Mabuku Aulere
MANYUZIPEPALA aulere mu Briteni akubweretsa ndalama zosatsira malonda madola mamiliyoni mazana angapo m’kufalitsidwa kwa makope ake mamiliyoni makumi ambiri pamlungu. Zotulukapo zake zaposadi kutalitali kalambula bwalo wochepa amene anakundika zaka 20 zapitazo. “Anthu anaseka lingaliro la kusatsira malonda m’chinthu chaulere,” anatero Ian Locks, mtsogoleri wamkulu wa Association of Free Newspapers. Koma, kwenikweni, “iyo yayamba kugaŵira manyuzipepala ake onse mwaulere, magazine ndi timabuku monga mtundu watsopano wa mwaŵi wa zamalonda,” iye waonjezera tero.
Magazinenso? Inde. Magazine osiyanasiyana oposa 400 amagaŵiridwa mwaulere mu United Kingdom, amagaŵiridwanso mamiliyoni makumi ambiri. Mtengo wake wochepa wakoka osatsa malonda a manyuzipepala a kumaloko, kumene ambiri a awa akugaŵiridwa aulere. The Times ya ku London ikufotokoza kampaniyi kukhala “magwero amphamvu atsopano mu indasitale yofalitsa ya ku Briteni,” yomwe idzakhalitsa.