Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 6/8 tsamba 3-5
  • Kodi Makhalidwe Abwino Akubwereranso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Makhalidwe Abwino Akubwereranso?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkubwereranso Kwa Makhalidwe Abwino?
  • Machitidwe Asintha—Osati Makhalidwe Abwino
  • Kodi Phunziro la Makhalidwe Abwino Laphunziridwa?
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingapeŵere Kutenga AIDS?
    Galamukani!—1993
  • AIDS ndi Makhalidwe
    Galamukani!—1986
  • Aids Kodi Idzatha Motani?
    Galamukani!—1992
  • AIDS—Kodi Ndili Paupandu?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 6/8 tsamba 3-5

Kodi Makhalidwe Abwino Akubwereranso?

NYUMBAZO ziribe anthu. Zikwangwani zikunena kuti zaikidwa kaamba ka lendi. Nyumba zimenezo mu Hamburg, Jeremani, kalelo zidali mbali ya malo aakulu koposa a dziko a akazi achigololo. Kodi zinatsekedweranji?

Kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho chimene malo osiyanasiyana otchuka okumanirako anthu ogonana ofanana ziŵalo a mu San Francisco anathaŵidwira. Mu United States monse, makalabu ambiri ndi malo osambira anthu ogonana ofanana ziŵalo anatseka zitseko zawo imodzi ndi imodzi.

Kodi nchiyani kwenikweni chimene chinapangitsa masinthidwe ameneŵa? Kufalikira kwa AIDS, kachirombo kakupha kamene kakhala kamodzi ka miliri yoipitsitsa ya zaka za zana la 20.

AIDS yapha kale miyoyo zikwi makumi ambiri. Ndipo ngati ziyerekezo zaposachedwapa zitsimikizira kukhala zowona, ingatenge mamiliyoni a miyoyo yowonjezereka mtsogolo posachedwapa.

Kodi Nkubwereranso Kwa Makhalidwe Abwino?

M’ma 1960 ndi m’ma 70, kusinthanso m’zakugonana kunakuta maiko ambiri a Kumadzulo. Chikondi chaufulu chinakhala cholandirika mofala. Chiŵerengero cha kubadwa kwa ana akunja kwa ukwati chinawonjezeka. Msinkhu wa awo okhala ndi unansi wakugonana kwa nthaŵi yoyamba unali wotsika kwambiri. Mapindu amwambo anazimiririka m’miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri, ndipo chiŵerengero chawo chinali kukula mofulumira.

Polankhula za mzimu wofalikira pa nthaŵiyo, magazine a ku Canada L’Actualité analengeza kuti: “Mchitidwe wa kugonana unakhala seŵero losavulaza.” Pa nthaŵi imodzimodziyo, pokhala ndi kuyambika kwa magulu omenyera “zoyenera” za ogonana ofanana ziŵalo, kugonana kwa ofanana ziŵalo kunakhala nkhani yotchuka, ndipo masinthidwe anapangidwa m’malamulo amene kalelo analetsa kugonana kwa ofanana ziŵalo.

Pamenepo AIDS inayambika padziko. Pamene imfa zochititsidwa ndi mliri wamakonowu zinawonjezeka ndipo mankhwala sanapezeke, mkhalidwe wa anthu kulinga ku kugonana unasintha mokulira. Monga mmene L’Actualité inalongosolera kuti: “Ndi AIDS, maseŵera ogonana akhala owopsya kwambiri.” Mtolankhani wa ku Amereka Ellen Goodman anathirira ndemanga pa kusintha kwa mkhalidwe kumene kunatanthauzidwa: “Pamene—osati ngati koma pamene—AIDS ikufalikira kwa anthu onse, kunena kuti ‘toto’ kudzakhala yankho lofala ku kugonana.”

Machitidwe Asintha—Osati Makhalidwe Abwino

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tikuchitira umboni kuzindikira kwina kotulukapo chifukwa cha kubwerera ku makhalidwe abwino? Monga mmene ofalitsa nkhani anenera nthaŵi zina, kodi ndiko “kubwezedwanso kwa miyambo ya makolo” kapena kwa “chiyero cha makhalidwe”?

Machitachita ena angosintha chifukwa chakuti anafunikira kusintha, koma kulingalira kolama sikunatsatire kusintha kumeneko. Mwachitsanzo, ogonana ofanana ziŵalo amene anasiya kugonana ndi anthu ambiri ndi kulekezera ku kugwirizana kwa “munthu mmodzi” sanganenedwe konse kuti akubwerera ku makhalidwe abwino. Kuwonjezerapo, kodi chingachitike nchiyani katemera wa AIDS atapezeka? Pali chifukwa chokhulupirira kuti ambiri angabwerere ku machitachita awo akale ndipo kuti malo okhazikitsidwa angatsegulidwenso.

Kwa ogonana osiyana ziŵalo, kusintha kwa mkhalidwe, koma osati m’kulingalira kolama, kungawonedwenso. Felice, wophunzira pa University of California mu Los Angeles, U.S.A., akudandaula chifukwa chosakhala ndi ufulu wa kugonana umene udali wofala pa kolejipo. Iye adati: “Zimadzutsa mkwiyo. . . . Ndinakhumbadi kukhala ndi ufulu wopanga zosankha zangazanga.” Ndipo mtolankhani wa ku Amereka analongosola kuti miyezo ya makhalidwe abwino yakaleyo singayambikenso, akumati: “Pamene kuli kwakuti kusintha kwa zakugonana kungakhale kukuchedwa, palibe kubwerera kotheratu ku kulingalira kukwatirana musanagonane kwa m’ma 1940 ndi m’ma 50.”

Mwachitsanzo, mu Canada, magazine a Maclean’s anasimba zotsatirazi ponena za kufufuza kolipiriridwa ndi boma kwa ophunzira a pa koleji: “Achichepere akulu msinkhu molingalirika amakhala odziŵitsidwa bwino lomwe za matenda opatsirana mwakugonana, kuphatikizapo AIDS, chindoko ndi chinzonono. Koma chidziŵitso choterocho mwachiwonekere chalephera kuwapanga kukhala osamala. Ophunzira ambiri ofufuzidwa ananena kuti anakhalapo ndi unansi wakugonana, koma anavomereza kuti sanasamale kutenga kachitidwe kochinjiriza kamodzi kamene kamathandiza kupeŵa matendawo: kugwiritsira ntchito condom.”

Lipotilo linanenso kuti: “Akuluakulu ambiri a zaumoyo amanena kuti ali odera nkhaŵa kuti, mosasamala kanthu za kufalitsidwa kwa kugonana kwachisungiko, uthengawo sukuyambukira mbali ya anthu okangalika m’zakugonana.” Dr. Noni MacDonald, katswiri wa matenda opatsirana wa ku Ottawa anati: “Ndawala zambiri zamaphunziro ndi za ofalitsa nkerani zowonjezera kugwiritsira ntchito condom zikulephera kotheratu.”

Maclean’s inawonjezera kuti: “Kufufuza kwa m’makoleji 54 kunapeza kuti makota atatu a ophunzira anali atagonanapo kale. Chifupifupi theka la amunawo ananena kuti anali ndi ogonana nawo asanu kapena kuposapo, ndipo kota inanena kuti chiwonkhetsocho chinali 10 kapena kuposapo. Pakati pa akazi akukoleji ofufuzidwa, 30 peresenti ananena kuti anakhala ndi unansi wakugonana ndi chifupifupi ogonana nawo asanu; 12 peresenti ananena kuti anatero ndi pafupifupi amuna 10. Komabe, macondom sanali ofala motchuka. . . . Awo amene anali apangozi koposa mwachiwonekere sanagwiritsire ntchito macondom.”

Kodi Phunziro la Makhalidwe Abwino Laphunziridwa?

Ambiri amakana kutenga phunziro la makhalidwe abwino kuchokera ku zimene zikuchitika. Adokotala ena amavomereza kusintha zizoloŵezi, akumayamikira kuti ayenera kukhala ndi wogonana naye mmodzi yekha ndi kugwiritsira ntchito macondom kuti apeŵe AIDS. Koma amathaŵa kutsutsiratu mkhalidwe wachiŵereŵere. Alan Dershowitz, profesa wa lamulo pa Harvard, ndiye woimira wa chikhoterero chimenechi pamene akulingalira kuti ofufuza sayenera kukaikira mbali ya makhalidwe abwino ya mkhalidwe wa kugonana umene umafalitsa AIDS. Iye analongosola kuti: “Asayansi ayenera kuchita ngati kuti matendawo amapatsiridwa ndi mkhalidwe wachete.”

Komabe, magazine Achifrenchi Le spectacle du monde akupereka ganizo lakuti zimenezi nzosakwanira. Iwo anati: “Palibe lamulo lolimbana ndi AIDS limene lidzakhala ndi chiyambukiro chirichonse kusiyapo kokha ngati latsagana ndi kubwerera kodzifunira, kofulumira, ku mtundu wapamwamba wa makhalidwe abwino kwa dziko lonse. (Siziyenera kuiwalidwa kuti kulekerera chisembwere, dama, ndi kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa ndizo mikhalidwe yeniyeni ya chitaganya imene ili ndi thayo la kufalitsa matendawa.) Kubwerera ku makhalidwe abwino kumeneku kungachitike kokha ngati mkhalidwe wamwambo watsopano ubuka. . . . Makhalidwe abwino sali zotulukapo za kulingalira kotsatira munthu. Poyang’anizana ndi mliri wa AIDS, ayenera kutanthauzidwa kukhala choyenera cha moyo ndi kakhalidwe pachimene chipulumuko cha mtundu wa anthu chikudalira.”

Kodi makhalidwe abwino ayenera kuyambidwanso monga “choyenera cha moyo ndi kakhalidwe”? Kodi kutengera dongosolo la mapindu a makhalidwe abwino kuyenera kuperekedwa ndi mikhalidwe yokha? Kodi malamulo onse a makhalidwe abwino ali ndi phindu lofanana? Tiyeni tiwone maphunziro amene mbiri ingatiphunzitse.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“PALIBE KUBWERERA KOTHERATU KU KULINGALIRA KUKWATIRANA MUSANAGONANE KWA M’MA 1940 NDI M’MA 50”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena