Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 November tsamba 2-7
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalalabe Ngakhale Kuti Ndinu Achikulire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalalabe Ngakhale Kuti Ndinu Achikulire
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUKHALA WACHIKULIRE KUNGAPANGITSE KUTI MUSAMASANGALALE
  • ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALABE
  • MMENE MUNGATHANDIZIRE ACHIKULIRE
  • Muziona Kuti Achikulire Okhulupirika Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Zimene Tikuphunzira pa Mawu Omaliza a Amuna Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 November tsamba 2-7

NKHANI YOPHUNZIRA 44

NYIMBO NA. 138 Imvi Ndi Chisoti Chaulemerero

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalalabe Ngakhale Kuti Ndinu Achikulire

“Atakalamba zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino.”—SAL. 92:14.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona chifukwa chake achikulire ayenera kupitiriza kukhala osangalala komanso mmene angachitire zimenezi.

1-2. Kodi Yehova amaona bwanji achikulire omwe ndi okhulupirika? (Salimo 92:​12-14; onaninso chapachikuto.)

PADZIKO lonse anthu amachita zinthu zosiyanasiyana akaona kuti akukula. Mwachitsanzo, kodi mukukumbukira zimene munachita mutaona kuti m’mutu mwanu mwayamba kumera imvi? Mwina munaganiza zongoizula aliyense asanaione. Koma munazindikira kuti kuzula imviko sikukanachititsa kuti imvi zina zambiri zisiye kumera. Chitsanzochi chikusonyeza kuti ambiri zimawavuta kuvomereza kuti akukula.

2 Koma kodi Atate wathu wakumwamba amaona bwanji atumiki ake achikulire? (Miy. 16:31) Iye amawayerekezera ndi mitengo yokongola. (Werengani Salimo 92:​12-14.) N’chifukwa chiyani amawayerekezera ndi mitengo? Mitengo yakalekale nthawi zambiri imakhala yokongola chifukwa imakhala ndi masamba komanso maluwa ambiri. Chitsanzo ndi mitengo ina imene imapezeka ku Japan. Ina mwa mitengoyi yakhala zaka zoposa 1,000 ndipo ndi yokongola kwambiri. Mofanana ndi mitengoyi, Yehova amaona kuti achikulire okhulupirika ndi okongola kwambiri kwa iye. Yehova amachita chidwi ndi makhalidwe abwino amene achikulire ali nawo. Iwo akhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo akhalabe okhulupirika pa nthawi imene zinthu zinali bwino komanso pa nthawi zovuta.

Banja lachikulire lakhala pampando panja, pansi pa mitengo yokongola.

Mofanana ndi mitengo yokongola imene yakhala zaka zambiri ndipo ikupitiriza kukula, Akhristu okhulupirika achikulire ndi okongola ndipo zinthu zimapitiriza kuwayendera bwino (Onani ndime 2)


3. Perekani zitsanzo za achikulire amene Yehova anawagwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake.

3 Yehovaa sasiya kutiona kuti ndife ofunika ngakhale titakalamba. Ndipotu nthawi zambiri amagwiritsa ntchito atumiki ake achikulire pokwaniritsa cholinga chake. Mwachitsanzo, Sara anali wokalamba pamene Yehova anamuuza kuti adzakhala mayi wa mtundu waukulu komanso adzakhala mumzere umene Mesiya adzabadwire. (Gen. 17:​15-19) Mose anali wachikulire pamene Yehova anamutuma kuti akatulutse Aisiraeli ku Iguputo. (Eks. 7:​6, 7) Komanso mtumwi Yohane anali wachikulire pamene Yehova anamuuzira kulemba mabuku 5 a m’Baibulo.

4. Mogwirizana ndi Miyambo 15:​15, n’chiyani chingathandize achikulire kuti azipirira mavuto amene amakumana nawo? (Onaninso chithunzi.)

4 Achikulire amakumana ndi mavuto ambiri obwera chifukwa cha ukalamba. Mlongo wina ananena mwanthabwala kuti, “Ukalamba osamauphweketsa.” Koma kukhala achimwemweb kungathandize achikulire kuti azipirira mavuto omwe amakumana nawo. (Werengani Miyambo 15:15.) Munkhaniyi tikambirana zinthu zimene achikulire angachite kuti apitirize kukhala osangalala. Tionanso zimene anthu ena mumpingo angachite kuti azithandiza achikulire. Koma choyamba, tiona chifukwa chake zimakhala zovuta kuti achikulire apitirizebe kukhala osangalala.

Banja lomwe taliona mu chithunzi choyambirira lija, laimirira pansi pamtengo wamasamba okongola, lagwirana manja ndipo likumwetulira.

Kukhala ndi mtima wosangalala kungathandize achikulire kuti azipirira mavuto amene amakumana nawo chifukwa cha ukalamba (Onani ndime 4)


KUKHALA WACHIKULIRE KUNGAPANGITSE KUTI MUSAMASANGALALE

5. Kodi n’chiyani chingapangitse achikulire ena kuti asamasangalale?

5 N’chiyani chingapangitse kuti musamasangalale? Mwina mumakhumudwa chifukwa mukulephera kuchita zimene munkachita poyamba. Mwina mukulakalaka mukanakhala wachinyamata komanso ndi thanzi labwino. (Mlal. 7:10) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Ruby anati: “Ndimavutika kuvala zovala chifukwa ndimamva ululu komanso ndimavutika kuyenda. Ngakhale zinthu zophweka monga kuvala sokosi zimandivuta. Manja amandipweteka kwambiri ndipo ndimavutika kuti ndigwiritse ntchito zala zanga ngakhale pa ntchito zing’onozing’ono.” M’bale Harold amene anatumikirapo pa Beteli ananena kuti: “Nthawi zina ndimakwiya chifukwa ndimalephera kuchita zinthu zonse zimene ndinkasangalala nazo. Ndinkakonda kuchita masewera enaake ampira. Anthu ena ankakonda kunena kuti, ‘M’patsireni mpira Harold chifukwa saphonya.’ Koma panopa ndikukayikira ngati ndingathe ngakhale kungokankha mpira.”

6. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingachititse achikulire ena kuti azikhumudwa? (b) Kodi n’chiyani chingathandize achikulire kusankha ngati akuyenera kusiya kuyendetsa galimoto kapena ayi? (Onani nkhani ya m’magazini ino yamutu wakuti, “Kodi Ndisiye Kuyendetsa Galimoto?”)

6 Mukhoza kumakhumudwa chifukwa simukukwanitsa kuchita zinthu zina panokha. Zimenezi zimakhala zovuta makamaka ngati mukufunikira munthu woti azikusamalirani kapena kusamuka kuti muzikakhala ndi mmodzi mwa ana anu. Mungakhumudwenso kwambiri chifukwa thanzi lanu silili bwino kapena simuona mokwanira moti nthawi zina simungathe kupita koyenda nokha kapena kuyendetsa galimoto. Zimenezitu n’zowawa kwambiri. Koma tingachite bwino kumakumbukira kuti Yehova komanso anthu ena sikuti amationa kuti ndife amtengo wapatali chifukwa timadzisamalira tokha, timakhala tokha kapena timayendetsa galimoto. Ndipo tisamakayikire kuti Yehova amamvetsa mmene timamvera. Iye amationa kuti ndife amtengo wapatali ngati tili achikondi ndipo timayamikira zimene iyeyo komanso anthu ena amatichitira.—1 Sam. 16:7.

7. N’chiyani chingalimbikitse anthu amene amakhumudwa chifukwa choganiza kuti mwina mapeto safika iwo adakali moyo?

7 N’kutheka kuti mumakhumudwa mukaganizira kuti mwina mapeto safika muli moyo. Ngati mumaona choncho, kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Muzikumbukira kuti Yehova akudikira moleza mtima kuti awononge dziko loipali. (Yes. 30:18) Iye ali ndi cholinga chomwe akulezera mtima. Kuleza mtima kwake kukuthandiza anthu mamiliyoni kuti akhale ndi nthawi komanso mwayi womudziwa n’kuyamba kumutumikira. (2 Pet. 3:9) Choncho mukakhumudwa muziganizira kuchuluka kwa anthu amene akupindula ndi kuleza mtima kwa Yehova mapeto asanafike. Ndipotu ena mwa anthu amenewa akhoza kukhala achibale anu.

8. Kodi mavuto amene achikulire amakumana nawo angawapangitse kuchita zinthu ziti?

8 Kaya ndife achikulire kapena ayi, tikakhala kuti sitikumva bwino tikhoza kulankhula zinthu zimene pamapeto pake tinganong’oneze nazo bondo. (Mlal. 7:7; Yak. 3:2) Mwachitsanzo, pamene Yobu amene anali mtumiki wokhulupirika ankavutika, analankhula “mosaganiza bwino.” (Yobu 6:​1-3) Kuwonjezera pamenepo, matenda angapangitse achikulire kulankhula kapena kuchita zinthu mosiyana ndi mmene amachitira nthawi zonse. Komabe, palibe aliyense wa ife amene mwadala angagwiritse ntchito uchikulire kapena matenda ngati chifukwa chodzikhululukira kuti azilankhula zinthu mosaganiza bwino kapena azivutitsa ena. Ndipo tikazindikira kuti talankhula mosaganiza bwino, tisamazengereze kupepesa.—Mat. 5:​23, 24.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALABE

Chithunzi cha nthambi za mtengo wamasamba okongola; tizithunzi tosonyeza zinthu zomwe abale ndi alongo achikulire angamachite kuti azikhalabe osangalala. Zithunzizi zagwiritsidwanso ntchito mundime 9 mpaka 13.

Kodi mungatani kuti muzisangalalabe ngakhale mukukumana ndi mavuto amene amabwera chifukwa cha uchikulire? (Onani ndime 9 mpaka 13)


9. N’chifukwa chiyani muyenera kulola kuti ena akuthandizeni? (Onaninso zithunzi.)

9 Muzilola kuti ena akuthandizeni. (Agal. 6:2) Poyamba zingamakuvuteni kulola kuti anthu akuthandizeni. Mlongo wina dzina lake Gretl ananena kuti: “Nthawi zina zimandivuta kulola kuti ena andithandize, chifukwa ndimaona ngati ndikuwavutitsa. Zinanditengera nthawi kuti ndisinthe n’kumavomereza modzichepetsa kuti ndikufunika thandizo.” Mukamalola kuti ena akuthandizeni mumawapatsa mwayi wosangalala chifukwa chopatsa. (Mac. 20:35) Ndipotu mungasangalale kuona kuti anthu ena amakukondani ndipo amafuna kukusamalirani.

Mlongo wachikulire wagwira mkono wa mlongo wachitsikana pamene akukagula zinthu limodzi kushopu.

(Onani ndime 9)


10. N’chifukwa chiyani muyenera kukumbukira kusonyeza kuti mukuyamikira zimene ena akuchitirani? (Onaninso zithunzi.)

10 Muziyamikira. (Akol. 3:15; 1 Ates. 5:18) Anthu ena akatichitira zabwino, timayamikira mumtima mwathu koma tikhoza kuiwala kuwathokoza. Komabe ngati titamwetulira n’kunena kuti zikomo kwambiri, timathandiza anzathu kudziona kuti ndi amtengo wapatali komanso tikuwayamikira. Leah amene amasamalira achikulire pa Beteli ananena kuti: “Mmodzi mwa alongo amene ndimawasamalira amandilembera timakadi tondiyamikira. Amalemba mawu ochepa koma amakhala osangalatsa kwambiri. Ndimasangalala kwambiri kulandira timakaditi chifukwa zimandithandiza kudziwa kuti mlongoyo amayamikira zimene ndimamuchitira.”

Mlongo wachikulire akulemba khadi lothokoza.

(Onani ndime 10)


11. Kodi mungathandize bwanji anthu ena? (Onaninso zithunzi.)

11 Muziyesetsa kuthandiza ena. Mukamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zanu pothandiza ena, simuganizira kwambiri za mavuto anu. Mwambi wina wa ku Africa unayerekezera achikulire ndi laibulale imene ili ndi mabuku ambiri okhala ndi malangizo anzeru. Koma mabuku amene angokhala pashelefu sangathandize munthu kupeza nzeru. Mofanana ndi zimenezi, muziyamba ndi inuyo kuuza achinyamata zimene mukudziwa komanso zimene mwakumana nazo. Muziwafunsa mafunso ndipo muzimvetsera. Muziwafotokozera chifukwa chake kutsatira mfundo za Yehova n’kofunika komanso mmene kungawathandizire kuti azisangalala. N’zosakayikitsa kuti mudzakhala osangalala mukamalimbikitsa achinyamata.—Sal. 71:18.

M’bale wachikulire akumvetsera mwachidwi pamene m’bale wachinyamata akumufotokozera zinthu.

(Onani ndime 11)


12. Mogwirizana ndi Yesaya 46:​4, kodi Yehova analonjeza kuti adzawachitira chiyani achikulire? (Onaninso zithunzi.)

12 Muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. Ngakhale kuti mungatope kapena kukhala ndi nkhawa, muzikumbukira kuti Yehova “satopa kapena kufooka.” (Yes. 40:28) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zopanda malire? Njira imodzi ndi kulimbikitsira atumiki ake okhulupirika. (Yes. 40:​29-31) Ndipotu analonjeza kuti aziwathandiza. (Werengani Yesaya 46:4.) Yehova nthawi zonse amakwaniritsa malonjezo ake. (Yos. 23:14; Yes. 55:​10, 11) Mukamapemphera n’kumaona kuti Yehova amakukondani ndipo akukuthandizani, mumakhala osangalala.

M’bale wachikulire akupemphera.

(Onani ndime 12)


13. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 4:​16-18, kodi tizikumbukira chiyani? (Onaninso zithunzi.)

13 Musamaiwale kuti zimene mukukumana nazo n’zakanthawi. Tikamakumbukira kuti vuto limene tili nalo ndi lakanthawi, sitingavutike kupirira. Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti ukalamba komanso mavuto athanzi, zitha posachedwapa. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) Choncho mukhoza kumasangalala mukadziwa kuti zabwino zili m’tsogolo osati m’mbuyo. (Werengani 2 Akorinto 4:​16-18.) Koma kodi ena angatani kuti akuthandizeni?

Mlongo wachikulire akuwerenga Baibulo ali panjinga ya olumala. Kenako akudziyerekezera ali kamtsikana m’Paradaiso ndipo wasiya kugwiritsa ntchito njinga ya olumala.

(Onani ndime 13)


MMENE MUNGATHANDIZIRE ACHIKULIRE

14. N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti tiziyendera kapena kuimbira foni achikulire?

14 Muziyendera komanso kuimbira foni achikulire nthawi ndi nthawi. (Aheb. 13:16) Achikulire akhoza kumaona kuti ali okhaokha. M’bale wina amene sachoka pakhomo dzina lake Camille ananena kuti: “Ndimakhala m’nyumba tsiku lonse choncho ndimaboweka kwambiri. Nthawi zina ndimamva ngati mkango umene autsekera muwaya. Ndimachita mantha komanso ndimakhala ndi nkhawa.” Tikamayendera achikulire zimawathandiza kuzindikira kuti timawaona kuti ndi ofunika komanso timawakonda. N’zosakayikitsa kuti tonse tikukumbukira nthawi ina pamene tinaganiza zoimbira foni kapena kukaona wachikulire mumpingo mwathu koma sitinakwanitse. Tonse timakhala otanganidwa. Ndiye n’chiyani chingatithandize kusankha “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri” kuphatikizapo kukaona achikulire? (Afil. 1:10) Mungachite bwino kulemba pakalendala yanu kuti mudzakumbukire kutumiza uthenga kwa achikulire amumpingo mwanu kapena kuwaimbira foni. Mukhozanso kukonza nthawi yoti muzikawaona, musamadikire kuti mupeze kaye mpata.

15. Kodi ndi zinthu ziti zimene achinyamata ndi achikulire angachitire limodzi?

15 Ngati ndinu wachinyamata, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingacheze nkhani zotani kapena kuchita zinthu ziti ndi achikulire?’ Komatu simukufunika kuda nkhawa. Mungokhala mnzawo wabwino. (Miy. 17:17) Muzicheza ndi achikulire misonkhano isanayambe kapena ikatha. Mungawafunse lemba limene amalikonda kwambiri kapena zomwe zinawachitikira ali mwana. Mungawaitanenso kuti mudzaonere pulogalamu ya JW Broadcasting®. Mungathandizenso achikulire m’njira zina. Mwachitsanzo, mungawathandize kupanga apudeti chipangizo chawo kapena kupanga dawunilodi mabuku atsopano ophunzirira. Mlongo wina dzina lake Carol anati: “Muzipempha achikulire kuti muchitire limodzi zinthu zimene inunso mumasangalala nazo. Ngakhale ndine wachikulire ndimafunabe kuti ndizisangalala. Ndimakonda kupita kokagula zinthu, kokadya komanso kukaona malo.” Mlongo wina dzina lake Maira ananena kuti: “Mmodzi mwa anzanga ali ndi zaka 90. Timasiyana zaka 57 koma nthawi zambiri ndimaiwala zimenezi chifukwa timaseka komanso kuonera mafilimu limodzi. Ndipo tikakumana ndi mavuto timathandizana.”

16. N’chifukwa chiyani zingakhale zothandiza kuperekeza achikulire kuchipatala?

16 Muziwaperekeza kuchipatala. Kuwonjezera pa kuperekeza achikulire kuchipatala, tizionetsetsanso kuti ogwira ntchito kuchipatalako akuwapatsa thandizo ndi kuwasamalira moyenera. (Yes. 1:17) Mungathandizenso achikulire polemba zimene adokotala akunena. Mlongo wachikulire dzina lake Ruth ananena kuti: “Nthawi zambiri ndikapita ndekha kuchipatala, madokotala sakhulupirira zimene ndikuwauza. Nthawi zinanso amanena zinthu monga, ‘vuto lanuli langokhala zimene mukuganiza. Simukudwala.’ Koma ndikapita ndi munthu wina madokotala amandithandiza moyenera. Ndimayamikira abale ndi alongo anga amene amandiperekeza kuchipatala.”

17. Kodi ndi mbali ziti za utumiki zimene tingachitire limodzi ndi achikulire?

17 Muzilalikira nawo limodzi. Achikulire ena sangakhale ndi mphamvu zoti azitha kulalikira kunyumba ndi nyumba. Ndiye kodi mungapemphe mlongo wachikulire kuti mukhale naye pa ulaliki wapashelefu? Mungapezenso mpando woti adzakhalire pafupi ndi pashelefupo. Kapena kodi mungachitire phunziro limodzi ndi m’bale wachikulire kapena kukachitira phunzirolo kunyumba kwake? Akulu angakonze zoti msonkhano wokonzekera utumiki uzichitikira kwa m’bale kapena mlongo wachikulire n’cholinga choti iye azikhala ndi mwayi wopezekapo. Yehova amasangalala tikamathandiza komanso kulemekeza achikulire.—Miy. 3:27; Aroma 12:10.

18. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Taona kuti Yehova amakonda achikulire ndipo amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Abale ndi alongo tonse timachitanso chimodzimodzi. Uchikulire ndi wovuta, koma mothandizidwa ndi Yehova tikhoza kumasangalalabe. (Sal. 37:25) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti zinthu zabwino zikubwera kutsogolo kwanu osati m’mbuyo. Koma bwanji za anthu amene akusamalira achikulire, mwana kapena wachibale amene akudwala? Kodi angatani kuti azisangalalabe? Tidzakambirana yankho la mafunso amenewa munkhani yotsatira.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi zinthu ziti zimene zingapangitse abale ndi alongo achikulire kuti asamasangalale?

  • Kodi achikulire angatani kuti apitirize kukhala osangalala?

  • Kodi tingathandize bwanji achikulire mumpingo?

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

a Onani pa jw.org komanso pa JW Library® vidiyo yakuti, Achikulire—Ndinu Ofunika Kwambiri.

b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Chimwemwe ndi khalidwe limene timakhala nalo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. (Agal. 5:22) Kuti munthu akhaledi wosangalala amafunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena