵira timabukhu 20 takuti Jehovah’s Witnesses and the Question of Blood ndi mabukhu aakulu asanu a Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Pofika nthaŵi imene ndinachoka, ndinali ntalandira makadi oposa 330 ndi matelefoni ambiri, kuwonjezapo maluwa ndi mabaluni okongola. Zinandisangalatsa motani nanga ndipo zinandipangitsa kuyamikira mowonjezereka ubale wathu wa dziko lonse!

Ndinatulutsidwa pa October 16, 1988. Limene linawoneka kukhala tsiku lokongola linawoneka kukhala lokoma koposa tsopano popeza ndinali kunja kachiŵirinso m’kuwala kwa dzuŵa ndi mpweya wabwino. Mtambo unawoneka kukhala wobiriŵira modera moposerapo, udzu unawoneka wobiriŵira moposerapo. Zinandipangitsa kulingalira za mmene dziko lapansi la Paradaiso lidzakhalira lokongola: kopanda nkhondo, kopanda njala, kopanda kuipitsa—ndipo kopanda zotupa za mu ubongo! Pomalizira pake, dziko lapansi loyeretsedwa!

Mautumiki a Maliro Akonzedwa

Mu December, ndinawonanso Dr. Richardson. Chotupacho chinali kukula. Kuchitidwa opareshoni kunali thandizo lokha lodalirika ndipo zikanakhala bwino titafulumira. Ndinawona opareshoni yachiŵiriyi kukhala chipupa chenicheni, chotchinga chachikulu chotseka njira imene ndinaikhazikitsa kaamba ka moyo wanga. Ndinalingalira za Salmo 119:165: “Akukonda chilamulo chanu [cha Mulungu] ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.” Mawuwa ananditonthoza, ndipo pang’onopang’ono, m’malo mokhala chipupa, opareshoni yomadzayo inali chinthu chaching’ono. Koma kuti mwina kungapangike zina, ndinalembera bwenzi lapamtima ku malikulu a Watchtower kumupempha kupanga makonzedwe a maliro ngati kutakhala koyenera. (Pambuyo pake ndinapeza kuti Atate anapanga pempho lofananalo kwa iye.)

Pa January 31, 1989, ndinapitanso ku chipatala. Mwanjira zina zake chinali chopepuka, komabe zinawoneka kukhala zovuta kwambiri. Kodi akachotsa chotupa chonsecho nthaŵi ino, kapena kodi pakakhala maopareshoni ena pambuyo pake? Madokotala anali opereka chitonthozo.

Pamene ndinafika, Dr. Pace, katswiri wa mankhwala oletsa kumva kupweteka amene ndinali naye papitapo, anabwera kudzandiwona, anakhala nane kwa ola limodzi pamene ntchito yolemba inkapangidwa, ndipo kenaka ananyamula sutikesi yanga kupita nayo ku chipinda. Dr. Richardson ananditsimikizira kuti: “Ndidzakuchitira monga chiŵalo cha banja langa, mmene ndingafunire kuchitiridwa.” Palibe maseŵera, ntchito yokha basi. Ndinali ndi lingaliro labwino lachidaliro pamene ndinadziika m’manja awo achisamaliro.

Kachiŵirinso, matelefoni ndi makadi anafika kunditonthoza, ndipo mabwenzi apamtima amodzimodziwo amene anali athithithi ndipo othandiza m’chochitika choyamba anabweranso kudzandipatsa nyonga ndikundipangitsa kumwetulira. Tinathera madzulowo tikulankhula ndi kuseŵera seŵero la pa thabwa.

Moyo Wanga Tsopano Wabwerera M’malo Mwake

M’mawa wotsatira nesi anabwera msanga kudzandipatsa jekeseni. Anali wogoneka, ndipo sipanatenge nthaŵi yaitali pamene ndinalinso m’chipinda chochirira. Opareshoniyo sinali yaitali monga yoyambayo—nthaŵi ino maola khumi—ndipo moni amene ine ndi banja langa tinalandira anali wochiritsa kwabasi. Dr. Richardson womwetulira anatiuza kuti anakhoza kuchotsa chotupa chonsecho, ndipo tingayembekezere kuchira kotheratu. Pambuyo pake, pamene ankasintha nsalu zanga zapachironda, anandiseketsa mwakunena kuti: “Bethel, tidzayenera kuleka kukumana motere.” Tinali oyamikira chotani nanga kwa Yehova ndi adokotala abwinowo!

Ndinagaŵira mabukhu ndi timabukhu onena za Ufumu wa Mulungu kwa ambiri amene ndinalankhula nawo. Limodzi la mabukhuwo, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, ndinalipereka kwa Dr. Richardson. Ndinalemba kumbali kwake kuti:

“Pamakhala nthaŵi zoŵerengeka pamene timakhala ndi kuyenera kwa kuyamikira winawake chifukwa chopulumutsa moyo wathu. Pamene kuli kwakuti mosakaikira inu mumalandira ziyamikiro zoterozo, ndinafuna kukhala wotsimikiza kuti mudziŵe mmene zimene munatichitira zinatanthauza kwa banja langa ndi ine. Ndikudziŵa kuti nthaŵi yanu yoŵerenga njochepa, koma ngati mudzakhala ndi nthaŵi yogwira ntchito ndi Mboni za Yehova mtsogolo, ndikhulupirira kuti bukhu limeneli lingakuthandizeni kumvetsetsa chifukwa chimene ndimakhulupirira njira imeneyi. Ndikupatsani moni ndi chiyamikiro chachikulu, Bethel Leibensperger.”

Ndinatulutsidwa masiku asanu ndi atatu pambuyo pa opareshoni yachiŵiriyo ndikupita ku Nyumba Yaufumu usiku umenewo. Miyezi iŵiri pambuyo pake ndinayamba kuyendetsa galimoto yanga. Ndinayambanso uminisitala wanga wa nthaŵi zonse monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinalinso wokhoza kupezekapo pa misonkhano yopanga mbiri ya Mboni za Yehova mu Poland mu August 1989.

Moyo wanga tsopano wabwerera m’malo mwake.

[Bokosi patsamba 14]

Zikumbukiro za Amayi

Usiku umenewo Bethel ndi bambo ake anapezekapo pa phunziro Labaibulo. Ndinasokonezeka; ndinalephera kuzisamalira. Ndinadzipinda ndikugona. M’mawa wotsatira zinaipiratu. Ndinalephera kudzilimbikitsa ndipo ndinayamba kulira. Mwamuna wanga ananena mwamphamvu kuti: “Tiyenera kukhala olimba ndi osangalala chifukwa cha Bethel.” Kenaka anaika mikono yake mondizungulira ndikupereka pemphero lachidule, kuika ife ndi mtsogolo mwathu m’manja mwa Yehova ndikupempha kaamba ka nyonga kuti tipirire masiku omadzawo. Zinali ngati kuti ndalasidwa pamkono ndi jekeseni imene yandisintha kuchokera ku chidole chazigamba kukhala mayi wochilikiza.—Judith Leibensperger.

[Bokosi patsamba 15]

Zikumbukiro za Atate

Mwana wanga wamkazi, Bethel, anali mphatso yochokera kwa Mulungu mochedwerako m’moyo. Tinali ndi unansi wathithithi wonga umene timaŵerenga m’mabukhu. Kuyambira pamene Bethel anali khanda, tinali kuchita zirizonse pamodzi. Tinkapita m’minda kukaphunzira zaluso zokongola za Yehova Mulungu pamene tinkayang’ana maluŵa amtchire. Tinkapanga anthu ndi chipale chofewa. Tinkalankhula za zinthu zakuya ndiponso zopusa. Tinkagwada popemphera panthaŵi yogona limodzi naye atavala zovala zogona nazo ali pakati pa amayi ake ndi ine. Tinkachezera okalamba ndi osoŵa limodzi. Tinakupatira Mboni zinzathu zochokera ku maiko akutali. M’nyumba mwathu tinkachezetsa amishonale ndi amuna ndi akazi odzipatulira koposa kutumikira Mulungu m’mapazi a Yesu Kristu. Tinagawana chikhulupiriro chathu chimodzi, ndipo tinagawana maloto athu a Paradaiso. Iye anakula kukhala wokonda anthu ndipo wofuna kukondedwa nawo. Moyo wathu monga banja unali wabwino—kufikira tsopano. ‘Nthaŵi ndi mwaŵi’ zimene Mlaliki ananena kuti zimagwera anthu onse zinatigwera. M’tsiku limodzi vuto lamatenda limeneli linadzetsa nthunzi wakuda. Popanda chenjezo, chizimezime cha imfa—mdani wamkulu wa munthu—chinali pa ife.—Charles Leibensperger.

[Chithunzi patsamba 16]

Bethel ndi makolo ake kanthaŵi pang’eono asanapite ku opareshoni yachiŵiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena