Lingaliro la Baibulo
Pemphero m’Maseŵera Kodi Mulungu Amamvetsera?
MPWEYA umanjenjemera ndi chikondwerero pamene zikwizikwi za ochemerera zikukhamukira m’sitediyamu, akumakuwa mochilikiza timu yawo yokondeka. Oseŵerawo angomaliza kumene maseŵera otenthetsa thupi, ndipo pinto yoyambira seŵerolo yatsala pang’ono kulira. Kumbali imodzi ya bwalolo, oseŵerawo awunjikana pamodzi, ndipo pakatipo pali kaputeni wawo wogwada pansi, amene akupemphera kuti: “Mulungu, chonde dalitsani timu yathu, tipatseni chilakiko pa olimbana nawo athu, ndipo tichinjirizeni ku kuvulala. Amen.” Gululo likubalalika ndi kufuula kokweza, oseŵerawo akukhala m’malo mwawo pa bwalolo, pinto yalira, ndipo mpira wolinganizidwa wa ku America wayambika.
Pemphero la munthu payekha ndi la timu kuchiyambi, mkati, ndi pamapeto pa kutengamo mbali m’maseŵera osiyanasiyana lakhala chochitika cha nthaŵi zonse. Koma kodi Mulungu amamvetsera? Kapena monga mmene ena amatsutsira, kodi zimenezi zimasuliza pemphero?
“Phwanya Mnansi Wako”
Pa dziko lonse, maseŵera aliwonse aipitsidwa ndi chiwawa—pa bwalo ndi m’masitandi. Yemwe kale anali katswiri woseŵera mpira mu United States analemba kuti: “Nchotsutsika kuti kuphwanya thupi ndiko nsonga yeniyeni ya mpira, monga mmene kupha ndi kupundula ziriri mu nkhondo.” Akuchitira ndemanga mowonjezereka kuti: “Kuvulaza kolinganizidwa, kopikisanitsa ndiko maziko a njira yathu ya moyo, ndipo mpira uli umodzi wa akalilore aluntha . . . otisonyeza mmene chiriri chosangalatsa ndi chopatsa mphotho Kuphwanya Mnansi Wako.”
Kuphwanya mnansi wako? Yesu ananena zokonda mnansi wako. (Mateyu 22:39) Nchosalingalirika kuti Mulungu wachikondi angakhalepo ndi kudalitsa chimodzi cha zochitika zamaseŵera alerolino, okhala ndi chigogomezero pa kupambana pa mtengo uliwonse.—1 Yohane 4:16.
Kodi Mulungu Amapezekapo pa Zochitika Zamaseŵera?
Nsonga ina yolimbikitsira pemphero m’maseŵera ndi chiphunzitso chachipembedzo chakuti Mulungu amapezeka ponseponse, kuti Mulungu, pa nthaŵi zonse, amakhalapo pa malo onse amene alipo ndi m’zinthu. Mwachitsanzo, m’bukhu lakuti God Goes to Football Games, mtsogoleri wachipembedzo ndi yemwe kale anali wansembe wa timu yamaseŵera L. H. Hollingsworth akunena kuti: “Chikhulupiriro chirichonse chimene tiri nacho chonena za Mulungu chimaphatikizapo lingaliro la kukhalapo Kwake ponseponse; ngati mungakonde, lingaliro lakuti Iye alipodi pa chimene timachitcha chokumana nacho chathu chakudziko . . . Uku ndi kuti, Mulungu amapita ku tchalitchi, ndipo Mulungu amapita kumaseŵera a mpira.”
Komabe, Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu amakhala ponseponse. Mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: ‘Kristu analoŵa . . . m’mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.’ (Ahebri 9:24) Pali nsonga ziŵiri zofunika zimene lembali likutithandiza kuwona: kuti Mulungu ali munthu wauzimu ndipo kuti anakhazikitsa malo ake okhalako, kumwamba. (1 Mafumu 8:49; Yohane 4:24) Chotero sangakhale ku malo ena aliwonse pa nthaŵi imodzi.
Mulungu Amamva Mabwenzi Ake
Chabwino, ngati Mulungu sapezekapo pa zochitika zamaseŵera, kodi amamvetsera ku mapempherowo? Kuti mapemphero afike kwa Mulungu wakumwamba ameneyu, kwa amene Yesu anawonekera, wopempherayo ayenera kukhala ndi chidziŵitso, chidziŵitso cha zifuno za Mulungu, umunthu wake, mikhalidwe yake, njira zake, ndi dzina lake. (Yakobo 4:3) Akumagogomezera kufunika kwa kudziŵa Mulungu, Yesu anapemphera kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha.”—Yohane 17:3.
Kuti mudziŵe winawake mumafunikira kulankhulana. Mulungu amalankhula ndi anthu kupyolera m’Baibulo, ndipo Baibulo ndilo njira mwa imene timadziŵira Mulungu wakumwamba. Limatiuza dzina lake, Yehova. (Salmo 83:18) Baibulo limanenanso kuti Mulungu anakonda dziko kwambiri kotero kuti anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, Yesu, pano pa dziko lapansi kotero kuti munthu akhale ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha. (Yohane 3:16) Pamene tikuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, Yehova amakhala weniweni kwa ife, ndipo timakokeredwa kufupi naye kupyolera mwa Yesu. (Yohane 6:44, 65; Yakobo 4:8) Chifukwa chakuti Yehova ali weniweni, tingakulitse unansi waumwini wathithithi ndi iye.
Komabe, ubwenzi ndi Mulungu umaloŵetsamo kulankhulana kwa njira ziŵiri. Zimenezi zimafunikira kulankhula kwa Yehova m’pemphero. Baibulo likunena kuti Mulungu ndiye “Wakumva pemphero” ndipo kuti “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Salmo 65:2; Machitidwe 17:27) Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu amamva mapemphero onse. (Yesaya 1:15-17) Kodi ndi mapemphero andani amene Mulungu ali wofunitsitsa kuwamva?
Wamasalmo Davide anati: “Chinsinsi cha Yehova chiri kwa iwo akumuopa Iye.” (Salmo 25:14) M’Chihebri choyambirira, tanthauzo la “chinsinsi” (sohd) limatanthauza “kulimbitsa.” Chotero, vesi limeneli likupereka lingaliro lakuloledwa kuloŵa m’bwalo lamkati la Yehova kapena m’pangano laubwenzi ndi iye. Kokha alambiri awo amene amasonyeza ulemu woyenera amaloledwa kuloŵa. Motero, ubwenzi wathu wathithithi ndi Mulungu umatipangitsa kuwopa kusokoneza unansi woterowo mwakuchita chirichonse chimene sichingamkondweretse, monga ngati kuwona pemphero monga matsenga otsimikizira chilakiko pamaseŵera.
Yehova amamvetsera ku mapemphero a anthu owona mtima amene amafunafuna ubwenzi naye, ndipo iye alibe tsankho. Iye samayanja kapena kulemekeza gulu la mtundu wina, fuko, kapena timu ya maseŵera, kuposa lina. (Salmo 65:2; Machitidwe 10:34, 35) Ngati Mulungu anamvadi mapemphero a opikisana pa maseŵera ndipo matimu aŵiriwo anapemphera kwa iye kaamba ka chilakiko, kodi ndi iti imene angadalitse? Kapena ngati woseŵera anavulazidwa kowopsya mkati mwa maseŵera, kodi Mulungu ayenera kukhala ndi liŵongo?
Chotero, tiyenera kupempherera zinthu zolondola. Mtumwi Yohane akulongosola zimenezi motere: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Yehova amamvetsera mapemphero amene ali ogwirizana ndi chifuniro chake. Tiyenera kudziŵa chifuniro chake ndi zolinga kotero kuti mapemphero athu akhale ogwirizana ndi zimenezi.
Chifuniro cha Mulungu ndi zolinga ndi dzina lake laulemerero sizogwirizana ndi zochitika zamaseŵera zopikisana ndipo zachiwawa zalerolino. Mulungu alibe tsankho. Chotero, pamene mapemphero aperekedwa pa zochitika zimenezi, kodi Mulungu akumvetsera? Ndithudi ayi!