“Simlandu Wanga!”—Mbadwo wa Kudzikhululukira
GWEBEDE! Atamva tero Amayi a Johnny wachichepere athamangira m’kitchini kukawona chimene chapangitsa phokoso lodzidzimutsalo. Atafikamo, apeza zidutswa za mbale ya mabisiketi ziri mbwee pansi. Johnny ali chiimire potero, atagwira bisiketi mwamantha m’dzanja lake ndikuyesera zolimba panthaŵi imodzimodzi kuwoneka wopanda liŵongo. “Simlandu wanga!” iye akufuula motero.
MAKOLO amadziŵa bwino lomwe kuti ana amakupeza kukhala kovuta kuvomereza liwongo la zolakwa zawo. Koma akulu a m’chitaganya lerolino ali ndi vuto limodzimodzilo. Anthu owonjezerekawonjezereka amawonekera kukhala akukhulupirira kuti msampha wa kudzisangalatsa okha ngwosatheka kuyembekezera kuuletsa.
Mwachitsanzo, talingalirani mwamuna wina amene anagwirira chigololo mkazi mmodzimodzi katatu. Iye anaumirira pakuzengedwa mlandu kwake kuti anali mnkhole wa magwero ake aubwamuna; iye anali ndi chilakolako chopambanitsa chakugonana. Anamasulidwa. Wandale zadziko amene anagwidwa akunama anatulira liwongo lake la kunena bodza pa vuto lake la zoledzeretsa. Mbala yoba mankhwala m’maiko ena inamasulidwa pamene inati inali mnkhole wa “vuto losakhoza kudziletsa.”
Mogwirizana ndi U.S.News & World Report, magulu oposa 2,000 amakumana mlungu uliwonse kupereka uphungu kwa odzilingalira kukhala omwerekera m’chikondi kapena kugonana. Magulu oposa 200 a m’dzikolo akhazikitsidwa odzitcha Alcoholics Anonymous (Zidakwa Zosatchedwa Maina) kuti athandize “minkhole” ya “zomwerekeretsa” zina, monga Batterers Anonymous (Omenya Anthu Osatchedwa Maina), Gay Men’s Overeaters Anonymous (Omwerekera m’Ntchito Osatchedwa Maina), Gamblers Anonymous (Otchova Njuga Osatchedwa Maina), Debtors Anonymous (Angongole Osatchedwa Maina), Messies Anonymous (Auve Osatchedwa Maina), ndi Workaholics Anonymous (Omwerekera M’zizoloŵezi Osatchedwa Maina).
Akatswiri ena amavomereza lingaliro lakuti mitundu yonseyi ya mkhalidwe wowononga ingakhale yomwerekeretsa, koma ena akuchititsidwa kakasi ndi mtundu watsopano umenewu wa kumwerekera. Monga momwe katswiri wa zamaganizo wina ananenera kuti: “Kupanga dziko la matenda a kumwerekera kungatanthauze kupanga dziko m’limene chirichonse chingakhululukiridwe.” Katswiri wina wochiritsa maganizo akuchenjeza kuti pamene anthu adzitcha okha kukhala minkhole ya kumwerekera yosachiritsika, amakhala ovuta kwambiri kuthandiza; chodzikhululukira chawo chimakhala mbali yawo.
Dr. William Lee Wilbanks, profesa wa chilungamo paupandu, akugomeka kuti kachitidwe kotchuka kamakono ndi thandizo la kuchiritsa kumwerekerako ndizo mbali ya nthanthi ya mawu anayi yakuti “I cannot help myself” (Sinditha kudziletsa), imene akuitcha Chamanyazi Chatsopano. Iye anatsutsa kotheratu “chizoloŵezi chomakulakulabe m’chitaganya cha sayansi cholingalira anthu kukhala zinthu zimene zikusonkhezeredwa ndi mphamvu zamkati ndi zakunja zimene anthuwo sakhoza kuziletsa.” “Lingaliro limeneli,” iye akuwonjezera motero, “limapereka lingaliro lakuti mphamvu zakudzisankhira zimachita mbali yochepa kapena sizimachita mbali iriyonse mumkhalidwe wa munthu.”
Kufufuza kwapereka lingaliro lakuti mphamvu yakudzisankhira ya munthu iri ndi chisonkhezero champhamvu ngakhale pa miyambo yomwerekeretsa kwambiri kuposa ndimmene zinalingaliridwa. Mwachitsanzo, pafupifupi 75 peresenti ya omwerekera ndi heroin amalephera kuleka chizoloŵezi chawo. Koma pakati pa amene kale anali asilikali a Nkhondo ya Vietnam, chiŵerengero cha opambana nchachikulu koposa—pafupifupi 90 peresenti akukhoza kuleka. Chifukwa ninji? Mankhwalawo ngamodzimodzi, ndi kumwerekerako nkofanana. Kodi chingakhale chifukwa chakuti, monga momwe Wilbanks akulingalirira, kuti “dongosolo lawo la makhalidwe abwino ndi kudzilanga zinawathandiza ‘Kunena Kuti Ayi’”? Sikuti zinthu zonga kudalira pa mankhwala kapena chizoloŵezi chachibadwa kulinga ku mavuto ena sizenizeni. Monga momwe Wilbanks akunenera, zinthu zoterozo “zingapangitse nkhondo yachiyeso kukhala yovutirapo. Koma nkhondoyo ingapambanidwebe.”
Ndithudi ingatero. Msampha wa kudzisangalatsa kwa panthaŵi yomweyo ungakhale wamphamvu, koma siwamphamvu yonse. Monga momwe ntchito ya Mboni za Yehova yasonyezera padziko lonse, omwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa, zidakwa, achigololo, otchova njuga, ndi ogonana ofanana ziŵalo satofunikira kusangalatsa zikhumbo zawo. Pogwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kudzisankhira ndipo, kwakukulukulu, ndithandizo la mzimu woyera wa Mulungu, iwo angathe ndipo amalaka mavuto awo. Chotero, mosasamala kanthu ndizimene “akatswiri” akunena, Mlengi wathu amadziŵa pamene timakhala ndi thayo la machitidwe athu. (Numeri 15:30, 31; 1 Akorinto 6:9-11) Koma iye alinso wachifundo. Samayembekezera zopambana pa zimene tingathe, ‘akumbukira kuti ife ndife fumbi.’—Salmo 103:14.