Kodi Ndisiye Kuyendetsa Galimoto?
MWINA mwakhala mukuyendetsa galimoto kwa zaka zambiri. Mumasangalala kuyendetsa galimoto yanu komanso kupita kulikonse kumene mukufuna. Koma anthu am’banja lanu komanso anzanu amada nkhawa kuti mukhoza kudzachita ngozi ndipo angakonde mutasiya kuyendetsa galimoto. Komabe inuyo zikukuvutani kumvetsa chifukwa chake akuda nkhawa.
Kodi zimenezi ndi zomwe zikukuchitikirani inuyo? Ngati ndi choncho, n’chiyani chingakuthandizeni kusankha kuti mupitirizebe kuyendetsa galimoto kapena ayi?
M’mayiko ena, madalaivala akafika zaka zinazake amafunika akaonane ndi adokotala kuti apatsidwe chilolezo choti akhoza kutenganso laisensi yatsopano. Akhristu amene akukhala m’mayiko amenewa, amafunika kumvera malamulo amene boma linakhazikitsa komanso kutsatira zimene anthu amaudindo akunena. (Aroma 13:1) Koma kaya mumakhala kuti, pali zinthu zimene muyenera kuziganizira kuti mupitirizebe kuyendetsa galimoto motetezeka.
MUZIGANIZIRA MMENE MUMAYENDETSERA GALIMOTO
Mogwirizana ndi zimene bungwe lina la National Institute on Aging (NIA) la ku United States linanena, mukhoza kuyamba ndi kudzifunsa mafunso otsatirawa:
Kodi ndimavutika kuwerenga zikwangwani zapamsewu kapena kuona zinthu usiku?
Kodi ndikumavutika kutembenuza mutu wanga kuti ndiyang’ane magalasi komanso malo ena omwe akhoza kuchititsa ngozi?
Kodi ndikumavutika kuchita zinthu mofulumira, monga kuchotsa phazi langa pachopondera moto kupita pabuleki?
Kodi ndimayendetsa pang’onopang’ono kwambiri moti ndimasokoneza madalaivala ena?
Kodi nthawi zambiri ndimatsala pang’ono kuchita ngozi kapena kodi galimoto yanga inaphwanyika kapena kukalikakalika chifukwa chowomba zinthu zoti zangokhala?
Kodi apolisi amakonda kundiimitsa chifukwa cha mmene ndimayendetsera galimoto?
Kodi nthawi zina ndimasinza ndikamayendetsa?
Kodi pali mankhwala amene ndimamwa omwe akhoza kusokoneza mmene ndimayendetsera galimoto?
Kodi anthu am’banja langa kapena anzanga anadandaulapo za mmene ndimayendetsera?
Ngati mwayankha kuti inde pa funso lina kapena awiri, ndiye kuti mukufunika kusintha zinthu zina. Mwachitsanzo, mungasankhe kuti musamayendetseyendetse galimoto makamaka usiku. Nthawi ndi nthawi muziganiziranso mmene mumayendetsera galimoto. Mukhoza kupempha wachibale kapena mnzanu kuti akuuzeni mmene mumayendetsera galimoto. Mukhozanso kukonza zoti mukalowenso sukulu yokuthandizani kuyendetsa galimoto motetezeka. Komabe ngati mwayankha kuti inde pa mafunso oposa awiri, mungachite bwino kuganizira zosiya kuyendetsa galimoto.a
MUZILOLA KUTI MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIZIKUTSOGOLERANI
Nthawi zina sitingazindikire kuti luso lathu loyendetsa galimoto likulowa pansi. Ndipo mwina mukhoza kukhumudwa mukaganizira zoti mukufunika kusiya kuyendetsa galimoto. Ndiye kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni kuona zinthu moyenera n’kusankha zinthu mwanzeru? Tikambirana mfundo ziwiri.
Muzikhala wodzichepetsa. (Miy. 11:2) Anthufe tikamakula, maso athu, makutu komanso minofu zimayamba kufooka ndipo timavutika kuchita zinthu mwachangu. Mwachitsanzo, anthu ambiri akamakula amasiya kuchita masewera enaake olimbitsa thupi chifukwa amadziwa kuti akhoza kuvulala mosavuta. N’chimodzimodzinso ndi kuyendetsa galimoto. Pa nthawi ina munthu amene ndi wodzichepetsa angafunike kusiya kuyendetsa galimoto pofuna kuteteza moyo wake. (Miy. 22:3) Anthu ena akatiuza kuti ali ndi nkhawa ndi mmene timayendetsera galimoto, ngati ndife odzichepetsa tidzamvetsera n’kuchitapo kanthu.—Yerekezerani ndi 2 Samueli 21:15-17.
Muzipewa kukhala ndi mlandu wamagazi. (Deut. 22:8) Ngati munthu sakuyendetsa bwino galimoto, akhoza kupha kapena kuvulaza anthu. Ngati munthu akupitirizabe kuyendetsa galimoto, ngakhale kuti luso lake loyendetsera likulowa pansi, akhoza kuika moyo wake komanso wa anthu ena pangozi. Ndipo ngati atachita ngozi n’kuphetsa anthu, akhoza kukhala ndi mlandu wamagazi.
Musamaganize kuti anthu akhoza kusiya kukulemekezani kapena kukuonani kuti ndinu ofunika ngati mutasankha kusiya kuyendetsa galimoto. Yehova amakukondani chifukwa cha makhalidwe anu abwino monga kudziwa malire anu, kudzichepetsa komanso kuganizira moyo wa anthu ena. Ndipo iye akulonjeza kuti azikuthandizani komanso kukulimbikitsani. (Yes. 46:4) Iye sadzakusiyani. Choncho muzimupempha kuti akuthandizeni kugwiritsira ntchito nzeru komanso mfundo za m’Baibulo pamene mukuganizira zosankha kusiya kuyendetsa galimoto kapena ayi.
a Kuti mupeze mfundo zina zowonjezera, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?” mu Galamukani! ya September 8, 2002.