Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 2/8 tsamba 5-7
  • Minkhole Iyang’anizana ndi Aliŵongo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Minkhole Iyang’anizana ndi Aliŵongo
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Minkhole
  • Waliŵongo
  • Kumaliza kwa Bungwe
  • Kodi Wolakwa Ndani?
    Galamukani!—1991
  • Msanganizo Wakupha
    Galamukani!—1991
  • Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?
    Galamukani!—2002
Galamukani!—1991
g91 2/8 tsamba 5-7

Minkhole Iyang’anizana ndi Aliŵongo

MPHALAYO idachitikira pa: Bungwe la Minkhole ya ku Upper New York State’s Genesee County DWI. Chochitikacho: Anthu asanu ndi mmodzi, ogwirizana pamodzi chifukwa cha chisoni chomwe onsewo ali nacho atagwirira zithunzi za okondedwa awo m’manja, akukhala ndi phande m’kuyesayesa kotopetsa kofuna kuzindikiritsa ogwidwa ndi liŵongo la kuyendetsa galimoto ali oledzera.

Omwe akutsatira pansipa ndimawu ofotokozedwa ndi iwo, osonkhanitsidwa ndi Galamukani!

Minkhole

Bambo: “Uyu ndimwana wathu Eric. Anali mwana wapamtima, wolama kwambiri, womwetulira nthaŵi zonse. Tsopano ndakhala bambo wachisoni, amene mwana wanga wa zaka 17 wandisiya. M’kamphindi kochepa kokha, zolinga zathu zonse zinatheratu, ziyembekezo zathu zamtsogolo, chikondi chathu—anaphedwa ndi woyendetsa galimoto wokhuta mowa.

“Ndimapita ndimkazi wanga kumanda. Ndicho chinthu chomalizira chimene tiyenera kumamatirako. Tinaŵerenga mawu a Eric ozokotedwa pamandapo akuti: ‘Ndidzakulakalakani ndi mtima wanga wonse, ndipo ndingoganizira kuti sitidzatalikirana kwambiri; ndipo ngati tidzatero, ndidzalira pakuti sindinafune konse kunena kuti tsalani bwino.’ Ndipo nafenso sitikufuna kunena kuti upite bwino mpang’ono pomwe.”

Mkazi wamasiye wachichepere: “Ili ndibanja langa. Mwamuna wa zaka 22 zakubadwa anachoka paphwando laukwati nati sanaledzere. Ali m’galimoto lake, akumayendetsa mwaliŵiro zedi mumsewu woipa, womwe sanauzolowere, anapeza chikwangwani chochenjeza nachinyalanyaza, kenaka nankabe nakapyola chizindikiro choti imani natigunda. Chomwe ndikukumbukira nchakuti ndinadzuka ndikumva kupweteka kwambiri m’chifuwa mwanga. Pamene ndinavutikira kutsegula maso anga, ndinakwanitsa kuwona mwamuna wanga atatsinyidwa kuchowongolera galimoto. Ndinamva khanda langa likulira. Ndikumbukira kuti ndinafunsa kuti, ‘Kodi chachitika nchiyani?’

“Palibe munthu anandiyankha. Bill, mwamuna wanga, wa zaka 31 zakubadwa; mwana wanga wamwamuna wamkulu, wa zaka 6; ndi anyamata anga amapasa, a zaka 4, anafa. Yemwe ndinayembekezera yekha anali mtsikana wanga wamng’ono wa miyezi isanu ndi inayi yakubadwa, yemwe anaikidwa m’chipatala chifukwa cha kuvulala koipa m’mutu.

“Ndidakali m’chipatala wokhwethemulidwa, pa Lachitatu mmawa, mwamuna wanga ndi anyamata atatuwo anaikidwa mmanda. Ndinavutika ndi kuganizira za mabokosi amaliro anayi, mitembo yophwanyika inayi, anthu anayi omwe sindidzawonanso, kumva, kapena kuŵakhudza. Kodi ndikadapirira nazo bwanji?

“Ine ndi mwana wanga wamkazi wamng’ono tinakakamizidwa kuyamba umoyo watsopano. Ndinagulitsa nyumba yanga, popeza kuti ndinalephera kupirira ndi zokumbukira. Mfundo yakuti mwamuna wanga ndi anyamata atatu okongola ali mmanda imandivuta kuchita nayo. Chisamaliro, nkhaŵa, chikondi zonsezo sizinali zokwanira kuŵatetezera. Kukhumudwitsidwa, kugwiritsidwa mwala, ndikusukidwa komwe ndimakumva sikungafotokozeke. Iwo anakhala ndimoyo kwa nthaŵi yaifupi chotero.

