Kodi Mulungu Amachirikiza Mbali Iliyonse m’Maseŵera?
WOPAMBANA mumpikisanao wothamanga agwada pansi ndi kuchita majesicha akupemphera, akumapereka chiyamikiro kaamba ka chipambano chake. Komabe, tiyenera kulingalira kuti othamanga ena mumpikisanowo nawonso anapemphera kwa Mulungu kuti apambane—koma analephera.
Ochita mpikisano wankhonya aŵiri agwada m’ngodya ziŵiri zoyang’anizana za bwalo lankhonya asanayambe gawo loyamba la kumenyana kwawoko. Onse aŵiriwo akuchita jesicha la mtanda, mtundu wa pemphero lakachetechete kwa Mulungu lopempha chipambano. Ndiyeno winayo akantha mnzake namgonjetsa. Pakumenyana kwina, mwina wankhonya mmodzi yekha ndiye angapemphe chilakiko kwa Mulungu, komabe kaŵirikaŵiri iye nkumamenyedwa.
M’maseŵera a matimu, magulu a oseŵera angapemphere maseŵera asanayambe, mkati mwake, ndipo ngakhale pambuyo pake. Mwachitsanzo, mkati mwa timphindi tomalizira ta mpikisano wampira wotchedwa American Super Bowl, wogoletsa anaima chile akumayembekezera kugoletsa chigoli chimene chikapambanitsa timu lake kapena kulilepheretsa ngati akaphonya. Pambuyo pake wogoletsayo anati: “Ndinali kupempherera chigolicho.” Koma ena a timu lopikisana nalo analinso kupemphera—kuti alephere kugoletsa.
Ngakhale kuti mbali ziŵirizo zingapemphere, mbali imodzi iyenera kugonjetsedwa. Ngakhale timu lomwe lapambana limene oseŵera ake anapempherera chilakiko likhoza kugonjetsedwa m’maseŵera otsatira. Ndithudi, potsirizira pake, pakutha kwa nyengo ya mpikisano, matimu ena onse ayenera kugonjetsedwa, pakuti payenera kukhala timu limodzi lokha lopambana onse. Komabe, oseŵera a matimu ochuluka ogonjetsedwawo anali atapempherera chilakiko.
M’nkhani ya mutu wakuti “Chonde, Lekani Mapemphero Anu,” wolemba m’danga nkhani za maseŵera analemba kuti: “Kokha chifukwa chakuti mumalankhula mwamphamvu modzionetsera za unansi wanu ndi Mulungu, sikumatanthauza kuti zili zowona. . . . M’nkhondo Yadziko II, asilikali Achijeremani anali ndi malamba olembedwapo kuti: Gott mit uns. Matembenuzidwe ake ngakuti: ‘Mulungu ali nafe’” Wolemba za maseŵera wina anati: “Mulungu samachirikiza mbali iliyonse m’maseŵera ampira. Zinthu za pakanthaŵi zonga zimenezi zimagamulidwa ndi amuna ndi akazi, osati Wamphamvuyonse.”
Mtumwi Petro analemba kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Kudziloŵetsa m’maseŵera achiŵaŵa sindiko ‘kuchita chilungamo.’ (Machitidwe 10:34, 35; Aroma 14:19) Ngati Mulungu anamva mapemphero a awo opempherera chilakiko ndipo wochita mpikisanowo nkuvulala kapena ngakhale kufa, kodi Mulungu akakhala ndi liwongo?
Mawu a Mulungu amanena kuti: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Kuti mapemphero ayankhidwe, munthu ayenera kudziŵa chifuniro cha Mulungu ndi zolinga zake, ndipo zochita za munthuyo ziyenera kugwirizana ndi zimenezo.—Yerekezerani ndi Mateyu 6:9, 10.
Ayi, chifuniro cha Mulungu ndi zolinga zake zilibe chochita chilichonse ndi zochitika zamaseŵera. Chotero, pamene mapemphero a chilakiko aperekedwa pazochitikazo, kodi Mulungu amamvetsera? Kutalitali!
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
UPI/Bettmann