“Munthu yemwe anapha ziŵalo zabanja langazi sanali wachifwamba woipa kapena chidakwa kapena kubwezera kwa waliŵongo wobwerezabwereza—anali munthu wamba pambuyo paphwando lamadzulo. Mtengo wovutawu ndikuwulipira chifukwa chakuti munthu wina anasankha kumwa ndikuyendetsa galimoto. Musalole ichi kukuchitikirani kapena kuchitikira munthu wina amene mumakonda.”

Mayi: “Dzina lamwana wanga wamkazi ndi Rhonda Lynn. Iye adafunikira kumaliza maphunziro a kusekondale pa June 21. Pa June 10 ankachita maphunziro ake a kuyendetsa galimoto omalizira. Patsikulo anthu aŵiri omwe ankachita phwando ndi kumwa mowa mopambanitsa anapanga chosankha choipa cha kuyendetsa galimoto. Pakanthaŵi kochepa, iwo analipanga kukhala tsiku lomalizira la moyo wa Rhonda, limodzinso ndi miyoyo ya mphunzitsi woyendetsa galimoto ndi amkalasi anzake aŵiri.

“Masana amenewo ndinalandira lamya yondidziŵitsa kuti Rhonda anali m’ngozi. Lomwe linali lingaliro langa lokha linali lakuti ndidafunikira kukakhala naye. Pamene ndinafika pachipatala, ndinauzidwa kuti ndisaloŵe kukamuwona Rhonda. Koma ndinafuna kutsimikizira. Ndinaŵachititsa kutsegula nsalu yochinga. Nkhope yake inali yotupa kwambiri ndiyokwalulidwa moipa. Ndinapitiriza kuyang’ana maso ake okongolawo ndikusisita mkono wake, koma sindinathe kuchititsa thupi lake lopwetekedwalo kukhala bwino. Chomwe ndinali wokhoza kuchita chinali kusisita tsitsi lake lobiriŵiralo. Sananyang’anye konse. Anali atamwalira.

“Ndinavutika kufotokozera atate wake ndi abale ake kuti wamwalira. Tsopano masiku athu saalinso chimodzimodzi chifukwa cha chinthu choipachi. Bwenzi ndidakangomkupatirako, kumsisitako pang’ono. Moyo wathu sudzakhalanso chimodzimodzi. Zomwe takhala nazo ndi zikumbukiro.”

Waliŵongo

Mnyamata: “Nkhani yanga njosiyana ndi zomwe mwazimva kale. Yanga idachitika miyezi 23 yapitayo. Ndimaikumbukira ngati kuti idachitika dzulo. Bwenzi langa lachikazi linkaseŵera mpira m’timu usikuwo, chotero ndinasankhapo kumwa pang’ono ndikumpenyerera akuseŵera mpirawo. Ndinamwa zikho za mowa zisanu kapena zisanu ndi chimodzi m’maola aŵiri ndi theka otsatirapo. Ndinalingalira kuti ndidali nazo mphamvu ndipo ndinayembekezera kwa ola limodzi ndisanayendetse galimoto kunka kunyumba.

“Nditayenda pafupifupi mphindi 30 paulendo wonka kunyumba, ndidawona ambulansi pamsewu, ndipo padali munthu pakati pamsewupo akusonyeza magalimoto kopita. Munthuyu ndinamuwonera pafupi kwambiri. Ndinayesa kuwongolawongala galimoto ndi kuponda mabuleki. Pamene galasi lakutsogolo linaphwanyika, ndidati ndekha: ‘Chonde akhale kasenye kapena galu!’ Koma ndinadziŵa kuti sanali chirichonse cha ziŵirizi. Ndinatuluka m’galimoto ndikunka komwe anali, ndikufuula kuti, ‘Kodi mulimoyo? Kodi mulimoyo?’ Sanandiyankhe. Ndikumbukira kuti ndinawerama, ndikumapenya nkhope yake. Inali yowopsa.

“Apolisi anabwera nandifunsa mafunso. Kenaka anati: ‘Ukuthandiza kwambiri, koma ukuyenda modzandiradzandira ndipo ukulankhula mwachilendo. Kodi umamwa mowa?’ Iwo anandipereka ku ofesi ya apolisi nandipima. M’thupi mwanga munapezeka mowa wokwanira 0.08 [kumwa zoledzeretsa kosaloledwa mwalamulo m’mbali zambiri za United States]. Sindinakhulupirire kuti izi zinkachitika kwa ine. Ndidalingalirapo kuti chinthu choterechi sichidzachitikapo kwa ine. Komabe, tsopano ndinkayang’anizana ndi mlandu wakupha munthu mosasamala wotchedwa, DWAI [Driving While Ability Impaired].

“Panatsala mwezi umodzi kuti ndipatsidwe satifiketi yanga yauphunzitsi. Tangolingalirani mmene chitaganya chimaŵalingalira aphunzitsi. Iwo amawayembekezera kukhala opanda mabanga mwamakhalidwe. Nchomwe ndinkagwirirapo ntchito, ndipo tsopano ndinkayembekezera kuchitaya.

“Ndinakhala waganyu kwa chaka chimodzi, ndinalandidwa laisensi yanga yoyendetsera galimoto kwa miyezi 19, ndinalipiritsidwa faindi ya madola 250, ndinaponyedwa m’ndende kumapeto a mlungu umodzi, ndinagwira ntchito ya m’mudzi kwa maola 600, ndipo ndinaloŵetsedwa m’kosi ya milungu isanu ndi inayi yolangiza za zakumwa zoledzeretsa. Kuposa apa, ndikumbukira usiku womwe ndinkadzidzimuka kutulo, ndiri ndi chithunzi cha nkhope ya munthu uja m’malingaliro. Ndipo ndidafunikira kubwerera kunyumba kukakumana ndi mabwenzi anga onsewo ndi banja. Zinawonekera kukhala zovuta kwambiri kupitirizabe ndi moyo wanga. Sindinatsimikizire kuti kunali koyenerera. Ndidafunikira kubwerera kukaphunzitsa ana a sukulu ndikupenya ana onsewo. Ndinalephera kudzithandiza koma ndinazizwa kuti ndi angati a iwo anadziŵa zimene ndinachita. Ndipo ndinagwidwa ndi liŵongo ndi kuipidwa kumene ndinali nako kulinga ku banja la munthu uja.

“Usiku umene ngoziyo inachitika, ndidafunikira kuchita chinthu chovuta kwambiri chomwe sindinachitepo m’moyo wanga—kuitana amayi anga ndikuwauza kuti, ‘Mayi, ndapha munthu m’ngozi. Ndifunikira kuperekedwa kunyumba.’ Pamene anafikako, tinangokupatirana ndi kulira. Sindingakhumbe mdani wanga woipa kwenikweni kukumana ndi zimene ndinakumana nazo. Anthu omwe amamwa ndi kuyendetsa galimoto—ndilo vuto limene ndikufuna kuŵathandiza nalo. Pamene muchoka pamsonkhano uno, pitani mukutikumbukira. Musatiiwale konse.”

Kumaliza kwa Bungwe

Patricia Johnston, mgwirizanitsi wa bungwe la minkholeyi, anamaliza ndi chokumana nacho chake chowopsa kwenikweni cha ngozi ya atate wake yochititsidwa ndi zakumwa zoledzeretsa. Iye anati: “Nditati ndisonkhanitse chisoni chimene zakumwa zoledzeretsa zimabweretsa ndikuika ‘chimodzi pamsewu,’ sipangafunikirenso programu yonga iyi!”

Pomalizira pake, tcheyamani anafunsa ngati padali aliyense yemwe anali ndi mafunso. Palibe omwe anafunsidwa. Koma padali ambiri omwe maso awo adali odzala ndi misozi omwe adati: “Simudzandiwonanso ine ndikumwa mowa ndikuyendetsa galimoto.”

Nthaŵi yokha njomwe idzaulula zotulukapo zimene mabungwe ameneŵa adzakhala nazo m’kuyambukira chiŵerengero chimene aliŵongo omangidwa abwereranso pamsewu akuyendetsa galimoto ataledzera. Koma chimene chikupangitsa vutoli kukhala lovutirako ndicho anthu ochuluka, mamiliyoni ambiri, omwe amapita pamsewu ali ofooka ndipo sakugwidwa.

Malipoti aposachedwapa ochokera ku Bureau of Justice Statistics ya U.S. Department of Justice anasonyeza kuti m’chaka chimodzi chaposachedwapa, pafupifupi anthu mamiliyoni aŵiri anamangidwa kaamba ka DUI (Driving Under the Influence). Koma ziŵerengero zinasonyezanso kuti pakumangidwa kulikonse kwa DWI (Driving While Intoxicated) kochitidwa, anthu okwanira 2,000 owonjezereka angapitirize osagwidwa m’madera osayang’aniridwa, anthuwa ngomwe adzachititsanso imfa zina.

Kodi nchiyani chachititsa mkhalidwe umene umapititsa patsogolo kachitidwe kakupha ndi kosasamala koteroko? Kodi nchifukwa ninji nkhondo yotsutsa kumwa ndi kuyendetsa galimoto idakapitirizabe kumenyedwa koma popanda chipambano? Tiyeni tisanthule mayankho ena.

[Chithunzi patsamba 7]

Kukhazikitsa lamulo la kulola aliŵongo kuyang’anizana ndi bungwe la minkhole

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena